Eks. 21 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za malamulo osungira akapolo(Deut. 15.12-18)

1“Tsono Aisraele uŵalangize izi:

2Lev. 25.39-46 Mukagula kapolo wachihebri, adzakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Muzidzammasula pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, iye osalipirapo kanthu.

3Akakhala kuti anali yekha, adzachokanso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pobwerapo, mkazi wakeyo adzapita naye limodzi.

4Ngati mbuyake adampatsa mkazi, ndipo adamubalirapo ana aamuna kapena aakazi, mkaziyo pamodzi ndi anawo onse ndi a mbuyakeyo. Tsono mwamuna yekhayo ndiye adzachoke.

5Koma kapoloyo akanena kuti, ‘Ndimakonda mbuyanga, mkazi wanga ndi ana anga, sindifuna kuti ndimasulidwe,’

6pamenepo mbuyakeyo abwere ndi kapoloyo ku Nyumba ya Mulungu. Abwere naye ku chitseko kapena ku mphuthu ya chitseko, ndipo amuboole khutu lake. Motero adzakhala kapolo wa mbuyakeyo moyo wake wonse.

7“Munthu akagulitsa mwana wake wamkazi ku ukapolo, mwanayo sadzaomboledwa monga m'mene amachitira ndi akapolo aamuna.

8Ngati mkaziyo amuipira m'maso mbuye amene ankafuna kumkwatirayo, amlole kuti aomboledwe. Sangathe konse kumgulitsa kwa anthu achilendo chifukwa chakuti sadamchite zokhulupirika.

9Akaganiza zopatsa mwana wake mkaziyo, azidzamsunga ngati mwana wake wamkazi ndithu.

10Akakwatira mkazi wina, ayenera kupitirira kumpatsa woyambayo chakudya ndi zovala. Azimlolanso zonse zomuyenera ngati mkazi wake, monga ankachitira kale.

11Akapanda kumchitira zimenezi, ammasule kuti akhale mfulu, koma osalandirapo ndalama.

Malamulo onena za mphulupulu

12 Lev. 24.17 “Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, nayenso aphedwe ndithu.

13Num. 35.10-34; Deut. 19.1-13; Yos. 20.1-9 Koma ikakhala ngozi, kuti sadaganize konse zomupha mnzakeyo, angathe kuthaŵira ku malo amene ndidzakupatsani.

14Koma munthu akapha mnzake mwadala mwa njira yonyenga, aphedwe ndithu ngakhale wathaŵira ku guwa langa.

15“Munthu aliyense amene amenya bambo wake kapena mai wake, aphedwe.

16 Deut. 24.7 “Munthu aliyense amene aba munthu mnzake ndi kumgulitsa kapena kungomsunga ngati kapolo, aphedwe.

17 Lev. 20.9; Mt. 15.4; Mk. 7.10 “Munthu aliyense wotemberera bambo wake kapena mai wake, aphedwe.

18“Anthu akamenyana, ndipo wina mwa iwowo amenya mnzake ndi mwala kapena nkhonya, koma osamupha mnzakeyo, munthu womenyedwayo akadwala nakagona pa bedi,

19koma pambuyo pake adzuka nkumayendayenda kunja, ngakhale kuti akuyenda ndi ndodo, munthu amene adammenyayo sadzalangidwa molipsira, koma adzangolipira chifukwa cha nthaŵi yotayika pa bedi ija. Ndipo adzayenera kumsamala ndithu mnzakeyo mpaka atachira.

20“Munthu akamenya kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi ndi ndodo, ndipo kapoloyo afera pomwepo, munthuyo adzalangidwa.

21Koma kapoloyo akakhala moyo tsiku lathunthu kapena masiku aŵiri, mbuyakeyo asalangidwe. Kapoloyo ndi chuma cha mbuyakeyo.

22“Anthu aamuna akamayambana, ndipo nkupweteka mai wapathupi, maiyo napititsa padera, koma osafa, amene adampwetekayo adzalipira mtengo uliwonse umene mwamuna wa maiyo angadzatchule. Ndipo adzalipira monga momwe anthu oweruza anganenere.

23Koma maiyo akampweteka, chilango chake chidzakhala chotere: moyo kulipa moyo,

24Lev. 24.19, 20; Deut. 19.21; Mt. 5.38 diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi,

25kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, ndipo mkwingwirima kulipa mkwingwirima.

26“Munthu akamenya kapolo wamwamuna kapena wamkazi pa diso, nkulikoloola disolo, ammasule kapoloyo, kuti akhale mfulu chifukwa cha disolo.

27Akamchotsa dzino, ammasule kapoloyo, kuti akhale mfulu chifukwa cha dzinolo.

Za udindo wa eniake zinthu

28“Ng'ombe ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga, iponyedwe miyala, ndipo nyama yake musadye. Koma mwiniwake wa ng'ombeyo asalangidwe.

29Koma ngati khalidwe lake la ng'ombeyo linali kumangogunda anthu, ndipo mwiniwake adachenjezedwa, koma iye osaimanga, ng'ombeyo ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi, iponyedwe miyala ndithu. Ndipo mwiniwakeyonso aphedwe.

30Koma ngati amlamula kuti adziwombole, adzayenera kulipira ndalama, kuti apulumutse moyo wake.

31Ng'ombe ikapha mnyamata kapena mtsikana, lamulo lake ndi lomwelo ndithu.

32Ng'ombe ikapha kapolo wamwamuna kapena wamkazi, mwini ng'ombeyo alipe mwiniwake wa kapoloyo masekeli asiliva makumi atatu, ndipo ng'ombe iphedwe ndi miyala.

33“Munthu akasiya dzenje lapululu, kapena akakumba dzenje, koma osaphimbira, tsono ng'ombe kapena bulu nkugweramo,

34ayenera kulipira chifukwa cha choŵetacho. Alipire ndalama kwa mwini choŵetacho, koma nyamayo atenge ikhale yake.

35“Ng'ombe ya munthu wina ikapha ng'ombe ya mnzake, anthu aŵiriwo agulitse ng'ombe yamoyoyo, ndipo ndalama zake agaŵane. Nyama yake ya ng'ombe yakufayo agaŵanenso.

36Koma kukadziŵika kuti ng'ombeyo inkangogunda anthu, mwiniwake osaimanga, mwiniwakeyo ayenera kulipira pakupereka ng'ombe yamoyo chifukwa cha yakufayo. Tsono ng'ombe yakufayo ikhale yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help