Num. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kora, Datani ndi Abiramu aukira Mose

1 Mphu. 45.18-20 Yuda 1.11 Kora mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, ndiponso Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Peleti, adzukulu a Rubeni,

2adakopa anthu. Adaukira Mose, iwowo pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele 250, osankhidwa ndi anthu pa msonkhano, anthu otchuka.

3Onsewo adasonkhana pamodzi ndipo adaukira Mose ndi Aroni, naŵauza kuti, “Inu mwankitsa nazo. Mpingo wonse ndi woyera, munthu aliyense mumpingomo ndi wa Chauta, ndipo Chauta ali pakati pathu. Chifukwa chiyani tsono mukudziyesa opambana pa msonkhano wa Chauta?”

4Mose atamva zimenezi, adagwada napemphera,

5kenaka adauza Kora pamodzi ndi gulu lake lonse kuti, “Maŵa m'maŵa, Chauta atiwonetse amene ali wakewake, ndiponso amene ali woyera mtima, ndipo adzamuuza kuti abwere pafupi naye. Munthu amene Mulungu amsankheyo, adzamufikitsa pafupi.

6Tsono iwe Kora, pamodzi ndi gulu lako lonse, muchite izi: mutenge zofukizira lubani,

7muikemo moto, ndipo muthiremo lubani maŵa pamaso pa Chauta. Munthu amene Chauta amsankheyo, ndiye woyera wake. Inu Alevi, ndinu amene mwamkitsa nazo.”

8Mose adauza Kora kuti, “Imvani tsono inu Alevi.

9Kodi simukukhutira nazo zakuti Mulungu wa Israele adakupatulani mu mpingo wa Israele, kuti mubwere pafupi ndi Mulungu kudzatumikira m'Chihema chake, ndipo kuti muime pamaso pa msonkhano ndi kuŵatumikira anthuwo?

10Ndiponso kodi Mulungu adakulolani kuti mubwere pafupi ndi Iye, inu pamodzi ndi abale anu Alevi, amene ali nanu? Kodi mukukhumbiranso ndi unsembe womwe?

11Tsono kutereku nkukangana ndi Chauta, pamene iwe ndi gulu lako mwasonkhana chotere. Kodi Aroni ndiye yani kuti muzimuukira?”

12Apo Mose adatuma munthu kukaitana Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu. Ndipo iwo adati, “Ife sitibwera kumeneko.

13Kodi zikukucheperani kuti mudatitulutsa ku dziko lamwanaalirenji ku Ejipito, kuti tifere m'chipululu muno? Kodi mukufunanso kuti mukhale mfumu yathu yotilamula?

14Kuwonjezera apo, simudatiloŵetse m'dziko lamwanaalirenji, ndipo simudatipatse polima kapena minda yamphesa, kuti ikhale choloŵa chathu. Kodi mukufuna kutigwira m'maso? Ife sitibwera kumeneko.”

15Apo Mose adapsa mtima kwambiri, ndipo adauza Chauta kuti, “Musalandire nsembe za anthu ameneŵa. Sindidaŵalande ndi bulu mmodzi yemwe, ndipo sindidalakwire ndi mmodzi yemwe mwa iwo.”

16Tsono Mose adauza Kora kuti. “Maŵa iwe pamodzi ndi anthu a gulu lako 250, mubwere ku hema lamsonkhano, iweyo ndi anthu akowo ndi Aroni.

17Aliyense mwa inu atenge chofukizira lubani, athiremo lubani. Nonsenu mubwere ku chihemacho, aliyense ndi chofukizira chake. Zofukizirazo zikhale 250, ndipo iweyo ndi Aroni mutenge aliyense chakechake.”

18Choncho munthu aliyense adatenga chofukizira lubani, naikamo moto, ndi kuthiramo lubani, ndipo adakaimirira pa chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi Mose ndi Aroni.

19Kora adasonkhanitsa mpingo wonse pa chipata cha chihema chamsonkhano moyang'anana ndi Mose ndi Aroni. Ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera mpingo wonsewo.

20Ndipo Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,

21“Chokani pakati pa mpingowu kuti ndiwononge onse nthaŵi imodzi.”

22Apo iwo adadziponya pansi, nati, “Inu Mulungu, Chauta mwini moyo wa anthu onse, kodi mukwiyira mpingo wonse chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi?”

23Chauta adauza Mose kuti,

24“Uza mpingo kuti achoke pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu.”

25Tsono Mose adapita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akuluakulu a Aisraele adamtsatira.

26Mose adauza mpingowo kuti, “Ndapota nanu, chokani pakati pa mahema a anthu oipaŵa, ndipo musakhudze chinthu chao chilichonse, kuti angakuphereni kumodzi chifukwa cha zoipa zao.”

27Choncho anthuwo adachokapo pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu. Pamenepo Datani ndi Abiramu adatuluka naima pakhomo pa mahema ao pamodzi ndi akazi ao, ana ao ndi makanda ao.

28Tsono Mose adati, “Pano muzindikira kuti ntchito zonse ndikuchitazi, adandituma ndi Chauta, si za m'mutu mwanga ai.

29Anthu aŵa akafa monga m'mene amafera anthu onse, Mulungu osaŵalanga, ndiye kuti Chauta sadanditume ai.

30Koma Chauta akachita chinthu china chachilendo, nthaka ikayasama ndi kuŵameza iwowo pamodzi ndi zinthu zao zonse, natsikira kumanda ali moyo, mpamene mudziŵe kuti anthu ameneŵa anyoza Chauta.”

31Mose atangomaliza kulankhula mau ameneŵa, nthaka idang'ambika pamene padaali iwopo.

32Nthakayo idayasama ndi kuŵameza onsewo pamodzi ndi mabanja ao ndiponso anthu onse a gulu la Kora ndi zinthu zao zonse.

33Motero iwowo adaloŵa m'manda ali moyo, pamodzi ndi zinthu zao zonse. Nthaka idaŵatsekera pansi, motero adazimirira pakati pa msonkhano wonse.

34Pomwepo Aisraele onse amene anali pafupi adathaŵa, atamva anthuwo akulira. Ankati, “Tiyeni tithaŵe kuti nthakayi ingatimeze nafenso.”

35Tsono padayaka moto wochokera kwa Chauta ndipo udapsereza anthu 250 amene ankafukiza lubani aja.

Zofukizira lubani

36Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti,

37“Uza Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti achotse zofukizira lubani zija m'motomo, ndipo motowo aumwazire kutali.

38Zofukizira za anthu amene aphedwa chifukwa cha kuchimwa kwao nzoyera. Zofukizirazo azisule chophimbira pa guwa, poti azipereka pamaso pa Chauta, nchifukwa chake nzoyera. Motero zidzakhala chizindikiro kwa Aisraele onse.”

39Choncho wansembe Eleazara adatenga zofukizira zamkuŵa zija zimene adadzapereka anthu amene adapsa ndi moto aja. Adazisula chophimbira pa guwa,

40kuti zikhale chikumbutso kwa Aisraele, kuti munthu aliyense amene sali wansembe, amene sali mmodzi mwa zidzukulu za Aroni, asayandikire kudzafukiza lubani pamaso pa Chauta, kuti zingamgwere zonga zimene zidagwera Kora ndi gulu lake. Zonse zidachitika monga momwe Chauta adauzira Eleazara kudzera mwa Mose.

Aroni apulumutsa anthu

41Koma m'maŵa mwake mpingo wonse wa Aisraele udaŵiringulira Mose ndi Aroni kuti, “Inu mwapha anthu a Chauta.”

42Pamene mpingo udasonkhana kuti uukire Mose ndi Aroni, anthuwo adatembenuka ndi kuyang'ana ku chihema chamsonkhano. Tsono adangoona mtambo utaphimba chihemacho, ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera.

43Mose ndi Aroni adabwera patsogolo pa chihema chamsonkhano,

44Lun. 18.20-25ndipo Chauta adauza Moseyo kuti,

45“Choka pakati pa gulu la anthuli, kuti ndiŵaononge onse nthaŵi imodzi.” Aŵiriwo adadziponya pansi.

46Mose adauza Aroni kuti, “Tenga chofukizira lubani chako, ndipo uikemo moto wa pa guwa ndi kuthiramo lubani. Upite nacho msanga kumene kuli gulu la anthuko, ndipo uŵachitire mwambo wopepesera machimo ao. Inde, mkwiyo wa Chauta watsika, ndipo mliri wayamba kale.”

47Choncho Aroni adatenga chofukizira, nathamangira pakati penipeni pa msonkhano. Ndipo adangoona mliri utayamba kale pa anthuwo. Tsono adathira lubani, nachita mwambo wopepesera machimo a anthuwo.

48Aroni adakaima pakati pa anthu akufa ndi amoyo aja, ndipo mliriwo udaleka.

49Komabe amene adafa ndi mliriwo anali 14,700, kuwonjeza pa anthu aja amene adafa pa mlandu wa Kora.

50Pambuyo pake Aroni adabwerera kwa Mose ku chipata cha chihema chamsonkhano, mliriwo utaleka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help