1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, panali akazi aŵiri, ana a mimba imodzi.
3Ankachita zadama ku Ejipito. Zadamazo ankachita akali atsikana. Kumeneko anthu ankangoŵasisita pa chifuwa ndi kumaŵagwira maŵere ao osagwa aja.
4Wamkulu anali Ohola, mng'ono wake anali Oholiba. Ndidaŵakwatira ndipo adandibalira ana aamuna ndi ana aakazi. ‘Ohola’ ndiye Samariya. ‘Oholiba’ ndiye Yerusalemu.
5“Ohola ankachita zadama ngakhale pamene anali wanga. Ankakangamira zibwenzi zake za ku Asiriya.
6Amuna amenewo ena anali asilikali ovala zamlangali, ena anali abwanamkubwa, ena atsogoleri a nkhondo, onsewo anyamata osiririka, kudzanso okwera pa akavalo.
7Oholayo ankachita zadama ndi onsewo, amuna otchuka a ku Asiriya. Ndipo anakadziipitsa ndi mafano a amuna onse amene ankachita naye zadama.
8Sadasiye makhalidwe ake a dama amene adaŵaphunzira ku Ejipito, kumene amuna ankagona naye akadali namwali. Ankamugwira maŵere akali anthete, namachita naye chigololo.
9Nchifukwa chake ndidampereka kwa zibwenzi zakezo, ndiye kuti Aasiriya, amene iye adaaŵakangamira.
10Iwowo adamuvula. Adamulanda ana ake aamuna ndi aakazi, ndipo adamupha ndi lupanga. Atalangidwa choncho, adasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi onse.
11“Tsono Oholiba mng'ono wake uja adatengerako, ndipo adachita zadama kupambana mkulu wake.
12Iyenso ankakangamira Aasiriya, makamaka abwanamkubwa, atsogoleri a nkhondo, asilikali ovala zamlangali, okwera pa akavalo, onsewo anyamata osiririka.
13Ndidaona kuti iyenso adadziipitsa, ndipo aŵiriwo adatsata njira imodzi.
14“Koma Oholiba uja adachita chigololo kopitirira mkulu wake. Adaona zithunzi za amuna pa makoma, zithunzi za Ababiloni zolembedwa ndi utoto wofiira.
15Anthuwo adaamanga malamba m'chiwuno, ndi kuvala nduŵira kumutu. Onse ankaoneka ngati atsogoleri ankhondo, ndipo ankaoneka ngati Ababiloni, mbadwa za ku Kaldeya.
16Atangoŵaona, mkazi uja adayamba kuŵalakalaka. Motero adatuma amithenga ku Babiloni kukaŵaitana.
17Choncho amuna a ku Babiloni adabwera kwa iye nagona naye. Mwa chilakolako chao adamuipitsa kaŵirikaŵiri. Koma iwowo atamuipitsa choncho, iye adanyansidwa nawo.
18Mkaziyo ankachita zadama poyera, ndipo ankaonetsa maliseche ake osachita manyazi. Motero ndidanyansidwa naye monga momwe ndidachitira ndi mkulu wake.
19Koma ankachitabe zadama zake osalekeza, namakumbukira zadama zimene ankachita pamene anali hule ku Ejipito pa ubwana wake.
20Ankalakalaka abwenzi ake amene ziwalo zao zinali zazikulu ngati za bulu, amene kutentha kwao kunali ngati kwa akavalo.
21Motero iwe Oholiba udafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Ejipito ukadali namwali, kumene ankakusisita pa chifuwa, nkumakugwira maŵere ako osagwa aja.
Mulungu alanga Yerusalemu ndi Samariya22“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Iwe Oholiba, ndidzakuutsira zibwenzi zako zimene udanyansidwa nazozo kuti zilimbane nawe. Ndidzaziitana kuti zibwere kwa iwe kuchokera ku mbali zonse
23Ndidzaitana anthu a ku Babiloni, onse a ku Kaldeya, onse amene ali ku Pekodi, a ku Sowa, a ku Kowa, pamodzi ndi Aasiriya onse. Onsewo ndi amuna osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri a nkhondo, asilikali, onsewo ndi okwera pa akavalo.
24Adzabwera kuchokera kumpoto kudzakuthira nkhondo ndi akavalo ankhondo, magaleta ndi ngolo zambiri, ndiponso gulu lalikulu la ankhondo ochokera ku maiko onse. Adzakuzinga mbali zonse atavala malihawo, zishango ndi zisoti zankhondo. Ndidzakupereka m'manja mwao kuti akulange. Ndipo adzakulangadi monga momwe adzafunire iwowo.
25Ndidzaŵalola kuti akuchite zankhanza chifukwa choti ndakukwiyira. Adzakudula mphuno ndi makutu, ndipo otsalira mwa iwe adzaŵapha ndi lupanga. Adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzapsa ndi moto.
26Adzakuvula zovala, ndipo adzakukolopola zodzikongoletsera zako za mtengo wapatali.
27Motero ndidzaletsa zonyansa zako ndi zigololo zako zimene wakhala ukuchita kuyambira nthaŵi imene unali ku Ejipito. Choncho sudzalakalakanso za ku Ejipito kapena kuzikumbukira.
28“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikukupereka m'manja mwa adani ako, amene udaŵafulatira chifukwa choipidwa nawo.
29Ndipo adzakuchita zachidani. Adzakulanda zonse zimene udapeza ndi dama lako, ndipo adzakusiya wamaliseche ndi wausiŵa. Thupi limene unkachitira zadama lidzakhala lamaliseche. Zonyansa zako ndi chigololo chako,
30ndizo zakubweretsera zimenezi, chifukwa choti wachita zonyansa ndi mitundu ya anthu achilendo, ndi kudziipitsa ndi mafano ao.
31Udatsanzira zochita za mkulu wako, ndipo ndidzaika chikho cha chilango chake m'manja mwako.”
32“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi:
Udzamwera chikho cha mkulu wako,
chikho choloŵa ndiponso chachikulu.
Anthu adzakuseka ndi kukunyoza,
chifukwa chikhocho nchodzaza kwambiri.
33Udzaledzera,
ndipo mumtima mwako mudzadzaza ndi chisoni.
Chimenechi ndi chikho choopsa ndi chachipasupasu,
chikho chachilango cha mbale wako Samariya.
34Udzachimwa chikhocho mpaka kuchigugudiza.
Tsono udzachitafuna,
ndipo udzang'amba maŵere ako ndi zigoba zake.
Ineyo ndanena zimenezi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
35“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Chifukwa chakuti wandiiŵala Ine ndi kundifulatira, uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi zigololo zako.”
Mulungu alanga abale aŵiriwo36Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukufuna kudzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uŵaimbe mlandu chifukwa cha zonyansa zao zimene adachita.
37Adachita chigololo, ndipo adapha anthu. Adachita chigololo popembedza mafano ao, ndipo ana anga amene adandibalira, adaŵapereka kwa mafanowo ngati chakudya chao.
38Adachitanso izi: adaipitsa malo anga ondipembedzera, ndipo adanyoza masiku anga a Sabata.
39Adangoti atapereka ana ao nsembe kwa mafano ao, nthaŵi yomweyo nkuloŵa m'Nyumba yanga yoyera naiipitsa. Ndithu zimenezi nzimene adachita m'Nyumba mwanga.
40“Komanso adatuma amithenga kukaitana amuna akutali. Anthuwo atabwera, abale aŵiri aja adasambasamba, nkukometsa m'masomu ndi utoto, navala zamakaka.
41Adakhala pa bedi lokongola, ndipo patsogolo pao panali tebulo. Patebulopo adaikapo lubani ndi mafuta, zonse zoŵapatsa Ine.
42Mfuu wa chigulu cha anthu udamveka. Kuwonjezera pa anthu wamba, panalinso ena oledzera ochokera ku chipululu. Adaveka akaziwo makoza kumanja ndiponso zisoti zaufumu zokongola ku mutu.
43“Tsono Ine ndidati, ‘Mkazi ameneyu ndi wotheratu ndi chigololo. Koma onani, anthu akutsatabe zadama zake zomwezo.
44Choncho adapita kwa iye monga m'mene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Ndimo adapitira kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama.
45Koma tsiku lina anthu abwino adzaŵazenga anthuwo mlandu wa chigololo ndi wa kupha anzao. Zoonadi ngachigololo, ndipo m'manja mwao magazi ali psu.’
46“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Itanani chigulu cha anthu, kuti chiŵazunze ndi kulanda chuma chao.
47Akazi aŵiriwo aŵaponye miyala ndi kuŵatema ndi malupanga ao. Aphenso ana ao aamuna ndi aakazi ndipo atenthe nyumba zao.
48Motero ndidzathetsa chiwerewere m'dziko lao, ndipo akazi onse adzaphunzira kuti asadzachite zonyansa ngati iwowo.
49Adzalangidwa chifukwa cha makhalidwe ao achiwerewere, ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo la kupembedza mafano. Tsono adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.