Zek. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta alonjeza kubwezeranso Yerusalemu mwakale

1Chauta Wamphamvuzonse adandipatsanso uthenga uwu wakuti,

2“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Mtima wanga wonse uli pa Ziyoni, anthu ake ndimaŵakonda mwansanje kwambiri.

3Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Tsopano ndidzabweranso ku phiri la Ziyoni, ndidzakhalanso ku Yerusalemu. Yerusalemuyo adzatchedwa Mzinda Wokhulupirika. Phiri la Ine Chauta Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Loyera.

4“Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, amuna ndi akazi okalamba, oyenda ndi ndodo chifukwa cha ukalamba, adzayendanso m'miseu ya Yerusalemu.

5Ndipo m'miseu ya mumzindamo mudzadzaza ndi ana, anyamata ndi atsikana, amene azidzaseŵeramo.

6“Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Ngakhale ziwoneke ngati zosatheka kwa anthu a m'fuko limeneli amene adzatsale nthaŵi imeneyo, kodi zimenezi zidzakhalanso zosatheka ndi kwa Ine ndemwe?

7“Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, Ndidzapulumutsa anthu anga amene ali ku maiko akuvuma ndi akuzambwe.

8Ndidzaŵabweza kuti akhalenso ku Yerusalemu. Pamenepo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, wokhulupirika ndi wolungama.

9“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Inu masiku ano mukumva mau a aneneri amene ankalankhula pa nthaŵi yoyala maziko a Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse. Choncho limbani mtima, kuti Nyumbayi imangidwenso.

10Mpaka nthaŵi imeneyo panalibe wina wolandirapo malipiro pa ntchito kapena wopindulapo pa zoŵeta. Panalibe munthu amene ankadziyendera mwamtendere, chifukwa cha adani, popeza kuti anthu onse ndidaaŵayambanitsa.

11Koma tsopano anthu atsalaŵa sindidzaŵachitanso zomwe ndidaaŵachita anthu kale. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.

12“Adzabzala mwamtendere, mpesa udzabala zipatso zake, ndipo nthaka idzabereka kwambiri. Mvula idzagwa kuchokera kumwamba. Madalitso onseŵa ndidzaŵapatsa otsala mwa anthuŵa.

13Inu mabanja a Yuda ndi Israele, kale munali chizindikiro cha matemberero pakati pa mitundu ina ya anthu. Koma tsopano ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala chizindikiro cha madalitso. Musaope, limbani mtima.

14“Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Paja ndidaatsimikiza mtima kuti ndikuwonongeni, chifukwa chakuti makolo anu adaandikwiyitsa, ndipo sindidafune kukhululuka. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.

15Koma masiku ano ndatsimikiza kuti ndimchitira zabwino Yerusalemu ndi banja la Yuda. Choncho musaope.

16Aef. 4.25 Muzichita izi: muzikambirana zoona, muziweruza moona ndi mwamtendere m'mabwalo a milandu.

17Musamachitirane chiwembu, musamakonde kulumbira zonama, pakuti zonsezi ndimadana nazo.” Ndikutero Ine Chauta.

18Chauta Wamphamvuzonse adandipatsa uthenga uwu wakuti, “Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa:

19Kusala zakudya pa mwezi wachinai, wachisanu, wachisanu ndi chiŵiri ndi wakhumi, kudzakhala nthaŵi yachimwemwe ndi yachisangalalo ku banja la Yuda. Muzikonda zoona ndiponso mtendere.”

20“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Anthu a mitundu yambiri ndi anthu okhala m'mizinda yambiri adzabweradi.

21Anthu a mzinda wina adzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe chifundo kwa Chauta, tikapembedze Chauta Wamphamvuzonse. Ifeyo tikupita komweko.’

22Anthu ambiri ndiponso a ku maiko amphamvu adzandipembedzadi Ine Chauta Wamphamvuzonse ku Yerusalemu ndi kupempha chifundo changa.

23“Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, pa masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a zilankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nao, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help