Mas. 68 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo ya fuko yokondwerera kugonjetsaKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide. Nyimbo.

1Mulungu adzambatuke, adani ake amwazikane.

Onse amene amamuda, athaŵe pamaso pake.

2Amwazeni iwowo monga m'mene mphepo imachitira utsi.

Anthu oipa aonongeke pamaso pa Mulungu,

monga m'mene sera amasungunukira pa moto.

3Koma anthu anu Mulungu, akondwere,

asangalale pamaso panu,

inde, asekere ndi chimwemwe.

4Muimbireni Mulungu,

imbani nyimbo zotamanda dzina lake.

Kwezani nyimbo yotamanda Iye amene amayenda pa mitambo.

Dzina lake ndi Chauta, musangalale pamaso pake.

5Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye,

ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.

6Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo,

am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu,

koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga.

7Inu Mulungu, pamene munkatsogolera anthu anu,

pamene munkayenda m'chipululu muja,

8 Eks. 19.18 dziko lidagwedezeka,

mlengalenga udagwetsa mvula

chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu.

Phiri la Sinai lidagwedezeka

chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu,

Mulungu wa Israele.

9Inu Mulungu, mudagwetsa mvula yokwanira pa dziko.

Mudalimbitsanso dziko, choloŵa cha anthu anu,

pamene lidaali lofooka.

10Anthu anu adapezamo malo okhala.

Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao

mwa ubwino wanu.

11Ambuye apereka lamulo.

Nchachikulu chiŵerengero

cha amene abwera ndi uthenga wakuti,

12“Mafumu a magulu a ankhondo akuthaŵa,

indedi akuthaŵa.

Tsono azimai ku mudzi akugaŵana zofunkha,

ngakhale atsalira pakati pa makola ankhosa.

13“Zofunkhazo zikuwoneka ngati mapiko a nkhunda

okutidwa ndi siliva,

nthenga zake nzokutidwa ndi golide wonyezemira.”

14Pamene Mphambe adabalalitsa mafumu kumeneko,

ku Zalimoni kudagwa chisanu choopsa.

15Iwe phiri la Basani, phiri laulemerero,

Iwe phiri la Basani, phiri la nsonga zambiri!

16Iwe phiri la nsonga zambiriwe,

chifukwa chiyani ukuliyang'ana mwansanje

phiri limene Mulungu adasankha kuti azikhalapo?

Ndithu Chauta adzakhalapo mpaka muyaya.

17Ambuye adafika ku malo ao oyera

kuchokera ku Sinai,

ali ndi magaleta amphamvu zikwi zambirimbiri.

18 Aef. 4.8 Inu mudakwera kumwamba,

mutatenga am'ndende ambiri,

ndipo mudalandira mphatso kwa anthu,

ngakhale kwa anthu oukira,

kuti mudzakhale kumeneko, Inu Chauta Mulungu.

19Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu,

amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.

20Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa,

ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa.

21Koma Mulungu adzatswanya mitu ya adani ake,

mitu ya anthu onse oyenda m'machimo ao.

22Ambuye adati,

“Ndidzaŵabweza adani anu kuchokera ku Basani,

ndidzaŵabweza kuchokera ku nyanja yozama,

23kuti musambe mapazi anu m'magazi,

kuti agalu anu anyambiteko magazi a adaniwo.”

24Inu Mulungu,

mdipiti wa anthu anu oyenda mwaulemu ukuwoneka,

mdipiti wolemekeza Mulungu wanga, Mfumu yanga,

wokaloŵa m'malo opatulika.

25Oimba nyimbo zapakamwa atatsogola,

oimba ndi zipangizo ali pambuyo,

anamwali oimba ting'oma ali pakati.

26“Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu.

Tamandani Chauta, inu zidzukulu za Israele.”

27Patsogolo pao pali Benjamini mng'ono wa onsewo,

akalonga a Yuda ali pambuyo,

ndiponso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafutali.

28Kungani mphamvu zanu, Inu Mulungu,

onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu,

amene mumatichitira zamphamvu.

29Chifukwa cha Nyumba yanu ya ku Yerusalemu,

mafumu amabwera ndi mphatso kwa Inu.

30Dzudzulani zilombo zija zokhala m'mabango,

ndiponso gulu la nkhunzi lija ndi malikonyani,

ndiye kuti akalonga ndi anthu ao.

Ponderezani amene amalakalaka ndalama moipa.

Abalalitseni anthu okonda nkhondo.

31Akazembe adzabwera kuchokera ku Ejipito.

A ku Etiopiya adzafulumira kugonjera Mulungu

pokweza manja ao kwa Iye.

32Imbirani Mulungu nyimbo,

inu maufumu a pa dziko lapansi.

Imbani nyimbo zotamanda Ambuye,

33Chauta amene amayenda mu mlengalenga,

mlengalenga wakalekale.

Imvani liwu lake,

liwu lake lamphamvu zedi.

34Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu,

ulamuliro wake uli pa Israele,

mphamvu zake zili mu mlengalenga.

35Mulungu ndi woopsa m'malo ake opatulika,

Mulungu wa Israele ndiye amapatsa mphamvu

ndi kuŵalimbikitsa anthu ake.

Mulungu atamandike.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help