Neh. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nehemiya ateteza anthu osauka

1Tsono anthu ena pamodzi ndi akazi ao adayamba kudandaula kwambiri chifukwa cha Ayuda anzao.

2Pakuti panali ena amene ankati, “Ife ndi ana athu tikuchuluka kwambiri, motero tikusoŵa tirigu wakudya, kuti tikhale ndi moyo.”

3Panalinso ena amene ankati, “Ife tikuchita kupereka minda yathu, mitengo yathu yamphesa, pamodzi ndi nyumba zathu, ngati chikole, kuti tipeze tirigu, poti njala yatipha.”

4Panali enanso amene ankati, “Ife tachita kukongola ndalama kuti tikhome msonkho wa minda yathu kwa mfumu, ndiponso kuti tikhomere mitengo yathu yamphesa.

5Tsonotu ife ndi anzathu aja ndife amodzi, ndipo ana athu ngofanafana ndi ana ao. Komabe ifeyo tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo, mwakuti ana athu ena aakazi agwidwa kale. Ifeyo tilibe mphamvu zoti nkuchitapo kanthu, poti anthu aja atenga kale minda yathu ndi mitengo yathu yamphesa.”

6Ine nditamva madandaulo amenewo, ndidapsa mtima kwambiri.

7Eks. 22.25; Lev. 25.35-37; Deut. 23.19, 20 Ndidatsimikiza kuti ndichitepo kanthu, ndipo ndidaŵadzudzula atsogoleri ndi akulu olamula omwe. Ndidati, “Kodi nzokuwonerani kuti mukulipitsana chiwongoladzanja anthu apachibale nokhanokha!” Pamenepo ndidachititsa msonkhano waukulu kuti ndiŵazenge mlandu.

8Tsiku limenelo ndidaŵauza kuti, “Monga m'mene kwathekera, tayesetsa kuwombola abale athu, Ayuda amene adaagulitsidwa ngati akapolo kwa anthu a mitundu ina. Koma tsopano inu mukugulitsa ngakhale abale anu omwe kwa anzao, kuti ife tiwumirizidwe kuŵaombola.” Anthuwo adangokhala chete osaona ponena.

9Tsono ine ndidaonjeza kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwinotu ai. Muziwopa Mulungu ndi kumachita zolungama, kuti adani athu a mitundu inaŵa asapeze chifukwa chotinyozera.

10Chinanso nchakuti ine, pamodzi ndi abale anga ndiponso antchito anga, tidaŵakongoza ndalama ndi tirigu. Tiyeni tisaŵaumirize kubwezera ngongolezo.

11Muŵabwezere lero lomwe lino minda yao, mitengo yao yamphesa, mitengo yao ya olivi, ndi nyumba zao, ndipo muŵakhululukire ngongole za ndalama, za tirigu, za vinyo, ndi za mafuta, zimene mudaaŵakongoza.”

12Ndiye iwowo adayankha kuti, “Tidzachitadi monga mukuneneramu. Tidzabwezera zimenezi osapemphapo kanthu.” Pamenepo ndidaitana ansembe, ndipo pamaso pao ndidaŵalumbiritsa akuluwo kuti adzachitedi monga momwe adalonjezera.

13Tsono ndidakutumula chovala changa ndipo ndidanena kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu aliyense wosasunga malonjezo akeŵa. Amsandutse mmphaŵi pakumlanda nyumba yake, antchito ake ndi zonse zimene ali nazo.” Apo msonkhano wonse udavomereza ponena kuti, “Zikhale momwemo ndithu!” Ndipo onsewo adatamanda Chauta. Pambuyo pake akulu aja adachita monga m'mene adaalonjezera.

Kukoma mtima kwa Nehemiya

14Kuyambiranso nthaŵi imene adandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa m'dziko la Yuda, kuchokera chaka cha 20 mpaka chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, ndiye kuti zaka khumi ndi ziŵiri, ineyo ndi abale anga sitidalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa.

15Abwanamkubwa amene analipo kale ankasautsa anthu pomaŵalanda chakudya ndi vinyo, ndi kuŵalipitsanso masekeli asiliva makumi anai. Ngakhale antchito ao nawonso ankathinitsa anthu. Koma ine sindidachite nawo zimenezo, popeza kuti ndinkaopa Mulungu.

16Ndiponso ndinkakangamira pa ntchito yomanga makoma a mzinda, osafuna kupata minda. Antchito anga onsenso anali komweko, ndidaaŵalamula kuti adzipereke pa ntchito yokhayokhayo.

17Komanso masiku onse ndinkadyetsa anthu 150, Ayuda ndi akulu olamula, kuphatikizapo anthu amene adaabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ina yotizungulira.

18Tsono chakudya cha pa tsiku limodzi chinali ichi: ng'ombe imodzi, nkhosa zisanu ndi imodzi zonenepa, ndiponso nkhuku zochuluka. Pa masiku khumi aliwonse panalinso matumba achikopa ochuluka a vinyo. Komabe ngakhale choncho, ine sindidafune kulandira chakudya chimene abwanamkubwa ankalandira, chifukwa chakuti anthu anga anali othinidwa kwambiri.

19Kuti tipeze bwino, kumbukirani, Inu Mulungu wanga, zonse zimene ndidaŵachitira anthuzi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help