1Mundisunge Inu Mulungu,
pakuti ndikuthaŵira kwa Inu.
2Ndimamuuza Chauta kuti,
“Inu ndinu Ambuye anga.
Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.”
3Kunena za oyera mtima amene ali pansi pano,
ameneŵa ndi olemekezeka,
ndipo ndimakondwera nawo.
4Amene amasankhula milungu ina,
amadzichulukitsira mavuto.
Sindidzatsira nawo nsembe zao zamagazi
kapena kutchula maina a milungu yaoyo.
5Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa.
Tsogolo langa lili m'manja mwanu.
6Malire a malo anga andikhalira mwabwino.
Inde, ndalandira madalitso abwino ndithu.
7Ndikutamanda Chauta amene ali phungu wanga.
Mtima wanga umandilangiza ndi usiku womwe.
8Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta.
Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja,
palibe amene angandiopse konse.
9Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa,
ndipo m'katikati mwangamu ndikusangalala.
Thupi langanso lidzakhala pabwino,
10 Ntc. 13.35 chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa,
simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko.
11 Ntc. 2.25-28 Mumandiwonetsa njira ya ku moyo.
Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu,
ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.