1 Lun. 2.1; Mphu. 40.1-11; 41.1-4 “Munthu wobadwa mwa mkazi amakhala masiku oŵerengeka,
komanso masiku ake ndi amavuto okhaokha.
2Amaphuka ngati duŵa, kenaka nkufota.
Sakhalitsa, amathaŵa ngati mthunzi.
3Kodi Inu Mulungu, mungamtuzulire maso woteroyo?
Kodi mungamzenge mlandu?
4Ndani angatulutse chabwino m'choipa?
Palibe ndi mmodzi yemwe.
5Masiku a munthu ndi oŵerengeka,
chiŵerengero cha miyezi yake mumachidziŵa ndinu.
Inu mudamulembera malire ake, sangathe kuŵalumpha.
6Mumleke tsono kuti apumule, akondweko,
akondwerere moyo wake monga amachitira waganyu poweruka.
7“Mtengo chiyembekezo chake
nchakuti akaudula udzaphukanso,
nthambi zake sizidzaleka kuphuka.
8Ngakhale mizu yake ikalambe m'nthaka,
ndipo chitsa chake chiwole,
9komabe chinyontho chikafika, udzaphukira,
udzaphukadi nthambi ngati mtengo wanthete.
10Koma munthu akafa, kutha kwake nkomweko.
Kodi munthuyo akafa, amapita kuti?
11Monga madzi amaphwa m'nyanja,
monganso mtsinje umaphwa nuuma,
12momwemonso munthu amagona pansi osadzukanso.
Mpaka zamumlengalenga zidzatha, iyeyo sadzadzuka.
Palibe aliyense angamdzutse kutulo kwake.
13Ha! Achikhala mudaangondibisa ku manda,
kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita.
Achikhala mudaangondiikira nthaŵi,
kuti pambuyo pake mundikumbukirenso.
14Kodi munthu atafa, nkudzakhalanso ndi moyo?
Koma masiku onse a moyo wanga wovutikawu,
ndidzadikira mpaka kumasulidwa kwanga kutafika.
15Inu mudzandiitana, ine nkukuyankhani.
Mudzafunitsitsanso kuwona ine, ntchito ya manja anune.
16Nthaŵiyo mudzayang'ana mayendedwe anga onse,
koma simudzalondoloza machimo anga.
17Zolakwa zanga zidzakhululukidwa,
Inu mudzafafaniza machimo anga onse.
18“Komabe monga phiri limagwa nkuswekasweka,
ndipo thanthwe limasendezeka kuchoka pamalo pake,
19monganso madzi oyenda amaperesa miyala,
ndipo madzi othamanga amakokolola nthaka,
momwemonso Inu mumaononga chiyembekezo cha munthu.
20Mumamtswanya munthu kamodzinkamodzi,
iye nkufafanizika kotheratu.
Mumasintha maonekedwe a nkhope yake, nkumtaya kutali.
21Ana ake akamalemekezedwa, iye sadziŵako,
akamachititsidwa manyazi, iye saziwona.
22Amangomva zoŵaŵa za m'thupi mwake zokha,
amangodzilira yekha mwiniwakeyo.”
Kukambirana kwachiŵiri(15.1—21.34)Elifazi
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.