Mal. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku likubwera pamene anthu onse odzikuza ndi ochita zoipa adzapsa ngati chiputu m'ng'anjo. Tsiku limenelo adzapserereratu osatsalako muzu kapena nthambi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.

2Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuŵa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuŵala kokuchiritsani. Mudzalumphalumpha mokondwa ngati ana a ng'ombe ochokera m'khola.

3Tsiku limene ndilikukonzalo mudzapondereza anthu oipa ngati phulusa ku mapazi anu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.

4“Kumbukirani zophunzitsa za Mose mtumiki wanga, malamulo ndi malangizo amene ndidamulamula ku phiri la Horebu kuti auze Aisraele onse.

5 Mt. 11.14; 17.10-13; Mk. 9.11-13; Lk. 1.17; Yoh. 1.21 “Koma lisanafike tsiku lalikulu loopsalo la Chauta, ndidzakutumizirani mneneri Eliya.

6Iyeyo adzayanjanitsa atate ndi ana ao, ana ndi atate ao, kuwopa kuti ndingadzabwere kudzatemberera dziko lanu kuti liwonongeke.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help