1“Inu Ambuye amphamvuzonse, Mulungu wa Israele, mtima wathu woda nkhaŵa ndi wolefuka ukulira kwa Inu.
2Imvani Ambuye, ndipo chitani chifundo, chifukwa tidakuchimwirani.
3Inu ndinu Mfumu mpaka muyaya, koma ife timafa nkuchokeratu chonse.
4Ambuye amphamvuzonse, Mulungu wa Israele, imvani pemphero la anthu akufafe a fuko la Israele ndi la ana ao a anthu aja amene adakuchimwirani. Zoonadi sitidamvere mau a Ambuye Mulungu wathu, ndipo masoka akanirira pa ife.
5Musakumbukirenso zoipa za makolo athu, koma mukumbukire mphamvu zanu ndi dzina lanu.
6Pajatu Inu ndinudi Ambuye Mulungu wathu, ndipo ife tidzakutamandani Ambuye.
7M'mitima mwathu Inu mudaikamo mantha oopa Inu, kuti tizilemekeza dzina lanu. Tsono tidzakutamandani m'dziko lino la ukapolo wathu, chifukwa takaniratu m'mitima mwathu zoipa zonga zija zimene makolo athu adakuchitirani.
8Tsopano tikupezeka ku dziko lino laukapolo kumene mudatibalalitsa, kumene amatinyoza ndi kutitemberera. Zimenezo zatigwera chifukwa cha machimo a makolo athu amene adasiyana nanu, Inu Ambuye Mulungu wathu.”
Ubwino wa Nzeru9 Miy. 4.20-22 Iwe Israele, imva malamulo opatsa moyo.
Tchera khutu kuti udziŵe nzeru.
10Zakhala bwanji, iwe Israele,
zakhala bwanji kuti ukupezeka m'dziko la adani,
ndipo kuti wayamba kukalamba m'dziko lachilendo?
Zakhala bwanji kuti uli woipitsidwa
pakati pa anthu akufa?
11Chifukwa chiyani wasanduka mnzao wa anthu akumanda?
12Iwetu udasiya kasupe wa nzeru.
13Ukadatsata njira ya Mulungu,
bwenzi uli mu mtendere nthaŵi zonse.
14Phunzira kumene kuli luntha,
kumene kuli mphamvu,
kumene kuli nzeru zomvetsa zinthu.
Pamenepo udzazindikira
kumene kuli moyo weniweni wa zaka zambiri,
kumene kuli kuyera kokuunikira,
ndiponso kumene kuli mtendere.
15 Yob. 28.12, 20 Ndani adapeza malo ake
kumene kumakhala nzeru?
Ndani adaloŵa m'nyumba
yosungiramo chuma chake?
16Nanga ali kuti akalonga
a mitundu ya anthu,
ali kuti anthu olamulira
ndi zilombo za pansi pano zomwe?
17Ali kuti anthu osaka mbalame zamumlengalenga?
Ali kuti anthu odziwunjikira siliva ndi golide
zimene anthu ena amazidalira,
koma osakhutitsidwa?
18Ali kuti amisiri oyesayesa
kupata siliva mtima uli phaphapha,
amene ntchito yaoyo ndi yakalavulagaga?
19Onsewo adazimirira,
adatsikira ku manda,
ndipo ena adaloŵa m'malo mwao.
20Achinyamata aona kuŵala kwa dzuŵa
ndipo akhazikika pansi pano.
Koma nawonso sadadziŵe njira ya nzeru,
sadamvetse njira zake,
nzeruzo sadazipeze.
21Ana ao ndiye adachita kuzilambalala kutali nzeruzo.
22Nzeru zimenezi ku Kanani sizidamveke konse,
ndipo ku Temani sizidaonekeko.
23Ana a Hagara ofunafuna nzeru m'dziko lapansi,
amalonda a ku Merani ndi a ku Temani,
anthu ofalitsa nkhani ndi anthu ofuna kudziŵa zinthu,
onsewo sadatulukire kapezedwe kake ka nzeru,
sadaganizeko za njira zake.
24Iwe Israele, taonatu kukula kwake
nyumba ya Mulunguyi!
Taonatu kukula kwake dziko lakeli!
25Ndi lalikuludi ndi lopanda malire,
ndi lalitali ndi losatheka kuliyesa.
26 Gen. 6.4; Lun. 14.6 Kumeneko nkumene kudabadwira ziphona,
zija zinkatchuka kalezi,
za misinkhu italiitali
ndiponso zaukatswiri pa nkhondo.
27Tsonotu Mulungu sadasankhule ziphonazo,
sadaziphunzitse njira ya nzeru.
28Motero zidaonongeka
chifukwa zinalibe nzeru,
zidatha chifukwa cha kupusa kwao.
29Ndani adapitako kumwamba,
nakazigwira nzeruzo
nkuzikokera pansi pano kuchokera ku mitambo?
30Ndani adaoloka nyanja nakazipeza,
nkubwera nazo atazigula ndi golide weniweni?
31Iyai, palibe munthu wodziŵa njira yozipezera,
kapena njira yokafikira ku nzeruzo.
Wodziŵa nzeru ndi wopatsa nzeru ndi Mulungu yekha32Koma Iye amene amadziŵa zonse,
amadziŵadi nzeru.
Adazipeza chifukwa cha kumvetsa bwino zinthu.
Ndiye amene adakonza dziko lapansi
kuti likhalepo mpaka muyaya,
nalidzaza ndi nyama zamitundumitundu.
33Amatuma kuŵala, ndipo kumapitadi.
Amakuitana kuŵalako,
ndipo kumamvera mau ake monjenjemera.
34Nyenyezi zimaŵala pamalo pamene adaziikapo,
ndipo zimasangalala.
35Iye akaziitana,
izo zimayankha kuti,
“Tili pano!”
Ndipo zimaŵala mosangalala,
kuŵalira amene adazilenga.
36Ameneyu ndiye Mulungu wathu,
palibe wina wofanafana naye.
37Iye adatulukira njira zonse zofikira ku nzeru,
nzeruzo adazipatsa Yakobe mtumiki wake,
adazipatsa Israele wokondedwa wake.
38Pambuyo pake nzeruzo zidadzaoneka pansi pano,
nkudzakhazikika pakati pa anthu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.