Mas. 38 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero la munthu wozunzikaSalmo la Davide la chikumbutso.

1Inu Chauta musandikwiyire ndi kundidzudzula.

Musapse mtima ndi kundilanga.

2Mivi yanu yandilasa,

ndipo dzanja lanu landipsinja.

3Thupi langa lilibe mphamvu

chifukwa cha ukali wanu.

M'nkhongono mwanga mwalobodoka

chifukwa cha uchimo wanga.

4Machimo anga andimiza msinkhu,

akundilemera ngati katundu woposa mphamvu zanga.

5Mabala anga aola ndipo akununkha

chifukwa cha kupusa kwanga.

6Ndapindika msana kwathunthu, ndaŵerama zedi,

ndatha mphamvu, tsiku lonse ndimangonka ndilira.

7Thupi langa likutentha kwambiri ndi malungo,

ndipo lilibe nyonga.

8Ndatheratu, ndipo ndatswanyika.

Ndikubuula chifukwa cha kuvutika mu mtima.

9Ambuye, mumadziŵa zonse zimene ndimakhumba,

kusisima kwanga sikuli kosamveka kwa Inu.

10Mtima wanga ukugunda, mphamvu zandithera,

ndipo sindikutha kupenya bwino.

11Abwenzi anga ndi anzanga omwe amandiimira kutali,

chifukwa cha matenda anga.

Achibale anga nawonso amandipewa.

12Anthu ofunafuna moyo wanga,

amanditchera misampha.

Ofuna kundipweteka amalankhula zondiwononga,

tsiku lonse amangolingalira zondichita chiwembu.

13Koma ine ndili ngati gonthi, sindikumvako,

ndili ngati mbeŵeŵe amene satha kulankhula.

14Inde ndili ngati munthu amene saamva,

chifukwa sindingathe kuyankhapo kanthu,

pamene akundilankhula.

15Koma tsono ndimayembekezera Inu Chauta,

Ndinu Chauta, Mulungu wanga amene mudzayankha.

16Popeza ndimapemphera kuti,

“Musalole konse kuti akondwerere pa ine,

amene amandinyodola akaona kuti ndikuterereka.”

17Inde, ndili pafupi kugwa,

ndipo ndikumva kuŵaŵa nthaŵi zonse.

18Ndikuvomera kuipa kwanga,

ndikuda nkhaŵa chifukwa cha machimo anga.

19Ngamphamvu adani amene amafuna moyo wanga,

ngambiri amene amandida popanda chifukwa.

20Anthu amene amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino

ndiwo adani anga,

chifukwa ine ndimachita zabwino.

21Musandisiye ndekha, Inu Chauta,

Inu Mulungu wanga, musakhale nane kutali.

22Fulumirani kudzandithandiza,

Inu Ambuye, Mpulumutsi wanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help