Mas. 88 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chithandizoSalmo la ana a Kora. Kwa Woimbitsa Nyimbo. Kutsata maimbidwe a nyimbo yoti: Pa matenda ndi pa mazunzo. Ndakatulo ya Hemani wa fuko la Ezara.

1Inu Chauta, Mpulumutsi wanga,

ndimalirira Inu usana ndi usiku,

kuti mundithandize.

2Pemphero langa lifike kwa Inu,

tcherani khutu kuti mumve kulira kwanga.

3Pakuti mtima wanga ndi wodzaza ndi mavuto,

moyo wanga ukuyandikira ku malo a anthu akufa.

4Ndikuŵerengedwa pamodzi ndi anthu otsikira ku manda.

Ndasanduka munthu wopanda mphamvu.

5Ndili ngati munthu womsiya yekha pakati pa anthu akufa,

ngati munthu wophedwa amene wagona m'manda.

Ndili ngati anthu amene Inu simuŵakumbukiranso,

popeza kuti ndi ochotsedwa m'manja mwanu.

6Inu mwandiika pansi penipeni pa dzenje

m'malo akuya a mdima wandiweyani.

7Mkwiyo wanu ukundipsinja,

mukundimiza ndi mafunde anu onse.

8Inu mwachititsa kuti anzanga azindithaŵa,

mwandisandutsa chinthu choŵanyansa.

Ndatsekerezedwa kotero kuti sindingathe kuthaŵa.

9M'maso mwanga mwada ndi chisoni.

Tsiku ndi tsiku ndimakuitanani, Inu Chauta,

Ndimakweza manja anga kwa Inu.

10Kodi zodabwitsa mumachitira anthu akufa?

Kodi iwowo nkuuka kuti akutamandeni?

11Kodi chikondi chanu chosasinthikacho

amachilalikira ku manda?

Kodi amasimba za kukhulupirika kwanu

ku malo achiwonongeko?

12Kodi zodabwitsa zanu zimadziŵika mu mdima?

Ndani angadziŵe za chithandizo chanu chopulumutsa

m'dziko la anthu oiŵalika?

13Koma ine ndimalirira Inu Chauta,

m'maŵa pemphero langa limakafika kwa Inu.

14Inu Chauta, chifukwa chiyani mukunditaya?

Chifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu?

15Kuyambira ubwana wanga mpaka kukula,

ndakhala ndikupirira zilango zanu

pozunzika mpaka pafupi kufa,

tsopano ndatheratu.

16Mkwiyo wanu wandimiza,

moyo wanga waonongekeratu ndi ukali wanu woopsa.

17Zonsezi zimandizinga tsiku lonse ngati chigumula,

zanditsekereza kwathunthu.

18Inu mwathaŵitsa anthu ondikonda ndi abwenzi anga,

mdima wokha ndiye mnzanga amene wanditsalira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help