Mas. 144 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumu ithokoza Mulungu chifukwa cha kupambana pa nkhondoSalmo la Davide.

1Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza,

amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga

kumenya nkhondo.

2Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza,

ndiye linga langa londipulumutsa,

ndiye chishango changa chothaŵirako.

Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.

3 Yob. 7.17, 18; Mas. 8.4 Inu Chauta, kodi munthu nchiyani, kuti muzimsamala?

Mwana wa munthu nchiyani, kuti muzimganizira?

4Munthu ali ngati mpweya,

masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.

5Ng'ambani thambo, Inu Chauta, ndi kutsikira pansi.

Khudzani mapiri kuti afuke nthunzi.

6Ng'animitsani zing'aning'ani ndi kuŵamwaza adani anga.

Ponyani mivi yanu, ndi kuŵapirikitsa.

7Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba.

Landitseni ndi kundipulumutsa ku madzi ozama,

omboleni m'manja mwa akunja,

8amene amalankhula zabodza,

ndipo amalumbira zonama.

9Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Inu Mulungu.

Ndidzakuimbirani zeze wa nsambo khumi,

10Inu amene mumapambanitsa mafumu pankhondo,

amene mumalanditsa Davide mtumiki wanu.

11Landitseni kwa adani ankhalwe,

mundipulumutse m'manja mwa akunja,

amene amalankhula zabodza,

ndipo amalumbira zonama.

12Ana athu aamuna pachinyamata pao

akhale amphamvu ngati mitengo,

ana athu aakazi akhale okongola

ngati nsanamira zozokotedwa zapangodya,

zoti zikometse nyumba yaufumu.

13Nkhokwe zathu zikhale zodzaza,

zisunge zokolola za mtundu uliwonse.

Nkhosa zathu zibale ana zikwizikwi m'mabusa athu.

14Ng'ombe zathu zikhale ndi maŵele,

zisapoloze kapena kulephera kubereka.

M'miseu mwathu musakhale kulira chifukwa cha mavuto.

15Ngodala anthu olandira madalitso ameneŵa.

Ngodala anthu amene Mulungu wao ndi Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help