1Pambuyo pake Chauta adandilankhulira m'makutu chokweza, adati, “Senderani pafupi, inu odzalanga mzindawu, aliyense akhale atatenga chida chake choonongera.”
2Pamenepo ndidaona anthu asanu ndi mmodzi akufika kuchokera ku chipata chakumtunda cha Nyumba ya Mulungu choyang'ana kumpoto chija, aliyense atatenga chida chankhondo. Pagulu paopo panali munthu wina wovala bafuta, atatenga zolembera pambalipa. Onsewo adaloŵa nakaima pambali pa guwa lamkuŵa.
3Tsono ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele udaoneka kuchokera mwa akerubi m'mene unaliri, nufika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Chauta adaitana munthu wovala zabafuta uja amene anali ndi zolembera pambali pake.
4Chiv. 7.3; 9.4; 14.1 Adamuuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu, ukaike chizindikiro pamphumi pa anthu onse amene akubuula ndi kulira chifukwa choipidwa ndi zonyansa zimene zikuchitika kumeneko.”
5Kenaka ndidamva Mulungu akuuza anzake ena aja kuti, “Mtsateni mumzinda monse, mukakanthe aliyense. Musakachite kaso ndi aliyense, musakachite konse chifundo.
6Muŵapheretu onse: okalamba, anyamata, atsikana, tiana, ndi akazi omwe. Koma musakhudze aliyense amene ali ndi chizindikiro chija. Muyambire ku Nyumba yanga yoyera.” Motero iwo aja adayambira kupha akulu a pakhomo pa Nyumba ya Chauta.
7Tsono Chauta adanena kuti, “Iipitseni Nyumba yangayo, ndipo mabwalo ake muŵadzaze ndi mitembo. Tiyeni, pitani!” Motero iwo adapita kukapha anthu mumzindamo.
8Pamene ankaŵapha, ine ndidatsala ndekha. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba ndi kufuula kuti, “Aa! Inu Ambuye Chauta, kodi mwakwiya nawo ndithu anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti mudzapha onse otsala ku Israele?”
9Mulungu adayankha kuti, “Uchimo wa Israele ndi Yuda ndi waukulu kwambiri. Dziko ladzaza ndi zophana, mzinda wadzaza ndi zosalungama. Anthu akunena kuti, ‘Chauta walisiya dzikoli. Sakuziwona zimene zikuchitikazi!’
10Nchifukwa chake ine sindidzaŵamvera chifundo kapena kuŵalekerera. Ndidzaŵalanga potsata zochita zaozo.”
11Ndipo munthu wovala zabafuta uja, ali ndi zolembera pambali pake, adadzafotokozera Chauta kuti, “Ndachita zimene munandilamula zija.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.