1 Ahe. 11.31; Yak. 2.25 Tsono Yoswa, mwana wa Nuni, adatuma anthu aŵiri okazonda mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu, naŵalangiza kuti, “Pitani, mukalizonde dzikolo, makamaka mukazondenso mzinda wa Yeriko.” Motero adapita anthu ozondawo, nakafikira ku nyumba ya mkazi wina wadama dzina lake Rahabu. Kumeneko nkumene adagona.
2Mfumu ya mzinda wa Yerikowo idamva kuti, “Aisraele ena afika mumzinda muno usiku, kudzazonda dziko.”
3Pomwepo mfumuyo idatuma anthu kwa Rahabu kukamuuza kuti, “Anthu amene ali m'nyumba mwakowo abwera kudzazonda dziko lonseli, tsono atulutse.”
4Koma pamenepo mkaziyo nkuti ataŵatenga amuna aŵiriwo naŵabisa, motero adayankha kuti, “Zoonadi kunyumba kwanga kuno kudaabwera anthu ena, koma kumene ankachokera, sindikudziŵa.
5Kuno achoka ndi chisisira, chipata cha mzinda uno chili pafupi kutsekedwa. Sindidaŵafunse kumene akupita, koma mukaŵalondola, mungathe kuŵapeza.”
6Pamenepo nkuti ataŵakweza pa denga azondiwo, nkuŵabisa pansi pa mapesi padengapo.
7Atangochoka anthu otumidwa ndi mfumuwo kutuluka mumzindamo, chipata chidatsekedwa. Ndipo adapita ku mseu kukaŵafunafuna azondiwo, mpaka adakafika ku dooko la Yordani.
8Tsono azondiwo asanagone, Rahabu adakwera padengapo
9naŵauza kuti, “Ndikudziŵa kuti Chauta wakupatsani dziko lonseli, ndipo tonsefe tikuchita mantha, mitima yathu ili thithithi!
10Eks. 14.21; Num. 21.21-35 Inde, tamva m'mene Chauta adaphwetsera Nyanja Yofiira inu mukufika, m'mene munkatuluka ku Ejipito. Tamvanso m'mene mudakanthira mafumu aŵiri a Aamori, Sihoni ndi Ogi, kuvuma kwa Yordani kuja. Mudakantha ndi magulu ao ankhondo omwe.
11Titangomva zimenezi, tonsefe tidataya mtima, ndipo mantha adatigwira kukuwopani inu. Tikudziŵa kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa kumwamba ndi dziko lonse lapansi.
12Tsopano mulumbire pamaso pa Chauta kuti mudzasunga zimene mulonjeze, ndipo kuti mudzachitira chifundo banja langa, monga momwe ndakusamalirani inu, ndipo munditsimikizire kwenikweni.
13Bambo wanga, mai wanga, pamodzi ndi alongo anga, abale anga ndi mabanja ao omwe, tonsefe mudzatisungire moyo, musadzatiphe.”
14Anthuwo adamuyankha kuti, “Ife tili okonzeka kufa kuti tikupulumutse iwe. Ukapanda kuulula zimene tachitazi, ifenso tidzasunga lonjezo lathu ndi iwe mokhulupirika, Chauta akadzatipatsa dzikoli.”
15Nyumba ya Rahabuyo idaali pa linga la mzindawo. Motero azondiwo atatulukira pa windo, Rahabu adaŵatsitsa pansi ndi chingwe.
16Anali ataŵauza kuti, “Pitani mudzere kumapiriko, kuti otumidwa ndi mfumu aja angakupezeni. Papite masiku atatu mukubisalabe, mpaka iwowo atachokako. Zitatero tsono, mungathe kumapita.”
17Tsono anthuwo adauza Rahabuyo kuti, “Lonjezo limene watilonjezetsali, tidzalisunga.
18Mvetsa tsono. Tikadzaloŵa, iweyo udzamange chingwe chofiirachi pawindo pomwe watitulutsirapa. Bambo wako, mai wako, abale ako ndi onse a m'banja la bambo wako, adzakhale m'nyumba mwako muno.
19Wina akadzatuluka m'nyumbamo kuti azidzayenda mu mseu, izo adzaone nzake, ife sitidzapalamula kanthu. Koma wina aliyense wokhala m'nyumba mwakomo akadzaona tsoka, mlandu udzakhala wathu.
20Komanso, ukangoulula zimene tikuchitazi, ife sitidzasunga lonjezo lathu tachitali.”
21Apo Rahabu adaŵayankha kuti, “Zikhaledi monga momwe mwaneneramo.” Pomwepo adaŵatulutsa, ndipo azondiwo adachoka. Tsono Rahabu adamanga chingwe chofiira pawindo paja.
22Pambuyo pake azondi aja adapita ku mapiri nakabisala, ndipo otumidwa ndi mfumu aja adaŵafunafuna ponseponse masiku atatu. Komabe sadapeze ndi mmodzi yemwe, motero adangobwerera.
23Pomwepo azondi aŵiri aja adatsika kumapiri kuja, ndipo ataoloka mtsinje uja, adakafika kwa Yoswa, namusimbira zimene adakumana nazo.
24Adauza Yoswayo kuti, “Ife tatsimikizadi kuti Chauta watipatsa dziko lonselo. Anthu onse kumeneko akuchita nafe mantha kwambiri.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.