Yer. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Fanizo la woumba mbiya

1Chauta adauza Yeremiya kuti,

2“Nyamuka, upite ku nyumba ya munthu woumba mbiya, kumeneko ukamva mau anga.”

3Motero ndidatsikira ku nyumba ya woumba mbiya, ndipo ndidampeza akuumba mbiya pa mkombero.

4Chiŵiya chimene ankaumbacho chitakhala chopotoka pomalinga ndi kaumbidwe kake kolakwika, iye uja ankaumbanso chiŵiya china ndi dothi lomwelo, monga ankafunira mwiniwakeyo.

5Tsono Chauta adafunsa kuti.

6“Inu Aisraele, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira woumba mbiya? Zedi, inuyo muli m'manja mwangamu monga momwe umakhalira mtapo m'manja mwa woumba mbiya.

7Ngati ndichenjeza mtundu wa anthu kapena ufumu kuti ndidzaugwetsa ndi kuuwononga,

8ngati mtundu umene ndauchenjezawo uleka machimo ake, ndiye kuti sindidzaulanga monga m'mene ndinkaganizira.

9Momwemonso ngati ndifuna kuyambitsa ndi kukhazikitsa mtundu kapena ufumu wina,

10koma mtunduwo nkumapitiriza kuchita zoipa pamaso panga, osamvera mau anga, ndiye kuti sindidzauchitira zabwino zimene ndidaati ndiwuchitire.

11Pita tsono, ukauze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti Chauta akuti, Ine ndikukonzekera zoti ndikuchiteni, ndikuganiza zoti ndikulangeni. Bwererani nonse, aliyense aleke njira zake zoipa. Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu.

12“Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nzopanda pake. Tidzachita monga m'mene tifunira, ndipo aliyense mwa ife azidzangotsata zoipa za mtima wake wokanika.’ ”

Anthu akana Chauta

13Nchifukwa chake Chauta akunena kuti,

“Ukafunse anthu a mitundu ina yonse,

ngati alipo amene adamvapo zotere.

Israele amene adaali ngati namwali wosadziŵa mwamuna

wachita chinthu choipa kwambiri.

14Kodi chisanu chimatha pa mathanthwe

otsetsereka a phiri la Lebanoni?

Kodi mitsinje ya madzi ozizira ochokera

ku phiri la Lebanoni imaphwa?

15Ai, komabe anthu anga andiiŵala.

Amafukizira lubani mafano opanda pake.

Amakhumudwa m'njira zao zakale.

Amayenda m'njira zodzera m'thengo,

kusiya mseu wabwino.

16Dziko lao amalisandutsa lochititsa nyansi

ndi lodzetsa mfuu wa mantha mpaka muyaya.

Aliyense wodutsamo adzakhala akudabwa ndi

kumapukusa mutu.

17Ndidzaŵabalalitsa ngati mphepo yakuvuma.

Adzathaŵa pamene adani ao akufika.

Ndidzaŵafulatira osaŵathandiza pa nthaŵi

ya mavuto ao.”

Adani a Yeremiya amchita chiwembu

18Anthu ena adati, “Tiyeni tsono tipangane zoti timchite Yeremiya. Ansembe otitsogolera tidzakhala nawobe. Tidzakhala nawo ndithu anzeru otilangiza, ndiponso aneneri otilalikira mau a Mulungu. Tiyeni tipeze zifukwa zomuimbira mlandu, ndipo mau ake tisaŵasamale konse.”

19Apo ndidapemphera kwa Mulungu kuti,

“Inu Chauta, mundimvere,

mumve zimene adani anga akunena za ine.

20Kodi choipa chingakhale dipo la chinthu chabwino?

Komabe andikumbira dzenje.

Kumbukirani kuti paja ndidaabwera kwa Inu

kudzaŵapempherera kuti muleke kuŵakwiyira.

21Nchifukwa chake mulange ana ao ndi njala.

Muŵaononge ndi nkhondo.

Akazi ao akhale amasiye, opanda ana.

Amuna ao afe ndi mliri,

anyamata ao afe ndi lupanga ku nkhondo.

22Muŵatumire gulu lankhondo

lidzaŵakanthe modzidzimutsa,

ndipo kulira kwamantha kumveke m'nyumba zao.

Iwotu andikumbira dzenje loti andiponyemo,

ndipo atchera mapazi anga msampha.

23Inu Chauta, mukudziŵadi ziwembu zao zonse

zofuna kundipha.

Musaŵakhululukire zolakwa zao,

ndithu, musaŵachotsere machimo ao.

Agonjetsedwe pamaso panu,

ndipo muŵalange muli okwiya.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help