1Tsiku lina Aefuremu adamufunsa Gideoni kuti, “Kodi udalekeranji kutiitana ife pamene unkakamenyana ndi Amidiyani?” Ndipo adamkalipira kwambiri.
2Iye adaŵayankha kuti, “Ndachita chiyani ine kuyerekeza ndi zimene mwachita inu? Kodi zimene mwachita inu Aefuremu si zazikulu koposa zimene fuko langa la Abiyezere lachita?
3Mas. 83.11 Mulungu wapereka m'manja mwanu mafumu a Midiyani, Orebu ndi Zebu. Ndachita chiyani kuyerekeza ndi zimene mwachita inu?” Gideoni atanena mau amenewo, anthuwo mitima yao idatsika.
4Gideoni adafika ku Yordani naoloka mtsinjewo, iye pamodzi ndi anthu 300 aja amene nali nawo, atatopa kwambiri, koma akupirikitsabe adani ao.
5Tsono atafika ku mudzi wa Sukoti, Gideoni adapempha eni mudziwo kuti, “Chonde, apatseniko buledi anthu ali ndi ineŵa, pakuti atopa kwambiri. Tikupirikitsa Zeba ndi Zalimuna, mafumu a Midiyani.”
6Koma atsogoleri a ku Sukoti adayankha kuti, “Kodi Zeba ndi Zalimuna waŵagonjetsa kale, m'mene ukuti tiŵapatse buledi ankhondo akoŵa?”
7Gideoni adayankha kuti, “Ai, chabwino! Chauta akapereka Zeba ndi Zalimuna m'manja mwanga, ndidzakukwapulani ndi matsatsa a minga yam'chipululu.”
8Kuchokera kumeneko adapita ku Penuwele kukapemphanso buledi. Koma anthu a ku Penuwele adamuyankha monga momwe adamuyankhira anthu a ku Sukoti.
9Apo Gideoni adauza anthu a ku Penuwele kuti, “Pamene ndizikabwerera nditagonjetsa, ndidzagwetsa nsanja ili apayi.”
10Nthaŵiyo nkuti Zeba ndi Zalimuna ali ku Karikori pamodzi ndi ankhondo ao, anthu pafupi 15,000. Iwoŵa ndiwo amene adatsalako mwa ankhondo a anthu akuvuma, pakuti ankhondo adaafapo 120,000.
11Gideoni adadzera njira ya anthu okhala m'mahema kuvuma kwa Noba ndi Yogobeha, ndipo adaŵathira nkhondo ankhondowo, pakuti anali osakonzekera.
12Zeba ndi Zalimuna adathaŵa. Gideoni adaŵapirikitsa nagwira mafumu aŵiri a Midiyaniwo, ndipo ankhondo ao onse adathaŵa ndi mantha.
13Tsono Gideoni mwana wa Yoasi adabwerako ku nkhondo kudzera ku chikweza cha Heresi.
14Kumeneko adagwira mnyamata wa ku Sukoti, nayamba kumfunsa mafunso. Mnyamatayo adalembera Gideoni maina a atsogoleri ndi a akuluakulu ena a ku Sukoti, okwanira makumi asanu ndi aŵiri.
15Apo Gideoni adabwera kwa anthu a ku Sukoti naŵauza kuti, “Naŵa anthu aja, Zeba ndi Zalimuna, aja munkandinena nawoŵa kuti, ‘Kodi Zeba ndi Zalimuna waŵagonjetsa kale, m'mene ukuti tiŵapatse buledi anthu ako otopa kwambiriŵa?’ ”
16Pamenepo Gideoni adagwira akuluakulu amumzindamo, ndipo adatenga matsatsa a minga yam'chipululu, naŵakwapula anthu a ku Sukotiwo.
17Ndipo adagwetsa nsanja ya ku Penuwele ija, napha anthu onse amumzindawo.
18Tsono Gideoni adafunsa Zeba ndi Zalimuna kuti, “Kodi anthu amene mudaŵapha ku Tabori aja ankaoneka bwanji?” Iwo adayankha kuti, “Aliyense ankaoneka monga momwe ukuwonekera iwemu. Ankaoneka ngati ana a mfumu.”
19Gideoni adaŵauza kuti, “Amene aja anali abale anga, ana a mai wanga. Ndikulumbira pamaso pa Chauta kuti, ‘Mukadapanda kuŵapha, inenso sindikadakuphani.’ ”
20Apo adauza Yetere, mwana wake wachisamba, kuti, “Tiye, ipha anthuŵa.” Koma mnyamatayo sadasolole lupanga lake pakuti ankaopa, chifukwa anali akali mnyamata.
21Tsono Zeba ndi Zalimuna adauza Gideoni kuti, “Mutiphe ndinu, pakuti inuyo ndiye muli ndi mphamvu za munthu wamkulu.” Pamenepo Gideoni adapha Zeba ndi Zalimuna. Ndipo adachotsa mphande zimene zinali m'khosi mwa ngamira zao.
22Tsono Aisraele adamuuza Gideoni kuti, “Muzitilamulira inuyo, mwana wanu ndi zidzukulu zanu, pakuti ndinu amene mwatipulumutsa kwa Amidiyani.”
23Koma Gideoni adaŵayankha kuti, “Ine sindidzakulamulirani, mwana wanganso sadzakulamulirani. Chauta ndiye amene adzakulamulirani.”
24Gideoni adaŵauzanso kuti, “Ndikupempheni kanthu kamodzi. Aliyense mwa inu andipatse ndolo zimene adafunkha.” (Adani aja anali ndi ndolo zagolide chifukwa chakuti anali Aismaele).
25Iwo adayankha kuti, “Tikuvomera kukupatsani zimenezi.” Apo adayala chovala, ndipo munthu aliyense adaponyapo ndolo zofunkhazo.
26Kulemera kwake kwa ndolo zagolide zimene anthu adaperekazo kunali makilogramu 20, osaŵerengera kulemera kwa mphande, ukufu wam'khosi, zovala zofiira za mafumu a Midiyani, ndiponso malamba am'khosi a ngamira.
27Ndi golideyo adapanga efodi naikhazika mu mzinda wake ku Ofura. Tsono Aisraele onse adasiya Mulungu nayamba kupembedza efodiyo kumeneko, ndipo idasanduka msampha kwa Gideoniyo ndi kwa banja lake.
28Choncho Amidiyani adagonjetsedwa ndi Aisraele ndipo sadayesenso zoŵaukira. Motero dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai pa nthaŵi ya Gideoni.
Kufa kwa Gideoni.29Gideoni mwana wa Yoasi adapita kukakhala kwao.
30Tsono anali nawo ana 70, akeake ndithu, pakuti anali ndi akazi ambiri.
31Mzikazi wake wina amene anali ku Sekemu, adamubaliranso mwana dzina lake Abimeleki.
32Gideoni, mwana wa Yoasi, adafa ndi ukalamba, naikidwa m'manda a Yoasi bambo wake ku Ofura, mzinda wa Abiyezere.
33Atangomwalira Gideoni, Aisraele adayambanso kupembedza Abaala, nasandutsa Baala wa Chipangano mulungu wao.
34Aisraelewo sadakumbukirenso Chauta, Mulungu wao, amene adaŵapulumutsa kwa adani ao onse a mbali ndi mbali.
35Ndipo sadaonetse mtima wothokoza kwa banja la Yerubaala (ndiye kuti Gideoni), chifukwa cha zabwino zonse zimene iye adaŵachitira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.