1Chaka chachitatu cha ufumu wa Kirusi, mfumu ya ku Persiya, Daniele amene ankatchedwa Belitesazara, adamva mau. Mauwo uthenga wake unali woona, ndipo unkanena za nkhondo yaikulu. Daniele adaumvetsa uthengawo pamene adaona zinthu m'masomphenya.
2Masiku amenewo, ine Daniele ndidalira pa milungu itatu.
3Ndidaleka kudya zakudya zonse zabwino. Sindidadye nyama kapena kumwa vinyo, ndipo sindidadzole mafuta pa milungu itatu yonseyo.
4Pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, ndinali pa gombe la mtsinje waukulu wa Tigrisi.
5Poyang'ana, ndidaona munthu atavala zabafuta ndi lamba wa golide wa ku Ufazi m'chiwuno mwake.
6Thupi lake linali lonyezimira ngati mwala woŵala. Nkhope yake inali yoŵala ngati mphezi. Maso ake anali ngati malaŵi a moto. Mikono yake ndi miyendo yake zinali zoŵala ngati mkuŵa wopukuta bwino. Mau ake ankamveka ngati a chinamtindi cha anthu.
7Ndine ndekha Daniele amene ndidaona zinthuzo m'masomphenya, koma anthu amene anali nane sadaziwone. Koma iwo adaachita mantha kwambiri, nkuthaŵa nakabisala.
8Ineyo ndidatsala ndekha ndikuyang'ana zinthu ndinkaonazo, koma mphamvu zidandithera. Nkhope yanga idasanduka nikhala yachisoni, ndipo sindidapezenso mphamvu.
9Kenaka ndidamva mau ake. Ndiye nditamva mauwo, ndidadzigwetsa pansi chafufumimba nthaŵi yomweyo ndafa nato tulo.
10Pambuyo pake dzanja lidandigwira ndi kundidzutsa, ine ndili njenjenje m'maondomu ndi m'manjamu.
11Mngeloyo adandiwuza kuti, “Iwe Daniele, munthu wokondeka kwambiriwe, imirira umve mau amene ndikukuuza, pakuti ndatumidwa kwa iwe.” Pamene ankandilankhula, ndidaimirira ndili njenjenje.
12Koma iyeyo adati, “Usachite mantha Daniele, pakuti kuchokera tsiku loyamba, pamene udatsimikiza zoti umvetse zinthu ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mapemphero ako adamveka, motero ndabwera kuti ndiyankhe mapemphero akowo.
13Mngelo wamkulu wa ufumu wa ku Persiya ankandiletsa pa masiku 21, koma Mikaele, mmodzi mwa angelo akuluakulu, adadzandithandiza. Ndidamsiya kumeneko akulimbana ndi woyamba uja.
14Tsono ndabwera kuti ndikufotokozere zimene zidzaŵachitikire anthu ako masiku akubweraŵa. Zinthu udaziwona m'masomphenyazi zidzachitika masiku akubweraŵa.”
15Pamene ankalankhula nane mau ameneŵa, ndidangoti pansi zoli, osalankhula.
16Ndiye wina wooneka ngati munthu adakhudza milomo yanga. Tsono iye ali chiimire pamaso panga, ndidayamba kulankhula, ndidati, “Inu mbuye wanga, zimene ndaona m'masomphenyazi zandilasa mtima, ndipo ndilibe mphamvu.
17Kodi ine kapolo chabe ndingathe kulankhula bwanji ndi mbuye wanga? Mphamvu zanga zandithera, ndipo sindikuthanso kupuma.”
18Tsono wonga munthu uja adandikhudza, nandibwezeranso mphamvu.
19Adati, “Usaope, iwe wokondeka kwambiriwe. Mtendere ukhale nawe. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima.” Akulankhula nane choncho, ndidapezanso mphamvu, ndipo ndidati “Lankhulani mbuye wanga, poti mwandilimbitsa.”
20Iyeyo adandifunsa kuti, “Kodi ukudziŵa chimene ndadzera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mngelo wamkulu wa ku Persiya uja. Tsono ndikakathana naye, mngelo wamkulu wa ku Grisi adzabwera.
21Koma ndikuuza zimene zidalembedwa m'buku la zoona. Palibe wina woti angandithandize kulimbana nawo kupatula Mikaele, Mngelo wanu wamkulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.