Lev. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za tsiku lochita mwambo wopepesera machimo

1Chauta adalankhula ndi Mose pambuyo pa imfa ya ana aŵiri a Aroni omwe adaphedwa, atasendera mosayenera pafupi ndi Chauta.

2

9Aroniyo abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Chauta, ndipo aipereke kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.

10Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Azazele, abwere nayo yamoyo pamaso pa Chauta, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo, ndi kuitumiza ku chipululu kwa Azazele.

11“Aroni apereke ng'ombe yamphongoyo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwini, ndipo motero achite mwambo wopepesera machimo ake ndi a banja lake. Tsono aphe ng'ombeyo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwini.

12Kenaka atenge kambiya kodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Chauta, atape lubani wonunkhira ndi woperapera, manja aŵiri, ndipo aloŵe naye kuseri kwa nsalu yochinga.

13Atatero, athire lubani pa moto pamaso pa Chauta, kuti utsi wa lubaniwo uphimbe chivundikiro chimene chikhala chili pamwamba pa bokosi lachipangano, kuti angafe.

14Kenaka atengeko magazi ena a ng'ombeyo, aŵawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha bokosi lachipangano mbali yakuvuma. Ndiponso awazeko magaziwo kasanu ndi kaŵiri ndi chala chake patsogolo pa chivundikirocho.

15 Ahe. 9.12 “Tsono Aroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu. Magazi ake aloŵe nawo kuseri kwa nsalu yochinga, ndi kuchita nawo monga momwe adachitira ndi magazi a ng'ombe, pakuwaza magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho.

16Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera malo oyera chifukwa cha kuipitsidwa kwa Aisraele, ndiponso chifukwa cha kusamvera kwao, ndiye kuti machimo ao onse. Achite chimodzimodzi ndi chihema chamsonkhano chokhala ndi iwo pakati pa machimo ao.

17Musakhale munthu ndi mmodzi yemwe m'chihema chamsonkhano, pamene Aroni akuloŵa kukachita mwambo wopepesera malo oyera. Musakhale munthu mpaka atamaliza kuchita mwambo wopepesera machimo ake a iye mwini, a banja lake, ndi a mpingo wa Aisraele.

18Tsono atatuluka Aroniyo apite ku guwa limene lili pamaso pa Chauta ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ng'ombe yamphongo ndiponso a mbuzi, ndi kuŵapaka pa nyanga za guwalo molizungulira.

19Awazeko magazi ena pamwamba pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri, kuti alipatule ndi kuliyeretsa pochotsa machimo a Aisraele.

Mbuzi yosenza machimo

20“Atamaliza kuchita mwambo wopepesera malo oyera, chihema chamsonkhano pamodzi ndi guwa, wansembeyo apereke mbuzi yamoyo kwa Chauta.

21Tob. 8.3Tsono Aroni asanjike manja ake pamutu pa mbuziyo, ndipo aululire pa mbuzi imeneyo zochimwa zonse za Aisraele pamodzi ndi kusamvera kwao konse, ndiye kuti machimo ao onse. Machimowo aŵaike pamutu pa mbuzi ija, ndipo munthu amene adamusankhiratu aithamangitsire ku chipululu mbuziyo.

22Mbuziyo isenze machimo ao onse ndi kumanka nawo ku chipululu. Munthuyo aileke mbuzi imeneyo kuti ipite ku chipululu.

23 Ezek. 44.19 “Kenaka Aroni aloŵe m'chihema chamsonkhano, avule zovala zabafuta zimene adavala pokaloŵa m'malo oyera zija, ndipo azisiye komweko.

24Asambe thupi lonse ku malo oyera, ndipo avale zovala zake. Atuluke kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero, ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini ndi a anthu.

25Mafuta a nyama ya nsembe yopepesera machimo, aŵatenthere pa guwa.

26Tsono munthu amene adathamangitsira mbuzi kwa Azazele uja, achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, pambuyo pake aloŵe ku zithando.

27Ahe. 13.11 Ng'ombe ndi mbuzi zoperekera nsembe zopepesera machimo zija, zimene magazi ake adabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera malo oyera, azitulutsire kunja kwa zithando. Zikopa zake, nyama yake ndi ndoŵe yake azitenthe.

28Munthu amene atenthe zimenezo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, tsono pambuyo pake angathe kuloŵa ku zithando.

Tsiku la mwambo wopepesera machimo

29 Lev. 23.26-32; Num. 29.7-11 “Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya kuti mwezi wachisanu ndi chiŵiri, pa tsiku lakhumi la mwezi, muzisala zakudya ndipo musagwire ntchito iliyonse, inu mbadwa, ndiponso mlendo wokhala nao pakati panu.

30Pajatu pa tsiku limenelo padzakhala mwambo wopepesera machimo anu, kuti machimo anu achotsedwe. Choncho mudzakhala oyera pamaso pa Chauta.

31Limeneli lidzakhala tsiku lanu lalikulu la sabata lopumula, ndipo mudzasale zakudya. Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya.

32Wansembe amene wadzozedwa nayeretsedwa kuti akhale mkulu wa ansembe onse m'malo mwa bambo wake, adzachite mwambo wopepesera machimo, atavala zovala zopatulika zabafuta.

33Adzachite mwambo wopepesera malo oyera. Adzachitenso mwambo wopepesera chihema chamsonkhano ndi guwa, ndiponso mwambo wopepesera machimo a ansembe anzake ndi a mpingo wonse.

34Limeneli lidzakhala lamulo lanu lamuyaya, kuti muzidzachita mwambo wopepesera machimo onse a Aisraele kamodzi pa chaka.” Tsono Mose adachita monga momwe Chauta adamlamulira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help