Yer. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuchimwa ndi kulangidwa kwa Yuda

1Chauta akuti, “Uchimo wa Yuda ndi wolembedwa ndi cholembera chachitsulo, cha nsonga ya mwala wadaimondi. Uchimowo walembedwa pa mitima yao ndiponso pa maguwa ao.

2Chonsecho ana ao amakumbukira maguwa ao aja ndi zoimiritsa zao zansembe, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse, pa mapiri am'dzikomo.

3Chuma chanu ndi katundu wanu yense ndidzazipereka kwa ofunkha, kuti zikhale dipo la machimo anu ochitika m'dziko lanu lonse.

4Mudzataya dziko limene ndidakupatsani kuti likhale ngati choloŵa chanu. Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu m'dziko limene simulidziŵa. Ndithu mkwiyo wanga uli ngati moto woyaka, ndipo udzayakadi mpaka muyaya.”

5Chauta akunena kuti,

“Tsoka kwa munthu wodalira munthu mnzake,

amene amagonera pa munthu mnzake

kuti amthandize,

pamene mtima wake wafulatira Chauta.

6Woteroyo adzakhala ngati chitsamba m'chipululu,

ndipo sadzapeza zabwino.

Adzakhala m'chipululu mopanda madzi,

m'dziko lamchere m'mene anthu sangathe kukhalamo.

7“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta,

amene amagonera pa Chautayo.

8 Mas. 1.3 Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa

m'mphepete mwa mtsinje,

umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi.

Suwopa kukamatentha,

chifukwa masamba ake safota.

Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa,

ndipo suleka kubala zipatso.”

9Mtima wa munthu ndi chinthu chonyenga kwambiri

kupambana zinthu zonse.

Kuipa kwake nkosachizika.

Kodi ndani angathe kuumvetsa?

10 Chiv. 2.23; Mas. 62.12 “Koma Ine Chauta ndimafufuza maganizo

ndi kuuyesa mtimawo.

Ndimamchitira munthu aliyense

molingana ndi makhalidwe ake

ndiponso moyenerera ntchito zake.”

11Munthu wopeza chuma pobera anthu ena,

ali ngati nkhwali yokonkhomola mazira amene sidaikire.

Masiku asanachuluke, chumacho chimamthera,

potsiriza amasanduka ngati chitsilu.

12Nyumba yathu yopembedzeramo

ili ngati mpando waufumu waulemerero,

wokhazikika pa phiri lalitali chiyambire.

13Inu Chauta, amene Aisraele amagonera pa Inu,

onse okukanani adzaŵachititsa manyazi.

Onse okusiyani adzafafanizika

ngati maina olembedwa pa dothi,

chifukwa chokana Chauta, kasupe wa madzi opatsa moyo.

Yeremiya apempha Chauta kuti amthandize

14Inu Chauta, chiritseni ndipo ndidzachiradi.

Pulumutseni ndipo ndidzapulumukadi.

Ndinu amene ndimakutamandani.

15Anthu akundifunsa kuti,

“Zija ankanena Chautazi zili kuti?

Zitachitikatu kuti tiziwone!”

16Ine sindidakukakamizeni kuti mufikitse zovuta.

Mukudziŵa kuti tsiku la tsoka sindinkalilakalaka.

Zonse zimene ndidalankhula mukuzidziŵa.

17Musandichititse mantha.

Inu nokha ndiye pothaŵira panga, tsoka likandigwera.

18Koma ondizunza ndiwo achite manyazi,

osati ineyo.

Ade nkhaŵa ndi iwowo, osati ineyo.

Tsiku la tsoka liŵafikire,

ndipo muŵaononge kotheratu.

Za kusunga tsiku la Sabata

19Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukaime pa chipata chachikulu chodzerapo anthu ambiri, chimene mafumu a ku Yuda amaloŵerapo ndi kutulukirapo. Upitenso ku zipata zonse za Yerusalemu.

20Ukanene kuti: Imvani mau a Chauta, inu mafumu a ku Yuda, inu anthu a ku Yuda, ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumaloŵera pa zipata zimenezi.

21Neh. 13.15-22M'mau a Chautawo ndi aŵa: Kuti musunge moyo wanu, samalani bwino kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu, kapena kuloŵa naye pa zipata za Yerusalemu.

22Eks. 20.8-10; Deut. 5.12-14 Musanyamule katundu aliyense kutuluka naye m'nyumba mwanu, kapena kugwira ntchito iliyonse pa Sabata. Koma muzilisunga tsiku la Sabatalo kuti likhale lopatulika, monga ndidalamulira makolo anu.

23Iwowo sadamvere kapena kusamalako, koma ndi mitima yokanika adakana kumva ndi kulandira malangizo anga.”

24Tsono Chauta akunena kuti, “Koma inu muzindimvera Ine, ndi kuleka kunyamula katundu kapena kumatuluka naye pa zipata za mzinda uno pa Sabata, ndipo muzisunga tsiku la Sabata osagwira ntchito pa tsiku limenelo.

25Mukatsata zimenezi, ndiye kuti pa zipata za mzinda umenewu pazidzaloŵera mafumu odzakhala pa mpando waufumu wa Davide. Azidzaloŵa atakwera pa magareta ndi pa akavalo, ali pamodzi ndi akalonga ao ndi anthu a ku Yuda ndiponso anthu a mu Yerusalemu. Ndipo anthu adzakhazikika mu mzinda umenewu mpaka muyaya.

26Anthu adzachokera ku mizinda ya Yuda ndi dziko lonse lozungulira Yerusalemu, dziko la Benjamini, dziko lazidikha, dziko lazitunda, ndiponso ku Negebu, atatenga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zalubani, ndiponso nsembe zothokozera, kupita nazo ku Nyumba ya Chauta.

27Koma inu mukapanda kundimvera, mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika, ndipo mukamanyamula katundu aliyense nkumakaloŵa pa zipata za Yerusalemu pa tsiku la Sabata, ndiye kuti ndidzazitentha zipata zimenezo. Moto udzapsereza nyumba zaufumu za ku Yerusalemu, moto wake wosazimika.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help