1Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu?
Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera?
2Ndi munthu amene amayenda mosalakwa,
amene amachita zolungama nthaŵi zonse,
amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.
3Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa,
kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake.
4Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu,
koma amalemekeza anthu omvera Chauta.
Ndi amene amachitadi zimene walonjeza,
ngakhale zikhale zoŵaŵa chotani.
5Ndi amene sakongoza ndalama zake
kuti alandire chiwongoladzanja,
amene salandira chiphuphu
kuti azunze munthu wosalakwa.
Munthu wochita zimenezi,
palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.