1 mfumu pamodzi ndi anthu ake omwe adanjenjemera, monga m'mene mitengo yam'nkhalango imagwedezekera ndi mphepo.
3Tsono Chauta adauza Yesaya kuti, “Tenga mwana wako Seari-Yasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku Munda wa Mmisiri Woyeretsa nsalu.
4Ukamuuze kuti achenjere, akhale phee, asaope, ndipo mtima wake usafooke chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi dziko lake la Siriya ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. Ameneŵa ali ngati zongofuka moto.
5Mfumu ya ku Siriya ndi mfumu ya ku Efuremu apangana kuti akuchiteni choipa. Akunena kuti,
6‘Tiyeni tikalimbane ndi dziko la Yuda, tikaliwopse. Tikaligonjetse kuti likhale lathu, ndipo tikalonge ufumu mwana wa Tabeele kumeneko.’
7“Komabe zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi, akuti,
‘Zimenezo sizidzatheka,
sizidzachitika konse.
8Paja dziko la Siriya
limagonera pa likulu lake Damasiko,
ndipo Damasiko amagonera pa mfumu yake Rezini.
Kunena za Aefuremu, zisanapite zaka 65,
adzaonongedwa kotheratu,
sadzakhalanso mtundu wa anthu.
9Dziko la Efuremu limagonera pa likulu lake Samariya,
ndipo Samariya amagonera pa mfumu yake Peka.
Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu,
ndithu simudzalimba konse.’ ”
Chizindikiro cha Imanuele10Chauta adalankhulanso ndi Ahazi kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
11“Upemphe chizindikiro kwa Chauta, Mulungu wako. Chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.”
12Koma Ahazi adati, “Sindidzapempha, ndipo sindidzayesa Chauta ai.”
13Apo Yesaya adati, “Mumve tsono, inu chidzukulu cha Davide! Kodi sikukukukwanirani kutopetsa anthu, apa mufuna kutopetsa ndi Mulungu wanga yemwe?
14 uja watenga pathupi ndipo adzabala mwana wamwamuna, mwanayo adzamutcha dzina lake Imanuele.
15Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziŵa kukana choipa ndi kusankha chabwino.
16Koma nthaŵi imeneyo isanafike, maiko a mafumu aŵiri amene akukuwopsaniwo, adzakhala atasanduka mabwinja.
17“Chauta adzafikitsa pa inu, pa anthu anu, ndiponso pa banja la bambo wanu, masiku amavuto oti sadakhalepo kuyambira tsiku limene Efuremu adapatukana ndi Yuda. Ndiye kuti adzafikitsa mfumu ya ku Asiriya.”
18“Tsiku limenelo Chauta adzalizira khweru Aejipito ndipo adzabwera ambiri ngati ntchentche, zochokera ku mathero a nthambi za mtsinje wa Nailo. Adzaliziranso Aasiriya ndipo adzabwera ambiri ngati njuchi.
19Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika m'zigwa zozama, m'ming'alu yam'matanthwe ndi pa zitsamba zonse zaminga, ndiponso pa mabusa onse.
20“Tsiku limenelo Ambuye adzalemba wometa wochokera ku tsidya la mtsinje wa Yufurate, ndiye kuti mfumu ya ku Asiriya. Ndi lumo lake adzakumetani tsitsi lakumutu ndi lam'thupi, ndi ndevu zomwe.
21“Tsiku limenelo mwina munthu adzangosunga ng'ombe yaing'ono yamkaka ndi mbuzi ziŵiri.
22Komabe adzapeza ndithu mkaka wochuluka, mwakuti munthuyo azidzadya bwino kwambiri. Pakuti aliyense amene adzatsalire m'dzikomo azidzadya chambiko ndiponso uchi.
23“Tsiku limenelo likadzafika, minda yamphesa yabwino, yomwe ili ndi mitengo yokwana chikwi m'munda uliwonse ndipo mtengo wake ndi masekeli siliva okwana chikwi chimodzi pa mtengo uliwonse, mudzamera a mkandankhuku ndi minga.
24Anthu adzafika kumeneko kudzachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti m'dziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga.
25Ndipo m'mapiri monse m'mene kale munkalimidwa, anthu sadzafikako, kuwopa mkandankhukuwo ndi mingayo. Malowo adzasanduka odyetserako ng'ombe ndi nkhosa basi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.