1Nchifukwa chake abale ako uŵauze kuti,
“Ndinu anthu a Chauta”,
ndiponso kuti, “Chauta wakukondani”.
Israele ali ngati mkazi wosakhulupirika2“Mudzudzule mai wanu,
mumdzudzule pakuti salinso mkazi wanga,
ndipo ine sindinenso mwamuna wake.
Mumdzudzule kuti aleke kuchita chigololo,
zibwenzi zake azichotse pachifuwa pake.
3Akapanda kutero ndimuvula,
kuti akhale monga momwe adabadwira.
Ndidzamuumitsa ngati chipululu,
adzakhala ngati dziko lopanda madzi,
ndidzamphetsa ndi ludzu.
4Ana ake onse sindidzaŵachitira chifundo
chifukwa ndi ana am'chiwerewere.
5Paja mai wao ndi wachiwerewere.
Amene adaŵabala ankachita zomvetsa manyazi.
Ankati, ‘Nditsatira zibwenzi zanga
zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi,
ubweya ndi thonje,
mafuta ndi vinyo.’
6“Nchifukwa chake njira yake ndidzaitseka ndi minga.
Ndidzamuzinga ndi khoma,
kuti asayendenso m'njira zake zakale.
7Adzathamangira zibwenzi zake,
koma sadzapezana nazo.
Adzazifunafuna, koma osazipeza.
Tsono adzati,
‘Ndibwereranso kwa mwamuna wanga uja,
chifukwa ndidaali pabwino ndi iyeyo
kupambana tsopano.’
8Sankadziŵa kuti
ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo ndi mafuta.
Sankadziŵa kuti
ndine amene ndinkamupatsa siliva ndi golide wambiri
zimene anthuwo ankapangira mafano a Baala.
9Nchifukwa chake ndidzamlanda tirigu wanga
pa nthaŵi yodula ndi vinyo wanga pa nthaŵi yofinya.
Ndidzamlandanso ubweya ndi thonje langa
zimene ankavalira.
10Motero ndidzaonetsa dama lake poyera
kwa zibwenzi zake,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe
amene adzampulumutse m'manja mwanga.
11Ndidzathetsa chimwemwe chake chonse,
zikondwerero zake za pokhala mwezi,
za masabata ndi za masiku ena onse opatulika.
12Ndidzaononga mitengo yake yamphesa ndi yankhuyu
imene ankanena kuti,
‘Ameneŵa ndiwo malipiro anga
amene zibwenzi zanga zidandipatsa.’
Ndidzaisandutsa malunje,
ndipo zilombo zizidzadya kumeneko.
13Ndidzamlanga chifukwa choti adafukiza lubani
kwa Abaala pa zikondwerero zao.
Ankadzikongoletsa povala mphete
ndi mikanda yamtengowapatali,
kuti azithamangira zibwenzi zake,
Ine nkumandiiŵala.
Ndatero Ine Chauta.”
Chikondi cha Chauta pa anthu ake14“Tsono tamverani, ndidzamkopa mkaziyo,
ndidzapita naye ku chipululu
ndi kukamsangalatsa ndi mau achikondi.
15 Yos. 7.24-26 Kumeneko ndidzambwezera minda yake yamphesa.
Ndidzasandutsa Chigwa cha Mavuto
kuti chikhale chipata cha kuchiyembekezo.
Ndipo kumeneko azidzandiyankha
monga m'mene ankandiyankhira pa ubwana wake,
atatuluka ku Ejipito.
16Nthaŵi imeneyo pondiitana uzidzati, ‘Amuna anga.’
Suzidzatinso, ‘Baala wanga.’
Ndikutero Ine Chauta.
17Ndidzamletsa kuti asatchulenso maina a Abaala,
Ndithu anthu sadzatchulanso maina aowo popembedza.
18Nthaŵi imeneyo ndidzachita chipangano
ndi nyama zakuthengo,
mbalame zamumlengalenga, ndi zokwaŵa pansi,
kuti ziyanjane ndi anthu anga.
Tsono ndidzathyola uta, lupanga,
ndi zida zina zonse zankhondo,
ndipo ndidzazichotsa m'dzikomo,
kuti iwo apeze moyo wamtendere.
19Iwe Israele, ndidzakutomera
kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya.
Ndidzakutomera mwaungwiro, mwachilungamo,
mwa chikondi chosasinthika,
ndiponso mwachifundo.
20Ndidzakutomera mokhulupirika,
ndipo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
21Chauta akunena kuti,
“Nthaŵi imeneyo ndidzamvera mlengalenga,
mvula idzagwa pa dziko lapansi.
22Nthaka idzamvera tirigu, vinyo ndi mafuta,
ndipo zimenezi zidzamvera Yezireele.
23 Aro. 9.25; 1Pet. 2.10 Israele ndidzamubzala m'dziko kuti akhale wanga.
Ndidzaonetsa chikondi kwa ‘Sakondedwa’ uja.
Anthu amene ndinkaŵatchula ‘Si-anthu-anga,’
ndidzaŵauza kuti, ‘Ndinu anthu anga.’
Ndipo iwo adzanena kuti, ‘Ndinu Mulungu wathu.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.