1Pambuyo pake Mose, ali pamodzi ndi akuluakulu a Aisraele adauza anthu kuti, Muzimvera malamulo onse omwe ndikukupatsani leroŵa.
2
16 Eks. 20.12; Deut. 5.16 “Atembereredwe aliyense wosalemekeza atate ndi amai ake.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
17 Deut. 19.14 “Atembereredwe aliyense wosuntha malire a mnansi wake.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
18 Lev. 19.14 “Atembereredwe aliyense wosokeza munthu wakhungu.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
19 Eks. 22.21; 23.9; Lev. 19.33, 34; Deut. 24.17, 18 “Atembereredwe aliyense woweruza mopotoza milandu ya alendo, ya ana amasiye, ndi ya akazi amasiye.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
20 Lev. 18.8; 20.11; Deut. 22.30 “Atembereredwe aliyense wogona ndi mkazi wa bambo wake, chifukwa wavula mkazi wa bambo wake.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
21 Eks. 22.19; Lev. 18.23; 20.15 “Atembereredwe aliyense wogona ndi nyama.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
22 Lev. 18.9; 20.17 “Atembereredwe aliyense wogona ndi mlongo wake, kapena mlongo wake wa mimba ina.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
23 Lev. 18.17; 20.14 “Atembereredwe aliyense wogona ndi mpongozi wake.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
24“Atembereredwe aliyense wopha mnzake mwachinsinsi.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
25“Atembereredwe onse olandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
26 Aga. 3.10 “Atembereredwe aliyense wosavomereza ndi wosatsata malamulo amene tatchulaŵa.”
Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.