Ezek. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mau odzudzula aneneri onyenga

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, ulose zodzudzula aneneri a ku Israele. Amene amalosa za kukhosi kwao, zongopeka okha, uŵauze kuti amve mau a Ine Chauta!

3Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Tsoka kwa aneneri opusa amene amachita kupeka zolosa zao, chonsecho sadaone chilichonse chochokera kwa Ine.

4Inu Aisraele, aneneri anu akhala ngati nkhandwe zam'mabwinja.

5Simudakwere khoma kuti mukakonze m'mene mudagumuka, kuti banja la Israele lidziteteze kolimba pa nkhondo, pa tsiku la Chauta.

6Aneneriwo amalankhula zonama, ndipo amalosa zabodza. Amanena kuti, ‘Akuterotu Chauta,’ pamene Chauta sadaŵatume konse. Komabe amayembekeza kuti zimene anenazo zidzachitika.

7Koma Ine ndikuti, Zimene inu aneneri mukuti mudaziwona m'masomphenya nzabodza. Ndipo kulosa kwanuko nkwabodza. Mumanena kuti ‘Akuterotu Chauta,’ ngakhale Ine sindidalankhule konse.”

8“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikukutsutsani chifukwa choti mau anu ngachabe, ndipo zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo nzabodza.

9Ndidzakantha aneneri onama amene amati adaona zakutizakuti ngati kutulo, amenenso kulosa kwao nkwabodza. Sadzakhala nao m'bwalo la aphungu la anthu anga. Sadzalembedwa m'kaundula wa nzika za Israele, ndipo sadzaloŵa m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.

10 Yer. 6.14; 8.11 “Ndithudi aneneri asokeza anthu anga pomanena kuti, ‘Kudzakhala mtendere,’ pamene kulibe mtendere, ndipo chifukwa anthu akamanga khoma, aneneri amalipaka njereza.

11Uŵauze opaka njerezawo kuti khomalo lidzagwa. Mvula idzavumba mwamphamvu, kudzagwa matalala akuluakulu, ndipo kudzaomba mphepo yamkuntho.

12Pamenepo khomalo litagwa, nanga anthu sadzakufunsani kuti, ‘Kodi njereza imene mudapaka ija ili kuti tsopano?’

13Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakunthitsa mphepo yolimba nditakwiya. Ndidzavumbitsa mvula yamphamvu ndili ndi ukali. Ndidzagwetsa matalala akuluakulu mwachipseramtima, mpaka khomalo litaonongeka kotheratu.

14Ndidzagwetsa khoma limene mudalipaka njerezalo. Ndidzaligamuliratu mpaka maziko ake ataoneka. Pamene lidzagwa, inunso mudzafera momwemo. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

15Ndimo m'mene ndidzagwiritsire ntchito mkwiyo wanga pa khomalo ndi pa amene ankalipaka njereza aja. Apo ndidzakuuzani kuti, ‘Khoma lagwa, amene ankalimata aja nawonso agwera kumodzi.

16Agwanso aneneri a ku Israele amene ankalosa ku Yerusalemu, amene ankati adaona zamtendere m'masomphenya, pamene mtendere kunalibe.’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Mau odzudzula aneneri aakazi

17“Tsono iwe mwana wa munthu, ugwepo pa nkhani ya akazi amene ali pakati pa anthu ako. Iwowo amalosa zopeka za mumtima mwao, tsono uŵadzudzule.

18Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu zakumutu za anthu a misinkhu yosiyanasiyana, kuti azikola mitima ya anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nkupulumutsa moyo wanu?

19Mwandichotsa ulemu pamaso pa anthu anga, chifukwa chofuna kulandira manja angapo a barele ndiponso zidutswa chabe za buledi. Mukupha anthu osayenera kufa, ndipo mukupulumutsa anthu osayenera kukhala moyo, pomanamiza anthu angaŵa amene amamva zabodza zanuzo.

20“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Ndikuzikana zithumwa zanu zapamkono, zimene mumakolera mitima ya anthu ngati mukukola mbalame. Ndidzazithothola pa mikono yanu, kuti ndiŵapulumutse anthuwo amene mumaŵakola ngati mbalame.

21Ndidzang'ambanso nsalu zanu zamankhwala zakumutu, ndipo ndidzapulumutsa anthu anga m'manja mwanu. Simudzakhalanso ndi mphamvu zoŵakolera. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

22Ndi mabodza anu mudatayitsa mtima anthu anga abwino amene Ine sindidafune kuti ataye mtima. Mudalimbitsa mtima anthu oipa kuti asaleke machimo ao, choncho satha kupulumutsa moyo wao.

23Nchifukwa chake zolosa zanu zabodza zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo, simudzaziwonanso, ndipo simudzaombezanso. Ndidzapulumutsa anthu anga m'manja mwanu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help