1 Sam. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsono Samuele adatenga nsupa ya mafuta nathira mafutawo pamutu pa Saulo. Ndipo adamumpsompsona nati, “Chauta akukudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu ake Aisraele. Udzalamulira anthu a Chauta ndi kuŵapulumutsa kwa adani oŵazungulira. Chizindikiro chakuti Chauta wakudzoza kuti ukhale mfumu yolamulira anthu ake, ndi ichi:

2ukachoka pano lero, ukumana ndi anthu aŵiri ku manda a Rakele ku Zeliza m'dziko la Benjamini. Iwowo akuuza kuti abulu unkafuna aja adapezeka, ndiponso kuti bambo wako waleka kusamala za abuluwo, koma akudera nkhaŵa za iwe, akunena kuti, ‘Nditani ine m'mene mwana wanga sakuwonekamu?’

3Tsono utabzola pamenepo, ufika pa mtengo wogudira wa ku Tabori. Kumeneko ukumana ndi anthu atatu, wina atanyamula anaambuzi atatu, wina atanyamula mitanda itatu ya buledi, ndipo wina atanyamula thumba lachikopa la vinyo, akupita kukapereka nsembe kwa Mulungu ku Betele.

4Atakupatsa moni, akuninkhako mitanda iŵiri ya buledi, iwe uilandire.

5Pambuyo pake mufika ku phiri la Mulungu ku Gibea kumene kuli gulu lankhondo la Afilisti. Ndipo kumeneko, pamene mukuyandikira mzindawo, mukumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku kachisi ku phiri, akuimba zeze, ting'oma, chitoliro ndi pangwe, ndipo akulosa.

6Pamenepo mzimu wa Chauta ukuloŵa mwamphamvu, ndipo nawenso uyamba kulosa nao, usinthika ndi kukhala munthu wina.

7Tsono ukaona zizindikiro zimenezi, uchite chilichonse choyenera nthaŵi imeneyo, poti Mulungu ali nawe.

8Udzatsogola ndiwe kupita ku Giligala. Patapita masiku asanu ndi aŵiri, ndidzabwera kudzapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere. Kumeneko ndidzakulangiza zoti uchite.”

Saulo abwerera kwao.

9Pamene Saulo adatembenuka kuti asiyane ndi Samuele, mtima wake Mulungu adausandutsa winawina. Ndipo zizindikiro zonse zija zidachitikadi tsiku limenelo.

10Atafika ku Gibea, adakumana ndi gulu la aneneri. Tsono mzimu wa Mulungu udamloŵa Sauloyo mwamphamvu, nayamba kulosa nao.

11Onse amene ankamdziŵa kale, ataona kuti akulosa limodzi ndi aneneri, adayamba kufunsana kuti, “Chamchitikira nchiyani mwana wa Kisi? Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”

121Sam. 19.23, 24 Munthu wina wakomweko adayankhako nati, “Nanga enaŵa ndiye abambo ao ndani?” Nchifukwa chake padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”

13Atatha kulosako, Saulo adapita ku kachisi ku phiri.

14Mbale wa bambo wake wa Saulo ataona Sauloyo ndi mnyamata uja, adaŵafunsa kuti, “Mudaapita kuti?” Saulo adayankha kuti, “Tidaakafunafuna abulu. Titaona kuti sakupezeka, tidaapita kwa Samuele.”

15Apo mbale wa bambo wakeyo adati, “Ndikukupempha, uzeko zimene adanena Samuele.”

16Saulo adati, “Samuele adatiwuza bwino lomwe kuti abuluwo adapezeka.” Koma sadanene kanthu za nkhani ya ufumu ija imene Samuele adaamuuza.

Saulo asankhidwa kukhala mfumu.

17Tsono Samuele adaitana anthu ku msonkhano wachipembedzo ku Mizipa.

18Adauza Aisraele onse kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akuti, ‘Ndidakutulutsani inu Aisraele ku dziko la Ejipito, ndipo ndidakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa mafumu onse amene ankakusautsani.’

19Koma lero lino, inu mwamkana Mulungu wanu amene amakupulumutsani m'mavuto anu onse ndi m'masautso anu. Mukuti, ‘Iyai! Koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Nchifukwa chake tsono musonkhane pamaso pa Chauta potsata mafuko anu ndi mabanja anu.”

20Choncho Samuele adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele, ndipo pochita maere, fuko la Benjamini ndilo lidasankhidwa.

21Adasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja, ndipo pochita maere, banja la Matiri ndilo lidasankhidwa. Potsiriza pake adasonkhanitsa anthu a m'banja la Matiri mmodzimmodzi, ndipo pochita maere, Saulo mwana wa Kisi, ndiye adasankhidwa. Koma pamene adamfunafuna, sadampeze.

22Tsono anthuwo adafunsa Chauta kuti, “Mwati munthuyo wafika kuno?” Chauta adayankha kuti, “Inde, akubisala pakati pa katundu.”

23Choncho adathamanga kukamtenga kumeneko. Ndipo ataimirira pakati pa anthu, ankaoneka wamtali, mwakuti anthu ena onse ankamugwa m'mapewa.

24Tsono Samuele adafunsa anthu onsewo kuti, “Kodi mukumuwona munthu amene Chauta wamsankha? Palibe wina wonga ameneyu pakati pa anthu onse.” Ndipo anthu onse adafuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali!”

25Tsono Samuele adafotokozera anthu zinthu zoyenera mfumu pa maudindo ake. Ndipo adazilemba m'buku nakaliika bukulo pa malo oyera pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Samuele adauza anthu kuti abwerere kwao.

26Saulo nayenso adapita kwao ku Gibea, ndipo adatsakana naye anthu amphamvu amene Mulungu adaŵafeŵetsa mtima.

27Koma anthu ena achabechabe adati, “Kodi munthu ameneyu angathe bwanji kutipulumutsa ife?” Ndipo adayamba kumnyoza Sauloyo, osampatsa ndi mphatso zomwe. Koma iye adangokhala chete.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help