Lun. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Israele sapembedza mafano

1Koma Inu, Mulungu wathu,

ndinu okoma mtima ndi okhulupirika.

Ndinu oleza mtima,

olamulira zinthu zonse mwachifundo.

Pajatu ngakhale tichimwe,

timakhalabe ana anu odziŵa mphamvu zanu.

2Koma poti tikudziŵa kuti ife ndife anthu anu,

sitidzachimwa, popeza kuti kukudziŵani Inu

ndiye njira yofikira ku chilungamo chenicheni,

3ndipo kudziŵa mphamvu zanu

ndiye maziko a moyo wamuyaya.

4Sitidasokere potsata maganizo opotoka

a amisiri aluso,

kapena zithunzi zopakidwa utoto wosiyanasiyana

zimene zili ntchito yopandapake ya mmisiri.

5Kungopenya zithunzizo kumautsa chilakolako

mwa munthu wopusa,

ndipo amayamba kukhumbira mapangidwe achabe

a chithunzi chopanda moyo.

6Amene amapanga zithunzi zotere

kapena kuzisirira kapena kuzipembedza,

amakondadi zoipa

ndipo amangoyenera kulandira

zimene amayembekezazo.

Anthu opanga mafano ngopusa

7Pamene mmisiri akuumba dothi lofeŵa,

amapanga mitsuko yake mwaluso kuti itithandize.

Potenga dothi lomwelo, amapanga ziŵiya zina

kuti tizigwiritse ntchito zabwino,

koma zina ndi za ntchito zoipa.

Ndiye zili kwa mmisiriyo kusankhula

m'mene anthu adzagwiritsire ntchito ziŵiya zake.

8Mwina dothi lomwelo amagwiritsa ntchito yopandapake,

nkuumbira mulungu wabodza.

Koma tsono si kale kwambiri munthuyo

adapangidwa ndi dothi lokhalokhalo,

ndipo posachedwa adzabwerera kudothi

komwe adachokera,

pamene adzayenera kubweza moyo

umene adachita kubwerekawu.

9Koma salabadako kuti adzafa

ndipo kuti moyo wake ndi wa nthaŵi yochepa.

Amangofuna kupikisana ndi amisiri

a ntchito za golide ndi siliva,

ndipo amatsanzira ogwira ntchito za mkuŵa.

Amanyadira milungu yabodza imene iye amaumba.

10Mtima wake uli ngati phulusa,

chikhulupiriro chake nchachabe kuposa dothi,

sadziŵa kuti moyo wake ndi wonyozeka kupambana thope,

11popeza kuti sadziŵa amene adamuumba

ndi kumpatsa nzeru zogwirira ntchito,

amenenso adamuuzira mpweya wamoyo.

12Koma iye amangoganiza kuti

moyo wathu wa pansi pano ndi maseŵera,

ndipo kuti nthaŵi yathu ya pansi pano

ili ngati msika wopezerapo phindu.

Amati, “Tiyenera kupeza chuma mwa njira zilizonse,

ndi zoipa zomwe.”

13Munthu ameneyu akatenga dothi kuti aumbire

ziŵiya zosakhalira kusweka kapena mafano,

amadziŵa bwino kupambana ena onse

kuti kutero nkuchimwa.

Kupenga kwa Aejipito

14Koma panali anthu ena opusa kwambiri

ndi omvetsa chisoni kuposa ana aang'ono,

amenewo ndi adani aja

amene ankasautsa mtundu wa anthu anu.

15Mafano onse a akunja iwo ankaŵayesa milungu,

ngakhale mafano ameneŵa maso ake sangathe kupenya,

mphuno zake sizingathe kupuma mpweya,

makutu ake sangathe kumva,

zala za manja ake sizingathe kukhudza kanthu,

ndipo miyendo yake singathe kuyenda.

16Zoonadi, adaŵapanga ndi munthu wina

amene ali ndi mpweya wobwereka.

Palibe munthu amene angathe kupanga mulungu

wofanafana ndi iye mwini.

17Iyeyo ngwodzafa,

ndipo zopanga ndi manja ake ochimwa nzakufa.

Mwiniwakeyo amazipambana

zinthu zimene amazipembedza,

poti ali ndi moyo, koma osati mafanowo.

18Anthuwo amapembedza

ngakhale zilombo zoipa kwambiri,

zimene zimapambana zinzake kusoŵa nzeru.

19Nyamazo palibe munthu angazikhumbire

chifukwa cha kukongola kwake,

zidaphonya matamando ndi madalitso a Mulungu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help