Mas. 149 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tamandani Chauta!

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,

imbani nyimbo yomtamanda

pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.

2Aisraele asangalale ndi Mlengi wao.

Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yao.

3Atamande dzina lake povina,

amuimbire nyimbo yokoma ndi ng'oma ndi pangwe.

4Paja Chauta amakondwera ndi anthu ake,

amaŵalemekeza anthu odzichepetsa

poŵagonjetsera adani ao.

5Okhulupirika akondwerere chigonjetso chopambanachi,

aziimba mokondwa ali gone pa mabedi.

6 2Am. 15.27 Atamande Mulungu kwambiri mokweza mau,

malupanga akuthwa konsekonse ali m'manja,

7kuti alipsire mafuko achikunja,

kuti alange mitundu ina ya anthu.

8Amange mafumu ao ndi maunyolo,

amange atsogoleri ao ndi zitsulo,

9kuti aŵalange monga momwe Mulungu adalamulira.

Umenewu ndiwo ulemerero wa anthu okhulupirira Chauta.

Tamandani Chauta!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help