Mphu. 34 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Maloto si kanthu

1 Deut. 13.1-5; 18.9-14 Anthu opanda nzeru amakhulupirira zinthu

zonama ndi zachabe,

zitsiru zimatekeseka ndi maloto.

2Kukhulupirira maloto kuli ngati kuumirira mtunda

wopanda madzi.

3Maloto amalingana ndi kalilole,

chifaniziro cha nkhope kuyang'anana ndi nkhope yeniyeniyo.

4Kodi m'zonyansa mungachokere kanthu koyera?

Nanga m'mabodza, kodi mungachokere zoona?

5Maula, mipingu ndi maloto, zonsezi nzachabe,

zili ngati zoganizira za munthu wamkazi

pa nthaŵi yake yochira.

6Usaikepo mtima konse pa zimenezo,

pokhapokha ngati Mulungu Wopambanazonse ndiye wazitumiza.

7Ambiri adasokera ndi maloto

ndipo amene ankaŵakhulupirira adaonongeka.

8Kutsata bwino Malamulo sikulira zopeka zonama zoterezi,

nzeru zabwino kwenikweni zimapezeka mwa munthu

wonena zoona.

Za maulendo

9Munthu woyenda kwambiri amadziŵa zambiri,

ndipo munthu amene adaona zambiri, amalankhula zanzeru.

10Amene sadaone zambiri, amangodziŵa zinthu pang'ono,

koma munthu woyenda kwambiri amakhala waluso pa zambiri.

11Ndidaona zinthu zambiri pa maulendo anga,

ndipo zimene ndimazimvetsa nzochuluka kuposa

zimene ndingakambe.

12Kaŵirikaŵiri ndidakumana ndi zoopsa zoti nkadafa,

koma ndidapulumuka chifukwa cha zimene ndidaphunzira.

Za kuwopa Ambuye

13Anthu oopa Ambuye adzakhala ndi moyo,

chifukwa amakhulupirira amene angathe kuŵapulumutsa.

14Munthu woopa Ambuye sadzakayika pa chilichonse.

Sadzakhala wamantha, chifukwa chikhulupiriro

chake chili mwa Ambuye.

15Ngwodala munthu woopa Ambuye,

amadziŵa kumene angapeze chithandizo.

16Ambuye amasunga anthu oŵakonda,

Ambuyewo ndi chishango chao cholimba ndi

mthandizi wamphamvu.

Amaŵateteza ku mphepo yotentha ndi ku dzuŵa lamasana.

Amaŵagwirira kuti asaphunthwe,

amaŵachirikiza kuti asagwe.

17Amasangalatsa mitima yao ndi kuŵalitsa maso ao,

amaŵapatsanso mphamvu, moyo ndi madalitso.

Za kupereka nsembe

18Nsembe zochokera pa phindu loipa nzonyansa,

mphatso za anthu oipa Mulungu sangazilandire.

19Mulungu Wopambanazonse sakondwera ndi nsembe

za anthu osasamala za Iye.

Ngakhale nsembe zaozo zichuluke,

sizingakwanire kupepesa machimo ao.

20Kupereka nsembe ndi chuma cholanda

kwa munthu wosauka

kuli ngati kupha mwana

bambo wake akuwona.

21Chakudya chongolaŵa

ndiye moyo wa anthu osauka,

kuŵalanda chimenecho nkuŵapha.

22Kuba chuma cha mnzako nkumupha,

kunyenga wantchito pa malipiro ndi ngati

kukhetsa magazi ake.

23Ngati munthu wina akumanga nyumba,

wina nkumagwetsa,

kodi aŵiriwo sangodzivuta chabe?

24Ngati wina akupemphera, wina nkumatemberera,

kodi Ambuye adzamvera uti?

25Ngati usamba m'manja utagwira mtembo, kenaka

nkuugwiranso,

kusamba kuja kuli ndi phindu lanji?

26Nchimodzimodzi munthu wosala zakudya chifukwa

cha machimo ake,

kenaka abwerezanso machimo omwewo.

Kodi ndani adzamva mapemphero ake?

Kodi kudzilanga kuja kuli ndi phindu lanji?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help