Yes. 48 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu ndiye amalamulira zam'tsogolo

1Mverani izi inu a banja la Yakobe,

inu amene dzina lanu amakutchulani Aisraele,

inu zidzukulu za Yuda.

Inu mumalumbira dzina la Chauta,

ndipo mumapemphera kwa Mulungu wa Israele,

pamene zimenezo sizichokera mu mtima

woona ndi wolungama.

2Komabe inu mukunyada kuti ndinu

nzika za mzinda wopatulika ndipo kuti

mumakhulupirira Mulungu wa Israele,

amene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.

3Chauta akuuza Israele kuti,

“Zimene zidachitika poyamba ndidaaloseratu kalekale,

zidaatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndidaazilengeza.

Tsono mwadzidzidzi ndidachitapo kanthu,

ndipo zidaonekadi.

4Ndidaadziŵa kuti ndiwe wokanika,

wa nkhongo gwa, ndi wa mutu wouma.

5Ndidaakuuziratu zakutsogolo kalekale.

Zisanachitike ndidaazilengezeratu kwa iwe,

kuti usadzanene kuti,

‘Fano langa ndilo lidachita zimenezi,

fano langa losema ndi fano langa loumba

ndiwo adalamula kuti zichitike!’

6“Zonsezi udazimva,

tsono uzilingalire bwino.

Monga iweyo sungazivomereze?

Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno

ndidzakuuza zinthu zatsopano,

zinthu zobisika zimene sudazidziŵe konse.

7Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino,

osati kalekale.

Mpaka lero unali usanazimve konse,

kuwopa kuti ungamati,

‘Zimenezi ndiye ai, ndidazidziŵa kale.’

8Chikhalire sudamve

chikhalire sudadziŵe,

nkale lonse makutu ako sanali otsekuka.

Chifukwa ndidaadziŵa kuti ndiwe wachiwembu,

ndipo kuti chiyambire cha ubwana wako

adakutchula waupandu.

9“Kuti anthu alemekeze dzina langa

ndikuchedwetsa mkwiyo wanga.

Kuti anthu aone ulemerero wanga

ndikukulezera ukali wanga,

kuti ndisakuwononge kotheratu.

10Ndidakuyeretsa, komatu osati ngati siliva,

ndidakuyesa m'ng'anjo yamasautso.

11Chifukwa cha ulemu wanga,

ulemu wanga wokha, ndiye ndimachita zonse.

Ndingalole bwanji kuti dzina langa linyozeke?

Ulemerero wanga sindidzapatsa wina ai.”

Kirusi, mtsogoleri wosankhidwa ndi Chauta

12 Yes. 44.6; Chiv. 1.17; 22.13 Chauta akunena kuti,

“Mverani Ine, inu zidzukulu za Yakobe,

inu Aisraele, amene ndidakuitanani.

Mulungu uja ndine,

ndine woyamba ndipo ndine wotsiriza.

13Manja anga adamanga maziko a dziko lapansi,

dzanja langa lamanja lidafunyulula mlengalenga.

Ndikaitana dziko lapansi ndi dziko lakumwamba,

zonsezo zimabwera pamodzi kwa Ine.

14“Sonkhanani nonsenu, ndipo mumvetsere.

Mwa milungu ina ndani adalosapo zimenezi?

Amene Chauta amamkonda uja

adzachita zomwe Chautayo adakonzera Babiloni,

ndi dzanja lake lamphamvu adzalimbana ndi Akaldeya.

15Ndine amene ndidalankhula ndi kumuitana.

Ndidambweretsa ndine,

ndipo zonse zidzamuyendera bwino.

16Bwerani pafupi tsono,

kuti mumve zimene nditi ndinene.

Kuyambira pa chiyambi sindidalankhule mobisa,

nthaŵi imene zimenezo zinkachitika,

nkuti Ine ndilipo.”

Tsono Ambuye Chauta andipatsa Mzimu wao, ndipo andituma.

Cholinga cha Chauta pa anthu ake

17Chauta, Mpulumutsi wako,

Woyera uja wa Israele, akunena kuti,

“Ine ndine Chauta, Mulungu wako,

amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino.

Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.

18Ukadamvera malamulo anga,

bwenzi mtendere ukukufikira ngati madzi amumtsinje,

ndipo bwenzi chilungamo chikukuphimba kosalekeza

ngati mafunde apanyanja.

19Ana ako akadachuluka ngati mchenga,

ndipo zidzukulu zako ngati fumbi.

Dzina lao silikadachotsedwa pamaso panga,

silikadafafanizika konse.

20 Chiv. 18.4 “Tulukani m'dziko la Babiloni,

thaŵani m'dziko la ukapolo.

Mulengeze zimenezi ndi mau amphamvu,

muzilalike, muzifikitse

mpaka ku mathero a dziko lapansi.

Muzinena kuti, ‘Chauta waombola Yakobe, mtumiki wake.’ ”

21Pamene ankatsogolera anthu ake m'chipululu,

iwo sadamve ludzu.

Adaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe.

Adang'amba thanthwelo, ndipo mudatuluka madzi.

22 Yes. 57.21 “Koma anthu ochimwa alibe mtendere,”

akuterotu Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help