2 Sam. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide amva za imfa ya Saulo.

1Saulo atamwalira, Davide adabwerako kumene adaakagonjetsa Aamaleke kuja, ndipo adakakhala ku Zikilagi masiku aŵiri.

2Tsono pa tsiku lachitatu lake, adangoona munthu akuchokera ku zithando zankhondo za Saulo, atavala zovala zong'ambika ndiponso atadzithira dothi kumutu. Munthuyo atafika kwa Davide, adadzigwetsa pansi, namlambira.

3Davide adamufunsa kuti, “Ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndathaŵa ku zithando zankhondo za Aisraele.”

4Davide adamufunsanso kuti, “Zinthu zidayenda bwanji? Tandiwuza.” Iye adati, “Anthu athaŵa kunkhondoko, ndipo ambirinso aphedwa. Saulo ndi mwana wake Yonatani, nawonso aphedwa.”

5Apo Davide adamufunsa mnyamatayo kuti, “Iwe wadziŵa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani nawonso adafa?”

61Sam. 31.1-6; 1Mbi. 10.1-6 Mnyamata wodzanena uja adati, “Zidangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa. Kumeneko ndidaona Saulo atangoti zyoli ku mkondo wake. Nthaŵi imeneyo nkuti magaleta ankhondo, ndiponso adani okwera pa akavalo atamuyandikira Sauloyo.

7Tsono Saulo atacheuka nandiwona, adandiitana. Ndidavomera kuti, ‘Ŵaŵa.’

8Adandifunsa kuti, ‘Ndiwe yani?’ Ine ndidati, ‘Ndine Mwamaleke.’

9Apo adandiwuza kuti, ‘Bwera pafupi, undiphe, chifukwa ndikumva ululu woopsa, komabe ndikali moyo.’

10Choncho ndidasendera pafupi, nkumupha, poti ndidaadziŵa kuti akagwa, sakhala moyo. Tsono ndidamuvula chisoti chaufumu kumutu kwake ndi chigwinjiri kumkono kwake, ndipo ndabwera nazo kuno kwa inu mbuyanga.”

11Apo Davide adang'amba zovala zake. Nawonso anthu amene anali naye adachita chimodzimodzi.

12Ndipo anthuwo adabuma maliro. Adalira ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Saulo ndi Yonatani mwana wake. Adaliranso chifukwa cha Aisraele, anthu a Chauta, chifukwa choti anali ataphedwa ku nkhondo.

13Tsono Davide adafunsa mnyamata wodzanena uja kuti, “Kodi iwe ndiwe wa kuti?” Iye adati, “Munthune ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke.”

14Davide adamufunsanso kuti, “Nanga iwe sudachite mantha bwanji kutambalitsa dzanja lako nkupha wodzozedwa wa Chauta?”

15Pomwepo Davide adaitana mmodzi mwa ankhondo ake, namuuza kuti, “Mtenge ameneyu, ukamuphe.” Wankhondoyo adamkanthadi naafa.

16Ndipo Davide adati, “Wadziphetsa wekha, unanena wekha ndi pakamwa pako kuti, ‘Ndidapha wodzozedwa wa Chauta.’ ”

Davide alira maliro a Saulo ndi Yonatani.

17Choncho Davide adaimba nyimbo ya madandaulo, kulira Saulo ndi Yonatani mwana wake.

18Yos. 10.13 Ndipo adalamula kuti mau a madandaulowo aŵaphunzitse kwa anthu a ku Yuda. Mau ake ndi aŵa, monga adalembedwera m'buku la Yasara.

19“Ulemerero wako wathera zitunda zako zachipembedzo,

iwe Israele.

Ha! Kani amphamvu agwa motere!

20Musakanene zimenezi ku Gati,

musakalengeze m'miseu ya ku Asikeloni,

kuti akazi a Afilisti angasekerere,

akazi a anthu osaumbalidwa angakondwe.

21“Inu mapiri a ku Gilibowa,

pa inu pasagwe mame ndi mvula,

pa inu pasapezeke minda yobereka dzinthu.

Paja kumeneko adani adanyoza

chishango cha munthu wamphamvu,

chishango cha Saulo, chosapukutidwapo ndi mafuta.

22“Uta wa Yonatani sudabwereko chabe

osakhetsa magazi a anthu osabayako ankhondo amphamvu.

Ndipo lupanga la Saulo silidabwereko chabe

osapha anthu.

23“Saulo ndi Yonatani pa moyo wao

anali okondedwa ndi okondwetsa,

ndipo sadalekane ali moyo ngakhale pa imfa.

Anali ndi liŵiro loposa la ziwombankhanga.

Anali amphamvu kuposa mikango.

24“Inu akazi a ku Israele, mlireni Saulo.

Chifukwa cha iye uja munkavala zovala zabwino zofiira,

ndiponso munkaika zokometsera zagolide pa zovala zanu.

25“Ha! Kani amphamvu agwa motere!

Yonatani ali gone,

atafa pa zitunda zako zachipembedzo.

26“Mbale wanga Yonatani,

ndikuvutika mu mtima chifukwa cha iwe,

wakhala wapamtima wanga.

Chikondi chako pa ine chinali chodabwitsa kwambiri,

chinali choposa ngakhale chikondi cha akazi.

27“Ha! Kani amphamvu agwa motere,

zida zao zankhondo nkuwonongeka!”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help