Ezek. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

EZEKIELE AYAMBA KUWONA ZINTHU M'MASOMPHENYA(Ezek. 1.1—7.27)Za mpando wa Chauta.

1 Chiv. 19.11 Tsiku lachisanu la mwezi wachinai, chaka cha 30, ndidaakhala pamodzi ndi akapolo a ku Yuda pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Tsono Kumwamba kudatsekuka, ndipo ndidaona maonekedwe a Mulungu m'masomphenya.

22Maf. 24.10-16; 2Mbi. 36.9, 10 Linali tsiku lachisanu la mwezi, chaka chachisanu cha ukapolo wa mfumu Yehoyakini.

3Nthaŵi imeneyo Chauta adandipatsira uthenga ine Ezekiele, wansembe, mwana wa Buzi, m'mphepete mwa mtsinje wa Kebara, m'dziko la Ababiloni. Ndipo ndidamva mphamvu zake zikundifikira.

4Ndiyang'ane, ndidangomva mphepo yamkuntho yochokera kumpoto. Panali mtambo waukulu woŵala m'mphepete mwake monsemu, moto uli laŵilaŵi kuchokera mumtambomo. Pakati pake pa motowo pankaoneka ngati mkuŵa wochezimira.

5Chiv. 4.6 M'katikati mwa motowo ndidaona zinthu zokhala ngati zilengolengo zinai. Maonekedwe ake anali otere: thupili mapangidwe ake onga a munthu,

6koma chilichonse chinali ndi nkhope zinai ndi mapiko anai.

7Miyendo yake inali yoongoka, koma mapazi ake okhala ndi ziboda zonga za mwanawang'ombe. Zibodazo zinkaŵala ngati mkuŵa wonyezimira.

8M'munsi mwa mapiko ake, pa mbali zonse zinai, chilengolengo chilichonse chinali ndi manja a munthu. Zilengolengo zonsezo nkhope zake ndi mapiko ake zidaakhala motere:

9mapiko akewo anali okhudzana. Chilichonse poyenda chinkalunjika kutsogolo ndithu, osatembenuka popitapo.

10 Ezek. 10.14; Chiv. 4.7 Nkhope zake zinkaoneka motere: chilichonse chinali ndi nkhope zinai zosiyana. Kutsogolo nkhope ya munthu, ku dzanja lamanja nkhope ya mkango, ku dzanja lamanzere nkhope ya ng'ombe, ndipo kumbuyo kwake nkhope ya chiwombankhanga.

11Ndimo m'mene zinaliri nkhope zake. Tsono mapiko ake anali otambasuka. Chilengolengo chilichonse chinali ndi mapiko aŵiri okhudzana ndi mapiko a chinzake. Chinalinso ndi mapiko aŵiri ena ophimbira thupi lake.

12Zilengolengozo poyenda zinkalunjika kutsogolo ndithu. Kulikonse kumene mzimu wake unkaziyendetsa, zinkapita kumeneko, osatembenuka popitapo.

13 Chiv. 4.5 Pakati pake pa zilengolengozo panali chinthu chooneka ngati makala oyaka, kapena ngati miyuni yoyaka yomangoyendayenda pakati pake. Motowo unali woŵala zedi, ndipo m'kati mwake munkatuluka mphezi.

14Zilengolengozo zinkathamanga uku ndi uku ngati kung'anipa kwa mphezi.

15 Ezek. 10.9-13 Tsono poyang'ana zilengolengo zija, ndidaona mikombero pansi, mkombero umodzi pambali pa chilengolengo chilichonse.

16Maonekedwe a mikomberoyo anali onga a mwala wonyezimira, ndipo inai yonseyo inali yolingana. Mapangidwe ake anali ngati kuti mikomberoyo idaloŵanaloŵana.

17Tsono poyenda inkatha kupita mbali iliyonse imene zilengolengozo zinkayang'ana, osachita kutembenuka.

18Chiv. 4.8 Mikombero inaiyo inali ndi marimu ataliatali ochititsa mantha. Marimuwo anali ndi maso pozungulira ponse.

19Zilengolengozo zinkati zikamayenda, mikomberoyo inkayendanso m'mbalimu. Zilengolengo zikamakwera m'mwamba, mikomberoyo inkakweranso.

20Kulikonse kumene mzimu wake unkaziyendetsa, zilengolengozo zinkapita kumeneko. Mikombero ija nayonso inkapita nazo pamodzi, chifukwa chakuti mzimu wa zilengolengozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.

21Zilengolengo zinkati zikamayenda, mikombero inkayendanso. Zilengolengo zikaima, mikombero inkaimanso. Zilengolengo zikauluka, mikombero inkauluka nazo pamodzi. Pakuti mzimu wa zilengolengozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.

22 Chiv. 4.6 Pamwamba pa mitu ya zilengolengozo panali chinthu chonga thambo loŵala looneka ngati galasi lochezimira, loyalidwa pamwamba pa mitu yake.

23Zilengolengozo zidaatambalitsa mapiko ake m'munsi mwa thambo lija, mapiko ake ena kumakhudzana, mapiko aŵiri kumaphimbira thupili.

24Chiv. 1.4-15; 19.6 Pamene zinkayenda, ndinkamva phokoso la mapiko ake ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati liwu la Mphambe kapena ngati phokoso la gulu lankhondo. Zikakhala chiimire, zinkagwetsa mapiko ake.

25Tsono pamwamba pa thambo la pa mitu yake padamveka phokoso, zilengolengozo zili chiimire choncho, mapiko akenso ali chigwetsere.

26 Ezek. 10.1; Chiv. 4.2, 3 Pamwamba pa thambo lija panali chinthu china chooneka ngati mpando waufumu, wopangidwa ndi mwala wa safiro. Pamwamba pa mpandowo panali chinthu chooneka ngati munthu.

27Ezek. 8.2 M'mwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo choŵala konsekonse ngati moto. M'munsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokhawo. Kuŵala kwamphamvu kudaamzungulira munthuyo.

28Kuŵalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza m'mitambo tsiku limene kwagwa mvula.

Umu ndi m'mene ulemerero wa Chauta unkaonekera. Ndidangoti ntauwona, ndidadzigwetsa pansi chafufumimba, ndipo ndidamva mau ondilankhula.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help