1Davide atatha kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani udagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani adakonda Davideyo monga momwe ankadzikondera iye mwini.
2Mwakuti adamtenga Davideyo tsiku lomwelo, osamlola kuti abwerere ku banja kwa bambo wake.
3Adachita naye chipangano chifukwa ankamkonda monga momwe ankadzikondera iye mwini.
4Tsono adavula mwinjiro umene anali nawo napatsa Davide pamodzi ndi zovala zankhondo, lupanga lake, uta wake ndi lamba wake.
5Tsono kulikonse kumene Davide ankatumidwa ndi Saulo kuti akamenye nkhondo, ankapambana adani. Motero Saulo adamuika Davide kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo. Chimenechi chidakondwetsa anthu onse, ngakhalenso atsogoleri a ankhondo a Saulo.
Saulo achita nsanje ndi Davide.6Pamene anthu ankabwerera kwao, Davide atapha Mfilisti uja, akazi adatuluka m'mizinda yonse ya Aisraele akuimba ndi kuvina, kuti achingamire mfumu Saulo. Ankaimba ndi kumavina mokondwa, kwinaku ng'oma ndi zitoliro zikugundika.
71Sam. 21.11; 29.5 Akaziwo ankapolokezana akukondwerera namati,
“Saulo wapha zikwi inde,
koma Davide wapha zikwi khumikhumi!”
8Apo Saulo adapsa mtima kwambiri, mau ameneŵa adaipidwa nawo. Adati, “Davide amuŵerengera zikwi zochuluka, koma ine andiŵerengera zikwi zochepa. Nanga chamkhaliranso nchiyani? Si ufumu basi?”
9Motero Saulo ankamuwona ndi diso loipa Davide kuyambira tsiku limenelo.
10M'maŵa mwake mzimu woipa uja udamtsikira Saulo, ndipo adayamba kubwebweta moyaluka m'nyumba mwake. Davide ankamuimbira zeze, monga momwe ankachitira tsiku ndi tsiku. Saulo anali ndi mkondo m'manja mwake.
11Tsono adaponya mkondowo ndipo mumtima mwake adati, “Ndimubaya ndi kumkhomera ku chipupa.” Koma Davide adauleŵa. Zidachitika kaŵiri konse.
12Pambuyo pake Saulo adayamba kuwopa Davide, chifukwa choti tsopano Chauta anali ndi Davide, kumsiya iyeyo.
13Motero Saulo adamtuma Davide kwina kwake, ndipo adamuika kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Davide ankapita namabwera akuŵatsogolera.
14Ndipo ankapambana pa zonse zimene ankachita, chifukwa Chauta anali naye.
15Tsono pamene Saulo adaona kuti Davide akupambana kwambiri, adayamba kuchita naye mantha.
16Koma anthu onse a ku Israele ndi a ku Yuda ankamkonda Davide, chifukwa iyeyu ankaŵatsogolera namapambana pa zonse.
Davide akwatira mwana wa Saulo.17Tsiku lina Saulo adauza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkulu. Ndidzakupatsa kuti akhale mkazi wako. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Chauta.” Potero Saulo ankaganiza kuti, “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisti.”
18Tsono Davide adafunsa Saulo kuti, “Kodi ine ndine yani, ndipo abale anga ndi banja la bambo wanga ndife yani m'dziko la Israele, kuti ine nkukhala mkamwini wa mfumu?”
19Koma pa nthaŵi yoti Merabi, mwana wa Saulo, akwatiwe ndi Davide, bambo wake adampereka kwa Adriyele Mmehola, kuti akhale mkazi wake.
20Komabe Mikala, mwana wina wamkazi wa Saulo, ankakonda Davide. Saulo atamva, adakondwa kwambiri.
21Adaganiza kuti, “Ndimpatse amkwatire, kuti adzakhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo Afilisti adzamupha.” Nchifukwa chake Saulo adauza Davide kachiŵiri kuti, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.”
22Motero adalamula nduna zake kuti, “Mulankhule naye Davide pambali nkumuuza kuti, ‘Mfumu imakukonda, ndipo ngakhale nduna zake zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ”
23Nduna za Saulo zidamuuza Davide mau amenewo. Koma iye adati, “Kani mukuchiyesa chinthu chapafupi kukhala mkamwini wa mfumu? Kodi simukuwona kuti ndine wosauka ndi wosatchuka?”
24Nduna za Saulo zidamuuza zonse zimene Davide adaanena.
25Tsono Saulo adati, “Kamuuzeni kuti, sindikufuna chiwongo cha mtundu uliwonse ai, ndingofuna timakungu ta nsonga za mavalo a Afilisti 100, kuti ndilipsire adani anga.” Potero Saulo ankaganiza zoti Davide aphedwe ndi Afilisti.
26Ndiye nduna za Saulozo zitamuuza Davide mau ameneŵa, zidamkondweretsa kuti akhale mkamwini wa mfumu.
Nthaŵi yoti atenge mkazi wake isanakwane,
27Davide adanyamuka napita pamodzi ndi ankhondo ake, ndipo adakapha Afilisti 200. Adabwera nato timakungu tija natipereka kwa mfumu, kuti choncho akhale mkamwini wake. Apo Saulo adapatsa Davideyo mwana wake Mikala, kuti akhale mkazi wake.
28Koma Saulo atazindikira kuti Chauta ali naye Davide, ndiponso kuti mwana wake Mikala ankamkonda Davideyo,
29adamuwopabe kwambiri ndi kudana naye moyo wake wonse.
30Tsono pamene Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, nthaŵi zonse Davide ankapambana kwambiri kuposa atsogoleri ena onse a ankhondo a Saulo. Choncho dzina lake la Davide lidatchuka kwambiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.