Yak. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Achenjeza achuma

1Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani.

2Mt. 6.19Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu.

3Mphu. 29.10-12Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.

4Deut. 24.14, 15Antchito okolola m'minda mwanu simudaŵalipire. Ndalama zamalipirozo zikulira mokutsutsani. Ndipo kufuula kwa okololawo kwamveka m'makutu a Chauta Mphambe.

5Mwakhala mukuchita maphwando, ndipo mwalidyera dziko lino lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lopha anthu.

6Lun. 2.10-20Mwamuweruza kuti ngwolakwa ndipo mwamupha munthu wolungama, iye osalimbalimba.

Za kuyembekeza mopirira

7Tsono abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m'mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m'munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokololansanu.

8Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera.

9Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo.

10Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m'dzina la Ambuye. Iwo adamva zoŵaŵa, komabe adapirira.

11Yob. 1.21, 22; 2.10; Mas. 103.8 Anthu amene timaŵatchula odala, ndi amene anali olimbika. Mudamva za kulimbika kwa Yobe, ndipo mudaona m'mene Ambuye adamchitira potsiriza, pakuti Ambuye ngachifundo ndi okoma mtima.

12 Mt. 5.34-37 Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula.

Za kupempherera odwala

13Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.

14Mk. 6.13Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye.

15Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.

16Mphu. 4.26Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.

171Maf. 17.1; 18.1; Mphu. 48.2, 3 Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.

181Maf. 18.42-45Atapempheranso, mvula idagwa, nthaka nkuyambanso kumeretsa mbeu zake.

19Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza,

20Miy. 10.12; Tob. 12.9; 1Pet. 4.8dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help