1Pomaliza Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chiŵiri. Pamenepo onse Kumwamba adangoti chete pa hafu la ora.
2Kenaka ndidaona angelo asanu ndi aŵiri aja amene amaimirira pamaso pa Mulungu, akupatsidwa malipenga asanu ndi aŵiri.
3 Amo. 9.1; Eks. 30.1, 3 Mngelo wina adabwera naimirira ku guwa lansembe ali ndi chofukizira chagolide. Adapatsidwa lubani wambiri kuti ampereke pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulungu pa guwa lagolide patsogolo pa mpando wachifumu uja.
4Pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulunguwo, utsi wa lubaniyo udakwera pamaso pa Mulungu kuchokera m'manja mwa mngelo uja.
5Lev. 16.12; Ezek. 10.2; Eks. 19.16; Chiv. 11.19; 16.18Pamenepo mngeloyo adatenga chofukiziracho nachidzaza ndi moto wochokera ku guwa lija. Adachiponya pa dziko lapansi, ndipo nthaŵi yomweyo padachitika mabingu, phokoso, mphezi ndi chivomezi.
Angelo aliza malipenga6 Lun. 11.5—12.2 Tsono angelo asanu ndi aŵiri amene anali ndi malipenga asanu ndi aŵiri aja adakonzeka kuti alize malipengawo.
7 Eks. 9.23-25; Ezek. 38.22 Mngelo woyamba adaliza lipenga lake. Atatero, padadza matalala ndi moto zosanganizika ndi magazi. Zimenezi zidaponyedwa pa dziko lapansi, ndipo chimodzi mwa zigawo zitatu za dziko ndi za mitengo chidapsa. Pamenepo padapsanso udzu wonse wauŵisi.
8Mngelo wachiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero, chinthu chooneka ngati chiphiri choyaka moto chidaponyedwa m'nyanja.
9Pomwepo chimodzi mwa zigawo zitatu za nyanja chidasanduka magazi, ndipo chimodzi mwa zigawo zitatu za zolengedwa zonse zamoyo zam'nyanjamo chidafa. Chimodzinso mwa zigawo zitatu za zombo chidaonongeka.
10 Yes. 14.12 Mngelo wachitatu adaliza lipenga lake. Atatero chinyenyezi choyaka ngati muuni chidagwa kuchokera kuthambo. Chidagwera pa chimodzi mwa zigawo zitatu za mitsinje, ndi pa akasupe.
11Yer. 9.15Chinyenyezicho dzina lake ndi “Kuŵaŵa”. Chimodzi mwa zigawo zitatu za madzi chidasanduka choŵaŵa, mwakuti anthu ambiri adafa nawo madziwo chifukwa cha kuŵaŵa kwakeko.
12 Yes. 13.10; Ezek. 32.7; Yow. 2.10, 31; 3.15 Mngelo wachinai adaliza lipenga lake. Atatero chimodzichimodzi mwa zigawo zitatuzitatu za dzuŵa, za mwezi ndi za nyenyezi chidamenyedwa. Zitachitika zimenezi, chimodzi mwa zigawo zitatu za zonsezo chidada. Panalibenso kuŵala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku.
13Pambuyo pake ndidayang'ana, ndipo ndidaona chiwombankhanga chikuuluka mu mlengalenga, ndipo ndidamva chikulira mokweza kuti, “Tsoka! Tsoka! Tsoka kwa anthu onse okhala pa dziko lapansi, angelo atatu otsala aja akangoliza malipenga ao.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.