1Tsono Tobiti adayamika Mulungu, nati,
“Atamandike Mulungu wamuyaya
chifukwa ufumu wake ndi wosatha.
2Iye amalanga, ndiponso amakhululukira.
Amafikitsa anthu ku dziko la akufa,
komanso amaŵatulutsa ku manda.
Palibe munthu amene angathe kuthaŵa dzanja lake.
3Ana a Israele, tamandani Mulungu,
muyamikeni pamaso pa mitundu ina ya anthu.
Chifukwa ngati adakumwazani
pakati pa anthu a mitundu ina,
4 Yes. 63.16; Yer. 3.4; Lun. 14.3; Mphu. 23.1, 4; Mt. 6.9 kumenekonso adakuwonetsani ukulu wake.
Muyamikeni pamaso pa anthu onse.
Iwowo ndi Ambuye athu,
Iwo ndi Mulungu wathu,
Iwo ndi Atate athu,
ndipo ndi Mulungu mpaka wamuyaya.
5“Angakhale amakulangani
chifukwa cha machimo anu,
adzakuchitirani chifundo nonsenu,
adzakusonkhanitsani
kuchokera ku mitundu yonse ya anthu
kumene adakumwazirani.
6Ngati mutembenukira kwa Iye
ndi mtima wanu wonse ndi nzeru zanu zonse,
pokhala okhulupirika pamaso pake,
ndiye kuti adzabwerera kwa inu
ndipo sadzakufulatiraninso.
Onani zimene adakuchitirani,
muzimuyamika mokweza mau.
Tamandani Ambuye achilungamo,
lemekezani Mfumu ya mibadwo yonse.
“Ine m'dziko la ukapolo lino
ndimayamika Mulungu,
ndimakamba za mphamvu zake zazikulu
kwa mitundu ya anthu ochimwa.
Anthu ochimwanu,
bwererani kwa Iye
ndi kuchita zolungama pamaso pake.
Mwina adzakukomerani mtima
ndi kukuchitirani chifundo.
7Ine ndimayamika Mulungu wanga,
mtima wanga umakondwerera kwambiri
Mfumu yakumwamba.
8Anthu onse azilalika ulemerero wake
ndi kumuimbira nyimbo zomutamanda mu Yerusalemu.
9 Yes. 60.1-22; Chiv. 21.9—22.5 “Iwe Yerusalemu, mzinda woyera,
udalangidwa chifukwa cha zoipa za anthu ako.
Koma anthu olungama adzaŵachitiranso chifundo.
10Uzithokoza Ambuye monga kuyenera,
uzitamanda Mfumu yamuyaya,
ndipo Nyumba ya Mulungu aimangenso mwa iwe,
kuti ukhale ndi chimwemwe.
Mwa iwe Mulungu asangalatsenso onse
amene ali ku ukapolo.
Mwa iwe akonde onse ovutika
pa mibadwo yonse yakutsogolo.
11“Kuŵala kwako kudzaŵala kwambiri
pa maiko onse a m'dziko lino lapansi.
Mitundu yambiri ya anthu idzafika
kuchokera kutali ku mathero onse
a dziko lino lapansi.
Idzatamanda dzina loyera la Ambuye Mulungu
izidzapereka mphatso kwa Mfumu yakumwamba.
Mwa iwe mibadwo yonse idzasangalala,
ndipo dzina la mzinda wosankhidwawe
lidzakumbukika pa mibadwo yonse yakutsogolo.
12“Atembereredwe onse amene adzakunyoza,
onse amene adzakuwononga
ndi kugwetsa makoma ako,
onse amene adzagwetsa nsanja zako
ndi kutentha nyumba zako.
Koma akhale odala nthaŵi zonse
amene adzakumanganso.
13Pamenepo iwe udzakondwa ndi kusangalala,
chifukwa ana ako olungama adzasonkhana pamodzi,
ndipo adzatamanda Ambuye mpaka muyaya.
14“Ngodala anthu amene amakukonda,
amene amakondwerera mtendere wako.
Ngodala amene adakumvera chisoni
pamene unali pa mavuto,
chifukwa adzakondwa nawe
adzasangalala nawe mpaka muyaya.
15Mtima wanga utamande Ambuye
Mfumu yaikulu,
16chifukwa Yerusalemu adzamangidwanso
kuti ukhale mzinda waowao mpaka muyaya.
“Ndidzakondwa ngati mwa anthu anga
adzatsalako ena kuti adzaone ulemerero wako
ndi kuthokoza Mfumu ya Kumwamba.
Zitseko za Yerusalemu adzazipanga
ndi miyala ya safiro ndi ya emeradi,
nsanja zake adzazipanga ndi golide,
malinga akenso adzapangidwa ndi golide weniweni.
17Miseu ya Yerusalemu adzaikonza
ndi miyala ya rubi,
ndiponso miyala ina yamtengowapatali ya ku Ofiri.
M'zipata za ku Yerusalemu adzaimba mosangalala,
ndipo mabanja onse am'menemo adzaimba kuti,
‘Aleluya! Atamandike Mulungu wa Israele.’
Mwa iwe anthu onse adzatamanda dzina loyera
la Mulungu mpaka muyaya.”
Nyimbo yoyamika ya Tobiti idathera pomwepo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.