2 Mbi. 29 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Hezekiya mfumu ya ku Yuda(2 Maf. 18.1-3)

1Hezekiya adamlonga ufumu ali wa zaka 25, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Abiya, mwana wa Zekariya.

2Adachita zolungama pamaso pa Chauta monga momwe ankachitira Davide kholo lake.

Ayeretsa Nyumba ya Chauta

3Pa chaka choyamba cha ufumu wake, pa mwezi woyamba, Hezekiya adatsekula zitseko za Nyumba ya Chauta, nazikonza.

4Adaloŵa ndi ansembe ndi Alevi, naŵasonkhanitsa ku bwalo lakuvuma,

5ndipo adaŵauza kuti, “Mverani inu Alevi. Mudziyeretse, muyeretsenso Nyumba ya Chauta Mulungu wa makolo anu, pakuchotsa zonyansa ku malo opatulika.

6Makolo athu adakhala osakhulupirika ndipo adachita zoipa pamaso pa Chauta, Mulungu wathu. Iwo adasiya Chauta, adaloza nkhongo ku malo a Chauta, ndi kumfulatira.

7Adatsekanso zitseko za khonde la poloŵera, nazima nyale. Sadafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika kwa Mulungu wa Israele.

8Nchifukwa chake Mulungu adaŵapsera mtima anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu. Adaŵasandutsa ochititsa anthu mantha, odabwitsa anthu ndiponso oti anthu aziŵatsonya monga m'mene mukuwoneramu.

9Makolo athu adaphedwa ndi lupanga, ndipo ana athu aamuna, ana athu aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo chifukwa cha zimenezi.

10Tsono ine ndikuganiza kuti ndichite chipangano ndi Chauta, Mulungu wa Israele, kuti mkwiyo wake woopsawo utichoke.

11Ana anga, musachedwe, pakuti Chauta wakusankhani inu kuti muziima pamaso pake ndi kumamtumikira, ndipo kuti mukhale atumiki ake, ndi kumafukiza lubani kwa Iye.”

Alevi ayeretsa Nyumba ya Chauta

12Tsono Alevi amene anali pomwepo ndi aŵa: a m'banja la Kohati: Mahati mwana wa Amasai, ndi Yowele mwana wa Azariya; a m'banja la Merari: Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehalelele; a m'banja la Geresoni: Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa;

13a m'banja la Elizafani: Simiri ndi Yeuwele; a banja la Safu: Zekariya ndi Mataniya;

14a m'banja la Hemani: Yehuwele ndi Simei; a m'banja la Yedutuni: Semaya ndi Uziyele.

15Iwowo adasonkhanitsa abale ao, ndipo adadziyeretsa, naloŵa m'Nyumba ya Chauta kuti aiyeretse monga momwe mfumu idaalamulira, potsata mau a Chauta.

16Ansembe ndiwo amene adaaloŵa m'katikati mwa Nyumba ya Mulungu kuti akayeretsemo. Adatulutsa zinthu zonse zonyansa zimene adazipeza m'Nyumbamo, m'bwalo la Nyumbayo. Alevi adazitenga zimenezo, nakazitaya ku mtsinje wa Kidroni.

17Adayamba mwambo wa kuyeretsa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo, mpamene adafika m'khonde la poloŵera m'Nyumba ya Chauta. Tsono adachita mwambo wa kuyeretsa Nyumba ya Chauta ija pa masiku asanu ndi atatu, ndipo adaimaliza pa tsiku la 16 la mwezi woyambawo.

Apereka Nyumba ya Chauta

18Atatha, adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza kuti, “Tayeretsa Nyumba yonse ya Chauta ija, guwa la nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndiponso tebulo la buledi wopereka pamaso pa Chauta, pamodzi ndi zipangizo zake zonse.

19Zipangizo zonse zimene mfumu Ahazi adaazichotsa pamene anali mfumu yosakhulupirika, tazibwezera, ndipo taziyeretsa. Taziika ku guwa la Chauta.”

Hezekiya akonzanso chipembedzo

20Pambuyo pake mfumu Hezekiya adanyamuka m'mamaŵa, nasonkhanitsa akuluakulu amumzindamo, ndipo adakwera ku Nyumba ya Chauta.

21Adabwera ndi ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndiponso atonde asanu ndi aŵiri kuti aperekere nsembe yopepesera uchimo, kuperekera banja la mfumu, Nyumba ya Chauta ndi Yuda. Ndipo iyeyo adalamula ansembe, ana a Aaroni, kuti azipereke pa guwa la Chauta.

22Choncho anthuwo adapha ng'ombe zamphongo zija ndipo ansembe adatenga magazi, nawaza pa guwa. Adaphanso nkhosa zamphongo zija, nawaza magazi ake pa guwa.

23Tsono atonde operekera nsembe yopepesera uchimo aja, adabwera nawo kwa mfumu ndi kwa msonkhano wonse. Ndipo adasanjika manja ao pa atondewo.

24Kenaka ansembe adazipha, napereka magazi ake pa guwa, kuti akhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraele onse, pakuti mfumu idaalamula kuti nsembe yopsereza ndi nsembe zopepesera uchimo zichitike chifukwa cha Aisraele onse.

25Tsono adaika Alevi kuti azikhala ku Nyumba ya Chauta ndi kumaimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, potsata lamulo la Davide ndi la Gadi mneneri wa mfumu, ndiponso la Natani mneneri. Pakuti lamulo limenelo nlochokera kwa Chauta kudzera mwa aneneri ake.

26Alevi adaimirira atatenga zipangizo zoimbira zonga za Davide, ndipo ansembe adatenga malipenga.

27Pamenepo Hezekiya adalamula kuti nsembe yopsereza iperekedwe pa guwa. Atayamba kupereka nsembe yopsereza, adayambanso kuimbira nyimbo Chauta. Ndipo adaliza malipenga ndi zipangizo zoimbira za Davide mfumu ya Israele.

28Msonkhano wonse udagwada moŵeramitsa mitu pansi, anthu oimba nyimbo akuimba, ndipo oliza malipenga akuliza. Adakhala akuchita zimenezi mpaka nsembe yopsereza idatha.

29Atatha kupereka nsembe, mfumu pamodzi ndi anthu onse amene anali nawo adagwada naŵeramitsa mitu pansi.

30Kenaka mfumu Hezekiya, pamodzi ndi nduna zake, adalamula Alevi kuti aimbe nyimbo zotamanda Chauta potsata mau a Davide ndi a mneneri Asafu. Pomwepo adaimba mosangalala nyimbo zotamanda, ndipo adagwada naŵeramitsa mitu pansi.

31Pamenepo Hezekiya adati, “Tsopano inu mwadzipereka kuti mugwire ntchito ya Chauta. Idzani pafupi, mubwere nazo nsembe ndi zopereka zothokozera ku Nyumba ya Chauta.” Msonkhanowo udabwera nazo nsembe ndi zopereka zothokozera. Anthu onse amene anali ndi mtima waufulu adabwera ndi nsembe zopsereza.

32Chiŵerengero cha nsembe zopsereza zimene msonkhano udabwera nazo ndi ichi: ng'ombe zamphongo 70, nkhosa zamphongo 100, ndi anaankhosa 200. Zonsezi adazipereka ngati nsembe yopsereza kwa Chauta.

33Tsono nsembe zina zopereka zinali izi: ng'ombe zamphongo 600 ndi nkhosa 300.

34Koma ansembe anali pang'ono, choncho sadathe kusenda nsembe zonse zopserezazo. Motero poyembekeza kuti ansembe onse adziyeretse, Alevi adaŵathandiza mpaka ntchito yonseyo idatha. Aleviwo adaachita changu kupambana ansembe pakudziyeretsa kwao.

35Kuwonjezera pa chiŵerengero cha nsembe zopsereza, panalinso mafuta a nsembe zamtendere, ndiponso zakumwa za pa nsembe zopsereza. Motero miyambo yonse ya ku Nyumba ya Chauta idakhazikikanso.

36Choncho Hezekiya ndi anthu onse aja adakondwa chifukwa cha zimene Mulungu adaŵachitira, pakuti zimenezo zidaachitika mwadzidzidzi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help