1Woipa mtima amangodzithaŵira
popanda wina wompirikitsa,
koma wochita zabwino amalimba mtima ngati mkango.
2Eni dziko akachita zaupandu, oŵalamulira amachuluka.
Koma anthu akakhala omvetsa ndi odziŵa zinthu,
dzikolo limakhazikika nthaŵi yaitali.
3Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake,
ali ngati mvula yamkuntho
yosasiya konse chakudya m'minda.
4Amene samvera malamulo amatamanda anthu oipa mtima,
koma otsata malamulo amatsutsana nawo.
5Anthu oipa samvetsa kuti chilungamo nchiyani,
koma amene amatsata kufuna kwa Chauta
amachimvetsa kwathunthu.
6Munthu wosauka amene amayenda mwaungwiro
amaposa kwambiri munthu wolemera amene ali wonyenga.
7Amene amatsata malamulo ndiye mwana wanzeru,
koma amene amayenda ndi anthu adyera,
amachititsa atate ake manyazi.
8Amene amachulukitsa chuma chake
polandira chiwongoladzanja ndi pochikundika,
chumacho amachikundikira ena amene
adzachitira chifundo anthu osauka.
9Wina akamakana kumvera malamulo,
ngakhale mapemphero ake amanyansira Mulungu.
10Amene amasokeza anthu olungama
kuti azitsata njira yoipa, adzagwa m'dzenje lake lomwe.
Koma anthu amene alibe cholakwa
adzalandira choloŵa chabwino.
11Munthu wolemera amadziyesa wanzeru,
koma munthu wosauka amene ali womvetsa zinthu,
amamtulukira.
12Anthu abwino akapambana,
pamakhala chikondwerero chachikulu,
koma oipa mtima akalandira ulamuliro, anthu amabisala.
13Wobisa machimo ake sadzaona mwai,
koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.
14Ndi wodala munthu amene amaopa Chauta nthaŵi zonse,
koma woumitsa mtima wake adzagwa m'tsoka.
15Monga muja umakhalira mkango wobangula
kapena chimbalangondo cholusa,
ndimonso imakhalira mfumu yoipa mtima kwa anthu osauka.
16Wolamulira amene samvetsa zinthu
amapondereza anthu mwankhanza,
koma wodana ndi phindu loipa amatalikitsa masiku ake.
17Munthu amene wapalamula mlandu wopha mnzake,
akhale womathaŵathaŵa mpaka kufa kwake.
Wina aliyense asamthandize.
18Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa,
koma woyenda mokhotakhota adzagwa m'dzenje.
19Wolima m'munda mwake adzakhala ndi chakudya chambiri,
koma wonka nafuna zopanda pake adzasauka kwambiri.
20Munthu wokhulupirika adzakhala ndi madalitso ambiri,
koma wofunitsitsa kulemera msanga
sadzalephera kupeza chilango.
21Kuchita tsankho si kwabwino,
komabe ena amaweruza mokondera
chifukwa cha kachidutswa ka buledi.
22Munthu wakaliwumira amafunitsitsa kulemera mofulumira,
koma sadziŵa kuti umphaŵi udzamgwera.
23Amene amadzudzula mnzake,
potsiriza pake mnzakeyo adzamkonda kwambiri
kupambana amene ali ndi mau oshashalika.
24Wobera atate ake kapena amai ake
namanena kuti kutero sikulakwa,
ameneyo ndi mnzake wa munthu woononga.
25Munthu waumbombo amautsa mkangano,
koma wokhulupirira Chauta adzalemera.
26Samvazaanzake nchitsiru,
koma wotsata nzeru za ena adzapulumuka.
27Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu
koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye,
adzatembereredwa kwambiri.
28Anthu oipa mtima akalandira ulamuliro,
anthu amabisala,
koma oipawo akaonongeka,
anthu ochita chilungamo amapeza bwino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.