1Pambuyo pake khamu lonse la Aisraele lidayamba ulendo kuchokera ku Elimu, ndipo pa tsiku la 15 la mwezi wachiŵiri atachoka ku Ejipito, adafika ku chipululu cha Sini, chimene chili pakati pa Elimu ndi Sinai.
2Ndipo khamu lonse lidadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu muja kuti,
3“Kukadakhala bwino Chauta akadatiphera ku Ejipito konkuja, kumene tinkakhala tikudya nyama ndi buledi, ndipo tinkakhuta. Koma inu mwatifikitsa kuchipululu kuno kuti mutiphe tonse ndi njala.”
4 Lun. 16.20-29; Yoh. 6.31 Apo Chauta adauza Mose kuti, “Chabwino, ndikupatsani chakudya chimene chidzagwa ngati mvula kuchokera kumwamba. Anthu azituluka tsiku ndi tsiku kukatola chakudya chokwanira tsiku limodzi, kuti ndiŵayese ndipo ndiwone ngati adzayenda motsata malamulo anga kapena ai.
5Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pokonza chimene adatola adzapeza kuti nchokwanira masiku aŵiri.”
6Tsono Mose ndi Aroni adauza Aisraele onse kuti, “Madzulo omwe ano mudzadziŵa kuti ndi Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito,
7m'maŵa mwake mudzaona ulemerero wa Chauta. Wamva madandaulo anu omuŵiringulira aja. Kodi ife ndife yani, kuti inu muzitiŵiringulira?”
8Ndipo Mose adati, “Ndi Chauta amene adzakupatsani madzulo nyama yoti mudye, ndi m'maŵa buledi woti nkukhuta, chifukwa choti wamva madandaulo anu onse omuŵiringulira aja. Ife ndife yani? Madandaulo anu simudaŵiringulire ife ai, koma Chauta.”
9Pamenepo Mose adauza Aroni kuti akauze anthuwo kuti, “Bwerani, mudzaime pamaso pa Chauta chifukwa wamva madandaulo anu onse.”
10Tsono Aroni akulankhula ndi khamu lonse lija, khamulo lidatembenuka kupenya ku chipululu, ndipo ulemerero wa Chauta udaoneka mu mtambo mwadzidzidzi.
11Chauta adauza Mose kuti,
12“Ndamva madandaulo a Aisraele. Ndiye uŵauze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama, ndipo m'maŵa mudzadya buledi, choncho mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ ”
13Motero madzulo kudagwa zinziri, ndipo zidadzaza ponseponse pamahemapo. M'maŵa ndithu padagwa mame ponse pozungulira mahemawo.
14Mamewo atangokamuka, panthakapo m'chipululu muja padapezeka tinthu tina topyapyala, tambee ngati chipale, ndiponso tonyata.
151Ako. 10.3Aisraele ataona tinthuto sadatidziŵe kuti nchiyani, mwakuti adayamba kufunsana kuti “Kodi timeneti ntiyani?” Mose adaŵauza kuti, “Ameneyu ndi buledi yemwe Chauta wakupatsani kuti mudye.
16Chauta walamula kuti aliyense mwa inu atole womukwanira kudya, ndiye kuti malita aŵiri pa munthu mmodzi, malinga ndi chiŵerengero cha anthu onse a m'hema mwake.”
17Aisraele adachitadi zimenezo. Ena adatola tambiri, koma ena pang'ono.
182Ako. 8.15 Tsono atayesa ndi muyeso wa malita aŵiri, adaona kuti amene adaatola tambiri, sitidaŵatsalireko, amene adaatola pang'ono, sitidaŵathere. Aliyense adangotola tokwanira.
19Pamenepo Mose adaŵauza kuti, “Munthu aliyense asasungeko mpaka m'maŵa.”
20Komabe ena mwa iwowo sadamvere zimene adaanena Mosezo, adasungako mpaka m'maŵa mwake. Koma kutacha, adaona kuti tonseto tagwa mphutsi, ndipo tikununkha. Apo Mose adaŵapsera mtima anthuwo.
21Ankatola m'maŵa mulimonse, ndipo aliyense ankatola monga m'mene ankasoŵera. Koma dzuŵa likatentha, tinthuto tinkasungunuka.
22Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi ankatola chakudya cha masiku aŵiri, chokwanira malita anai ndi theka pa munthu mmodzi. Ndipo atsogoleri onse a Aisraele adabwera kwa Mose kudzamuuza zimenezo.
23Eks. 20.8-11 Tsono Mose adaŵauza kuti, “Chauta walamula kuti, ‘Maŵa ndi tsiku lopumula, tsiku la Sabata, loperekedwa kwa Chauta. Wotchani yense amene mufuna kuwotcha, ndipo muphike yense amene mufuna kuphika. Wotsalako mumsunge padera mpaka maŵa.’ ”
24Mose atalamula zimenezi, anthuwo adasungadi totsalato mpaka m'maŵa mwake tosaonongeka, ndipo sitidagwe mphutsi.
25Pambuyo pake Mose adauza anthuwo kuti, “Idyani ameneyu lero, chifukwa lero ndi tsiku la Sabata loperekedwa kwa Chauta. Lero simumpezatu kunjaku.
26Mutole chakudya pa masiku asanu ndi limodzi. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku la Sabata, chakudyacho sichidzapezeka.”
27Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo anthu ena adaapita kuti akatole chakudya, koma sadachipeze.
28Pamenepo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi mudzakhalabe osamvera mau anga ndi malamulo anga mpaka liti?
29Kumbukirani kuti ndine Chauta, amene ndidakupatsani tsiku la Sabata. Tsono chifukwa cha chimenechi ndimakupatsani chakudya chokwanira masiku aŵiri pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Aliyense azingokhala komwe aliriko pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Asachoke ndi mmodzi yemwe pakhomo pake.”
30Motero anthu sankagwira ntchito pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.
31 Num. 11.7, 8 Aisraele chakudyacho adachitcha mana. Maonekedwe ake anali onga njere zamapira, ndiponso oyera. Pakudya, ankazuna ngati buledi wopangidwa ndi uchi.
32Tsono Mose adati, “Chauta walamula kuti ‘Musungeko mana ena kuti zidzukulu zanu zidzaone chakudya chimene ndidakupatsani m'chipululu, nditakutulutsani ku Ejipito kuja.’ ”
33Ahe. 9.4 Ndipo Mose adauza Aroni kuti, “Tenga mtsuko, uikemo mana wokwana malita aŵiri. Utatero uike pamaso pa Chauta kuti manayo asungike chifukwa cha zidzukulu zanu.”
34Monga momwe Chauta adalamulira Mose, Aroni adaika mtsukowo patsogolo pa bokosi lachipangano, kuti manayo asungike.
35Yos. 5.12 Aisraelewo adakhala alikudya mana zaka makumi anai, mpaka adakafika kudziko kokhala anthu. Adadya mana mpaka adafika ku malire a dziko la Kanani.
36Malita aŵiri alingana ndi gawo lachikhumi la efa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.