1Tsiku lina Yonatani, mwana wa Saulo, adauza mnyamata womnyamulira zida zake zankhondo kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka Afilisti tsidya ilo.” Koma sadauze bambo wake.
2Saulo ankakhala m'malire a Gibea patsinde pa mtengo wa makangaza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600 pamodzi.
3Panalinso Ahiya, wansembe amene ankavala efodi. Iyeyo anali mwana wa Ahitubi, mbale wa Ikabodi mwana wa Finehasi. Finehasiyo anali mwana wa Eli, wansembe wa Chauta ku Silo. Tsono anthu sankadziŵa kuti Yonatani wachokapo.
4Pampata pamene Yonatani ankafuna kudzerapo kuti akafike ku kaboma kankhondo kaja, panali thanthwe lotsetsereka mbali ina, ndi lina lotsetsereka mbali inanso. Dzina la thanthwe lina ankati Bozezi, ndipo linalo ankati Sene.
5Thanthwe lina linali kumpoto kuyang'anana ndi Mikimasi, ndipo linalo linali kumwera kuyang'anana ndi Geba.
6Yonatani adauza mnyamata wake uja kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka anthu osaumbalidwaŵa. Mwina mwake Chauta atigwirira ntchito. Pakuti palibe chomletsa Chauta kutipambanitsa ngakhale tikhale ochepa chotani.”
7Mnyamata wakeyo adati, “Muchite zonse monga momwe mtima wanu ufunira. Ine ndili nanu, ndipo monga momwe mukuganizira inu, ine mmomwemonso.”
8Tsono Yonatani adati, “Tiwolokere kwa anthuwo, ndipo tikadziwonetse kwa iwo.
9Akatiwuza kuti, ‘Dikirani mpaka tikupezeni,’ tikangoima pamalo pathu, osapita kwa iwowo.
10Koma akanena kuti, ‘Bwerani kuno,’ ife tikapitadi, pakuti Chauta waapereka anthuwo m'manja mwathu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa ife.”
11Choncho aŵiriwo adadziwonetsa ku kaboma kankhondo ka Afilisti. Tsono Afilisti adati, “Taonani Ahebri akutuluka m'maenje m'mene ankabisala.”
12Ndipo anthu akukabomawo adafuulira Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Tabwerani kuno, muwona!” Apo Yonatani adauza mnyamata wakeyo kuti, “Unditsate, Chauta wapereka anthuŵa m'manja mwa Aisraele.”
13Choncho Yonatani adakwera chokwaŵa, mnyamata wake uja akumtsata pambuyo. Tsono Yonatani adaŵathira nkhondo Afilistiwo ndi kumaŵagwetsa, mnyamata wake uja nkumaŵapha pambuyo pa iyeyo.
14Anthu amene Yonatani ndi mnyamata wake uja adapha nthaŵi yoyamba analipo ngati makumi aŵiri, ndipo adaŵaphera pa malo ochepa okwanira ngati theka la ekala.
15Tsono Afilisti onse m'dzikomo adasokonezeka ndi mantha aakulu. Ankhondo a ku kaboma kankhondo kaja ndi anzao enanso ankanjenjemera kwambiri. Kudachita chivomezi ndipo kugwedezeka kwa dziko kudakulitsa mantha a Afilisti aja.
Kugonjetsedwa kwa Afilisti.16Alonda a Saulo a ku Gibea ku dziko la Benjamini poti ayang'ane, adangoona chigulu cha adani chikumwazikira uku ndi uku.
17Tsono Saulo adauza anthu amene anali naye aja kuti, “Ŵerengani anthu, ndipo muwone amene achokapo.” Ataŵaŵerenga, adaona kuti Yonatani ndi mnyamata womnyamulira zida uja palibe.
18Apo Saulo adauza Ahiya kuti, “Bwera nayo kuno efodiyo.” Nthaŵi imeneyo efodiyo inali ndi Ahiya pamaso pa Aisraele.
19Pamene Saulo ankalankhula ndi wansembeyo, phokoso linkakulirakulira ku zithando za Afilisti. Tsono Saulo adauza wansembe uja kuti, “Leka, usaombeze!”
20Pamenepo Saulo pamodzi ndi anthu amene anali naye adasonkhananso napita kukamenya nkhondo, ndipo adaona Afilisti akungophana okhaokha. Motero kunali chisokonezo chachikulu kwambiri.
21Ahebri ena amene kale adaali pamodzi ndi Afilistiwo, ndipo anali atapita nao ku zithandozo, iwonso adatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraele a mbali ya Saulo ndi Yonatani.
22Chimodzimodzinso Aisraele amene adaabisala m'dziko lamapiri la Efuremu, atamva kuti Afilisti akuthaŵa, nawonso adaŵathamangira Afilistiwo naŵathira nkhondo.
23Ndipo nkhondoyo idapitirira mpaka kubzola mzinda wa Betaveni. Umu ndimo m'mene Chauta adapulumutsira Aisraele tsiku limenelo.
Yonatani aphwanya lamulo la Saulo24Koma ankhondo a Aisraele adavutika tsiku limene lija, pakuti Saulo adaŵaopseza pakunena kuti, “Atembereredwe amene adye kanthu kusanade, ndisanalipsire adani anga.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe amene adalaŵa chakudya.
25Tsono onse adaloŵa m'nkhalango ina m'mene munali uchi.
26Ataloŵa m'nkhalangomo, adangoona uchi ukukha pansi, koma panalibe amene adatengako kuika pakamwa, poti ankaopa temberero lija.
27Koma Yonatani anali asanamve za temberero la bambo wake lija. Choncho adatosa chisa cha njuchi ndi nsonga ya ndodo imene inali m'manja mwake, naika uchi wake pakamwa naadya. Atatero m'maso mwake mudachita kuti ngwee.
28Tsono mmodzi mwa anthuwo adati, “Bambo wanu waopseza anthu pakunena kuti, ‘Atembereredwe amene adye kanthu lero.’ Nchifukwa chake anthuŵa akuchita ngati akomoke ndi njala.”
29Tsono Yonatani adati, “Bambo wanga wavutitsa anthu onse. Taonani ine m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndalaŵako uchiwu.
30Kukadakhala bwino kwambiri, anthu akadadya mwaufulu lero zofunkha zimene adazipeza kwa adani ao. Zidakatero bwenzi tsopano lino titapha Afilisti ambiri.”
31Tsikulo Aisraele adapha Afilisti kuyambira ku Mikimasi mpaka ku Ayaloni. Koma Aisraelewo anali pafupi kukomoka nayo njala.
32Motero adathamangira pa zofunkha, ndipo adatenga nkhosa, ng'ombe ndi makonyani, nazipha. Ndipo adazidya pamodzi ndi magazi omwe.
33Gen. 9.4; Lev. 7.26, 27; 17.10-14; 19.26; Deut. 12.16, 23; 15.23 Koma ena adauza Saulo kuti, “Onani, anthu akuchimwira Chauta podyera kumodzi ndi magazi.” Saulo adati, “Mwaukira Chauta lero! Pezani mwala waukulu muukunkhunizire kuno.”
34Ndipo adatinso, “Mwazikanani pakati pa anthu, muŵauze kuti, ‘Aliyense abwere ndi ng'ombe yake, kapena nkhosa yake, aziphere pompano, kenaka adye. Ndipo musachimwire Chauta podyera kumodzi ndi magazi.’ ” Motero aliyense mwa anthuwo adabwera ndi ng'ombe yake usiku umenewo, naiphera komweko.
35Tsono Saulo adamangira Chauta guwa. Limeneli linali guwa loyamba limene Sauloyo adamangira Chauta.
Tchimo la Yonatani liwululuka, koma anthu ampulumutsa.36Pamenepo Saulo adati, “Tiyeni tipite usiku, tilondole Afilisti, ndipo tilande zinthu zao mpaka m'maŵa kutacha. Tisasiyepo ndi mmodzi yemwe mwa iwo.” Anthuwo adati, “Chitani chilichonse chimene chikukukomerani.” Koma wansembe adati, “Tiyeni tiyambe tapempha nzeru kwa Mulungu.”
37Tsono Saulo adafunsa Mulungu kuti, “Kodi tiŵalondole Afilistiŵa? Kodi muŵapereka m'manja mwathu?” Koma Mulungu sadamuyankhe kanthu tsiku limenelo.
38Apo Saulo adati, “Bwerani kuno nonse atsogoleri a anthu. Tiwone ndi tchimo lanji lachitika lero.
39Pali Chauta, Mpulumutsi wa Aisraele, wochimwayo ngakhale akhale mwana wanga Yonatani, afe ndithu.” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pakati pa anthu onsewo amene adamuyankha.
40Tsono adauza Aisraelewo kuti, “Inu mukhale mbali imodzi, ine ndi mwana wanga Yonatani tikhalanso mbali ina.” Anthuwo adauza Saulo kuti, “Muchite zimene zikukomereni.”
41Num. 27.21; 1Sam. 28.6 Nchifukwa chake Saulo adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani simudandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati wolakwa ndineyo kapena mwana wanga Yonatani, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, aoneke ndi Urimu. Koma tchimolo likakhala la Aisraele, aoneke ndi Tumimu.” Maere adagwera Yonatani ndi Saulo, anthu nkupulumuka.
42Tsono Saulo adati, “Chitani maere pakati pa ine ndi mwana wanga Yonatani.” Ndipo maere adagwera Yonatani.
43Apo Saulo adauza Yonatani kuti, “Tandiwuza zimene wachita.” Yonatani adauza bambo wakeyo kuti, “Ndidalaŵako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo yanga. Ndiye ai, chomwecho, ine ndili wokonzeka kuti ndife.”
44Apo Saulo adati, “Mulungu andilange ine, ngakhale kundipha kumene, ngati suufa iwe Yonatani.”
45Tsono anthu adafunsa Saulo kuti, “Kodi afe Yonatani amene wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele kunkhondo? Sizingatheke mpang'ono pomwe. Pali Chauta wamoyo! Tsitsi nlimodzi lomwe la kumutu kwake silipezeka lothothoka. Zimene wachita lerozi, wamthandiza ndi Mulungu.” Motero anthu adamupulumutsa Yonatani, ndipo sadaphedwe.
46Pambuyo pake Saulo adaleka kuŵathamangira Afilisti, ndipo Afilistiwo adabwerera kwao.
Za ulamuliro wa Saulo ndi banja lake.47Pamene Saulo adakhala mfumu yolamulira Aisraele, adamenyana nkhondo ndi adani ake onse omzungulira. Adamenyana ndi Amowabu, Aamoni, Aedomu, mafumu a ku Zoba ndiponso Afilisti. Kulikonse kumene ankapita, ankaŵagonjetsa.
48Adachita zamphamvu, ndipo adagonjetsa Aamaleke. Motero adapulumutsa Aisraele kwa anthu amene ankaŵalanda zinthu zao.
49Ana aamuna a Saulo anali Yonatani, Isivi ndi Malikisuwa. Analinso ndi ana aŵiri aakazi, wamkulu anali Merabi, wamng'ono anali Mikala.
50Mkazi wa Saulo anali Ahinowamu mwana wa Ahimaazi. Ndipo mkulu wa ankhondo a Saulo anali Abinere, mwana wa Nere, mbale wa bambo wa Saulo.
51Kisi bambo wa Saulo ndipo Nere bambo wa Abinere, anali ana a Abiyele.
52Pa moyo wake wonse Saulo ankakhalira kuchita nkhondo ndi Afilisti. Tsono ankati akaona munthu wamphamvu kapena wolimba mtima, ankamulemba m'gulu lake lankhondo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.