Ezek. 32 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumu ya ku Ejipito aifanizira ndi ng'ona

1Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiŵiri, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, imbira Farao, mfumu ya ku Ejipito, nyimbo yamaliro. Umuuze uthenga uwu wakuti:

“Iwe umadziyesa mkango pakati pa mitundu ya anthu,

koma uli ngati ng'ona.

Umakhuvula m'mitsinje yako.

Umavonongera madzi ndi mapazi ako,

ndi kudetserera mitsinje.

3Ine Ambuye Chauta ndikuti,

Ndikadzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yambiri,

ndidzakuponyera khoka

ndipo iwowo adzakugwira m'kombe mwanga.

4Ndidzakuponya ku mtunda ndi kukutaya pansi.

Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga

kuti zidzatere pa iwe,

ndiponso zilombo za m'dziko lonse

kuti zidzakudye.

5Nyama yako ndidzaiyanika pa mapiri,

ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsala zako.

6Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,

mpaka ku mapiri komwe,

ndipo mitsinje idzadzaza ndi nyama yako.

7 Yes. 13.10; Mt. 24.29; Mk. 13.24, 25; Lk. 21.25; Chiv. 6.12, 13; 8.12 Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba thambo,

ndipo ndidzadetsa nyenyezi.

Ndidzaphimba dzuŵa ndi mtambo,

ndipo mwezi sudzaŵala.

8Ndidzazimitsa zoŵala zonse zamumlengalenga,

ndipo dziko lako ndidzalichititsa mdima.

Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

9“Ndidzavutitsa mitima ya anthu a mitundu yambiri, pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ina, ku maiko amene sudaŵadziŵe.

10Ndidzadabwitsa anthu ambiri ndi zimene zidzakugwere. Mafumu ao adzanjenjemera pokumbukira iwe, nditaŵaonetsa lupanga langa. Pa tsiku la kugwa kwako, aliyense adzadera nkhaŵa moyo wake.

11“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni idzakufika.

12Ndidzagwetsa gulu lako lonse lankhondo ndi malupanga a asilikali oopsa kwambiri kupambana a mitundu ina yonse.

“Adzathetsa kunyada kwa Ejipito,

ndipo gulu lake lonse lankhondo lidzaonongeka.

13Ndidzaononga ziŵeto zao zonse

zokhala pambali pa madzi am'dzikomo.

Kumadziko sikudzaonekanso phazi la munthu,

ndipo phazi la nyama silidzavonongeranso madzi.

14Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi akumeneko,

ndipo mitsinje idzayenda mokometsera ngati mafuta.

Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

15Ejipito nditamsandutsa bwinja,

ndipo dziko lonse nditaliwononga,

nditapha onse okhala kumeneko,

adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

16“Mau angaŵa adzakhala nyimbo yamaliro, ndipo akazi a mitundu yachilendo adzaiimba, kuimbira Ejipito ndi gulu lake lonse lankhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Dziko la anthu akufa

17Pa tsiku la khumi ndi chisanu la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

18“Iwe mwana wa munthu, lira kwambiri chifukwa cha anthu ochuluka a ku Ejipito, ndipo uŵaloŵetse, pamodzi ndi anthu a m'maiko ena amphamvu, ku dziko la anthu akufa.

19Uŵafunse kuti, ‘Kani ndinu okongola kupambana ena? Tsikirani ku manda pamodzi ndi ena onse osaumbalidwa.’

20Aejipito adzagwa pakati pa anthu amene adaphedwa pa nkhondo. Lupanga nlosololasolola, iwowo adzaphedwa pamodzi ndi anthu ao ochuluka.

21M'kati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana kuti, ‘Kani anthu osaumbalidwa aja, ophedwa pa nkhondo, afika kunsi kuno. Si aŵa agona apaŵa!’

22“Komweko kuli Asiriya ndipo ankhondo ake onse ali m'manda omzungulira. Onsewo adaphedwa pa nkhondo.

23Manda ao ali m'malo ozama kwambiri m'dziko la anthu akufa, ndipo manda ao adazungulira manda ake. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, koma tsopano onsewo adafa, adaphedwa pa nkhondo.

24“Komweko kulinso Elamu ndipo ankhondo ake onse ali m'manda omzungulira. Onsewo adaphedwa pa nkhondo. Anthuwo adatsikira ku manda ali osaumbalidwa. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo. Tsopano akuchita manyazi, pamodzi ndi amene ali m'manda.

25Elamuyo amupangira malo ogonapo pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo, loikidwa momzungulira. Onsewo ndi osaumbalidwa, ophedwa pa nkhondo. Zoonadi, anthu amene kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali m'dziko la anthu akufa. Aikidwa pakati pa anthu ophedwa.

26“Komwekonso kuli Meseki ndi Tubala. Ankhondo ao onse ali m'manda oŵazungulira. Anthuwo ndi osaumbalidwa, ndipo adaphedwa pa nkhondo. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo.

27Sadaikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zao zomwe zankhondo. Malupanga ao adaŵaika ku mitu yao, ndipo zishango zao adaphimbira mafupa ao. Kale anthu amphamvu ameneŵa ankaopsa m'dziko la anthu amoyo.

28“Iwenso Farao, udzatswanyika ndipo udzagona pamodzi ndi anthu akufa osaumbalidwa, pamodzi ndi amene adaphedwa pa nkhondo.

29Komweko kuli Edomu pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, komabe adaikidwa m'manda. Akugona pamodzi ndi anthu osaumbalidwa, pamodzi ndi onse amene adatsikira ku dziko la anthu akufa.

30“Komweko kulinso akalonga onse akumpoto, pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi, pamodzi ndi ophedwa, ngakhale anali oopsa ndi mphamvu zao. Akugona osaumbalidwa pamodzi ndi ophedwa pa nkhondo. Kumeneko akuchita manyazi pamodzi ndi onse amene adatsikira kale ku dziko la anthu akufa.

31“Farao akadzaona onseŵa, iye ndi magulu ake ankhondo adzathuza mtima pokumbukira kuchuluka kwa anthu ake amene adaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

32Ndithudi ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, koma iyeyo ndi magulu ake onse ankhondo adzaikidwa pamodzi ndi osaumbalidwa, pamodzi ndi onse ophedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help