1Mose adaitana Aisraele onse naŵauza kuti, “Chauta akukulamulani kuti,
2Eks. 20.8-11; 23.12; 31.15; 34.21; Lev. 23.3; Deut. 5.12-14 Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri, lidzakhala la Sabata, tsiku lanu lopumula, loperekedwa kwa Chauta. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo, adzaphedwa.
3Pa tsiku la Sabata limenelo, musamasonkha ndi moto womwe m'nyumba mwanu.”
Za zopereka za ku malo opatulika(Eks. 25.1-9)4Mose adauza Aisraele onse aja kuti, “Chauta akukulamulani kuti,
5‘Muzipereka zopereka kwa Chauta. Tsono aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka, azibwera ndi zopereka izi: golide, siliva, mkuŵa,
6thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira. Azibweranso ndi nsalu yokoma yabafuta, nsalu zopangidwa ndi ubweya wambuzi,
7chikopa chankhosa chonyika mu utoto wofiira, zikopa zambuzi, matabwa a mtengo wa kasiya,
8mafuta anyale, zonunkhira zopangira mafuta odzozera, ndiponso zopangira lubani wonunkhira bwino,
9miyala ya mtundu wa onikisi ndi ina yokoma yoika pa chovala chaunsembe cha efodi ndiponso pa chovala chapachifuwa.’ ”
Zipangizo za m'chihema chamapemphero(Eks. 39.32-43)10“Anthu onse aluso pakati panupa abwere, ndipo apange zonse zimene Chauta adalamula.
11Apange chihema cha Chauta, hema lake pamodzi ndi chophimbira chake, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake pamodzi ndi masinde ake omwe.
12Apangenso bokosi lachipangano ndi mphiko zake, chivundikiro chake cha bokosilo ndi nsalu zotchinga bokosilo;
13tebulo, pamodzi ndi mphiko zake ndi zipangizo zake, ndiponso buledi woperekedwa kosalekeza kwa Mulungu;
14choikaponyale ndi zipangizo zake, nyale zake ndi mafuta a nyalezo;
15guwa lofukizirapo lubani ndi mphiko zake, mafuta odzozera, lubani wa fungo lonunkhira bwino, ndiponso nsalu zochingira za pa chipata cha chihema cha Chauta.
16Apangenso guwa la zopereka zopsereza pamodzi ndi chitsolo cha sefa yamkuŵa, mphiko zake ndi zipangizo zake zomwe, beseni losambira ndi phaka lake lomwe;
17nsalu zochinga bwalo, nsanamira pamodzi ndi masinde ake omwe, nsalu za pa chipata choloŵera ku bwalo,
18zikhomo zake pamodzi ndi zingwe za chihema cha Chauta ndi za bwalo lake;
19nsalu zokoma kwambiri zovala anthu otumikira m'malo opatulika, ndiponso zovala zopatulika za wansembe Aroni ndi za ana ake, akamatumikira ngati ansembe.”
Anthu abwera ndi zopereka20Tsono Aisraele onse aja adachoka ndi kumsiya Mose.
21Ndipo munthu aliyense, monga momwe mtima wake unkafunira, adabwera kwa Chauta ndi zopereka zopangira chihema chamsonkhano cha Chauta. Adabwera nazo zonse zogwiritsira ntchito potumikira, ndi zonse zopangira zovala zopatulika.
22Kudabwera amuna ndi akazi omwe. Munthu aliyense malinga ndi kufuna kwake adabwera ndi zokometsera zomangira zovala, nsapule zakukhutu, mphete, ukufu wam'khosi, ndi zokometsera zina zagolide. Munthu aliyense adabwera ndi zagolide zimene adazipatula kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.
23Munthu aliyense amene anali ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, bafuta wa thonje losalala kwambiri, nsalu za ubweya wambuzi, zikopa zankhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi zikopa zambuzi, adabwera nazo kwa Chauta. Aliyense adabwera ndi zimene anali nazo.
24Anthu onse amene anali ndi siliva kapena mkuŵa, zonsezo adabwera nazo kwa Chauta. Onse amene anali ndi matabwa a mtengo wa kasiya wogwiritsira ntchito pomangapo, adabwera nawo ndithu.
25Akazi onse aluso adaomba nsalu za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira. Adabweranso ndi bafuta wa thonje losalala kwambiri.
26Akazi onse alusowo adaombanso nsalu za ubweya wambuzi.
27Ndipo atsogoleri adabwera ndi miyala ya onikisi ndi miyala ina yoika pa chovala cha efodi ndiponso pa chovala chapachifuwa.
28Adaperekanso zonunkhira, mafuta anyale, mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma.
29Motero Aisraele onse, amuna ndi akazi omwe, amene adafuna ndi mtima wao wonse kupereka zao ku ntchito zimene Chauta adalamula kudzera mwa Mose, adabwera ndi zopereka zao kwa Chauta.
Antchito omanga chihema(Eks. 31.1-11)30Pambuyo pake Mose adauza Aisraele kuti, “Chauta wasankhula Bezalele, mwana wa Uri, mdzukulu wa Huri, wa fuko la Yuda.
31Chauta wadzaza Bezaleleyo ndi mzimu wa Mulungu, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndiponso ndi wodziŵa ntchito zonse zaluso.
32Amadziŵanso kulemba mapulani a ntchito zaluso ndi kugwira ntchito ndi golide, siliva ndi mkuŵa.
33Amadziŵa kusema miyala yakongoletsera, kujoba matabwa, ndi kuchita ntchito zonse zaluso.
34Tsono Chauta wapatsa nzeru kwa iyeyo ndi kwa Oholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, kuti aziphunzitsa ena luso laolo.
35Iwoŵa adapatsidwa luso lalikulu, kuti achite ntchito za mitundu yonse zimene amachita anthu ozokota, amisiri a ntchito zaluso, anthu oomba nsalu za bafuta wa thonje losalala kwambiri. Akudziŵadi kugwira ntchito zonse, ndipo angathenso kuganizira ntchito zonse zaluso.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.