1 Deut. 17.17 Mfumu Solomoni ankakonda akazi ambiri achilendo. Kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, adakwatiranso akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni ndi Ahiti.
2Eks. 34.16; Deut. 7.3, 4 Akazi ameneŵa anali a mitundu ija imene Chauta adaauza Aisraele kuti, “Musadzakwatire akazi a mitundu imeneyi, ndipo amuna amitunduyo asadzakwatire akazi a mtundu wanu, poti ndithudi iwowo adzatembenuza mitima yanu, kuti muzitsata milungu yao.” Koma Solomoni ankakondabe akazi a mitundu imeneyo.
3Iyeyo adakwatira ana achifumu 700 ndipo anali ndi azikazi 300. Ndipo akaziwo adamsokoneza.
4Solomoni atakalamba, akazi akewo adamnyengerera kuti azitsata milungu yachilendo. Choncho sadatsate Chauta, Mulungu wake, ndi mtima umodzi, monga ankachitira Davide bambo wake.
5Solomoni ankapembedza Asitoreti, mulungu wachikazi wa Asidoni, ndiponso Milikomu, mulungu wonyansa uja wa Aamoni.
6Motero Solomoni adachimwira Chauta, ndipo sadatsate Chauta ndi mtima wonse, monga ankachitira Davide, bambo wake.
7Tsono Solomoni adamanga akachisi pa phiri la kuvuma kwa Yerusalemu, kumangira Kemosi, mulungu wonyansa wa Amowabu, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni.
8Akazi ake onse achilendo adaŵamangira malo ofukizirapo lubani ndi operekerapo nsembe kwa milungu yao.
9Choncho Chauta adakwiyira Solomoni, chifukwa choti mtima wake udaasinthika ndi kusiya Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene adamuwonekera kaŵiri konse,
10namulamula kuti asatsate milungu ina. Koma Solomoni sadamvere zimene Chauta adamlamulazo.
11Nchifukwa chake Chauta adamuuza kuti, “Popeza kuti sudasunge chipangano changa ndi malamulo anga amene ndidakulamula, ndithudi ndidzakulanda ufumu, kuuchotsa m'manja mwako, ndi kuupereka kwa mmodzi mwa atumiki ako.
12Koma chifukwa cha Davide bambo wako, sindidzachita zimenezi iwe uli moyo ai. Ndidzaulanda kwa mwana wako.
13Komabe sindidzalanda ufumu wonse. Mwana wako ndidzamsiyirako fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu umene ndidausankha.”
Adani a Solomoni14Tsono Chauta adamuutsira Solomoni mdani dzina lake Hadadi, wa ku Edomu. Hadadiyo anali wa banja laufumu ku Edomuko.
15Kale ndithu pamene Davide ankamenyana nkhondo ndi Aedomu, Yowabu mkulu wankhondo adaapita kukakwirira Aisraele ophedwa, ndipo adakapha mwamuna aliyense ku Edomuko.
16Yowabu ndi ankhondo ake adaakhala kumeneko miyezi isanu ndi umodzi, mpaka adapha amuna onse a ku Edomu.
17Koma Hadadi adaathaŵira ku Ejipito pamodzi ndi Aedomu ena, atumiki a bambo wake. Pamenepo nkuti Hadadiyo ali mwana wamng'ono.
18Adanyamuka ku Midiyani, napita ku Parani, ndipo adatengako amuna ena ku Paraniko, nakafika ku Ejipito kwa mfumu Farao. Farao adapatsa Hadadi ndi anthu ake nyumba ndi chakudya, namninkhanso kadziko.
19Tsono Farao adakomera mtima Hadadi, kotero kuti adampatsa mlamu wake kuti akhale mkazi wake. Mkaziyo anali mbale wake wa mfumukazi Tapenesi wa ku Ejipito.
20Tsono mkazi wa Hadadiyo adabala mwana wamwamuna dzina lake Genubati, ndipo Tapenesi adalerera Genubati ku nyumba yaufumu. Genubatiyo ankakhala m'nyumba ya Farao pamodzi ndi ana a Farao.
21Koma Hadadi atamva ku Ejipitoko kuti Davide adamwalira, ndiponso kuti Yowabu mtsogoleri wankhondo nayenso adafa, adauza Farao kuti, “Loleni ndichoke kuti ndipite ku dziko lakwathu.”
22Koma Farao adati, “Chakusoŵa nchiyani kwathu kuno kuti uziti ukufuna kupita ku dziko lakwanu?” Hadadi adauza Farao kuti, “Iyai sizimenezo, mungondilola basi kuti ndizipita.”
23Mulungu adautsiranso Solomoni mdani wina, dzina lake Rezoni, mwana wa Eliyada, amene anali atathaŵa kwa mbuyake Hadadezere, mfumu ya ku Zoba.
24Munthu ameneyu adasonkhanitsa anthu, nakhala mtsogoleri wao wa gulu la achifwamba. Izi zidachitika pamene Davide adati atagonjetsa Hadadezere, adapha ankhondo a ku Zoba. Tsono Rezoni ndi gulu lake adapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko, ndipo anthuwo adamlonga ufumu womalamulira dziko la Siriya.
25Rezoni anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, namamvuta Solomoniyo monga momwe Hadadi ankachitira.
Lonjezo la Mulungu kwa Yerobowamu26Winanso woukira Solomoni anali Yerobowamu, mwana wa Nebati wa fuko la Efuremu, wa ku Zereda. Anali mmodzi mwa nduna za Solomoni, amene mai wake anali Zeruya, mkazi wamasiye.
27Nkhani ya kuukira kwakeyo idaayenda motere: Solomoni adaamanga linga la Milo, nakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide bambo wake.
28Yerobowamu anali munthu wolimba mtima, ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo ngwachangu, adamuika kuti akhale kapitao woyang'anira ntchito yathangata m'dziko la ana a Yosefe.
29Ndiye tsiku lina pamene Yerobowamu anali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, mneneri Ahiya wa ku Silo adampeza pa mseu. Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano, ndipo aŵiriwo anali okha kuthengoko.
30Tsono Ahiya adagwira mwinjiro watsopano adaavalawo, nkuung'amba m'zidutswa khumi ndi ziŵiri.
31Ndipo adauza Yerobowamu kuti, “Iwe utengeko zidutswa khumi. Pakuti Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ndithudi, Ine ndikuchotsa ufumu m'manja mwa Solomoni, ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko khumi.
32Solomoni ndidzamsiyira fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Aisraele.
33Ndidzachita zimenezi chifukwa Solomoniyo wandisiya Ine, wayamba kupembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa Aamoni. Choncho sadandimvere, sadachite zimene ine ndifuna, ndipo sadasunge malamulo anga ndi malangizo anga, monga momwe ankachitira Davide, bambo wake.
34Komabe sindidzamlanda ufumu iyeyo. Adzakhalabe wolamulira masiku onse a moyo wake, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene ndidamsankha, amene ankasunga malamulo anga.
35Tsono ufumuwo ndidzauchotsera m'manja mwa mwana wake, ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko khumi.
36Komabe mwana wake ndidzamsiyira fuko limodzi kuti pakhalebe Davide mtumiki wanga azidzakhala ndi nyale nthaŵi zonse pamaso panga ku Yerusalemu, mzinda umene ndausankha kuti azindipembedza kumeneko.
37Ndidzatenga iweyo Yerobowamu, udzalamulira paliponse pamene mtima wako ufuna, ndipo udzakhala mfumu ya Israele.
38Ukamamvera zonse zimene ndikukulamula, ndi kumayenda m'njira zanga, ndi kumachita zimene Ine ndifuna, posunga malamulo anga monga m'mene ankachitira Davide, mtumiki wanga, ndiye kuti Ine ndidzakhala nawe. Ndipo zidzukulu zako zidzalamulira monga m'mene ndidalonjezera Davide. Chigawo cha Israele ndidzachipereka kwa iwe.
39Chifukwa cha kuchimwa kwa Solomoniku, ndidzazunza zidzukulu za Davide, koma osati nthaŵi zonse ai.’ ”
40Nchifukwa chake Solomoni ankafunitsitsa kupha Yerobowamu. Koma Yerobowamu adachoka nathaŵira ku Ejipito, kwa Sisake mfumu yakumeneko. Adakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira.
Kumwalira kwa Solomoni(2 Mbi. 9.29-31)41Tsono ntchito zina za Solomoni, ndi zonse zimene adachita, ndiponso nzeru zake, zidalembedwa m'buku la Ntchito za Solomoni.
42Iye adalamulira Aisraele ku Yerusalemu zaka makumi anai.
43Tsono Solomoni adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide, bambo wake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.