Yes. 50 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Bar. 4.6 Chauta akuti,

“Ili kuti kalata yake imene ndidasudzulira mai wanu?

Mwa anthu amene ndili nawo ndi ngongole,

ndidakugulitsani kwa uti?

Iyai, inutu mudagulitsidwa ku ukapolo

chifukwa cha machimo anu,

ndipo mai wanu adachotsedwa

chifukwa cha upandu wanu.

2Chifukwa chiyani panalibe anthu,

pamene ndidabwera kudzaŵapulumutsa?

Chifukwa chiyani panalibe wondiyankha,

pamene ndidaitana?

Kodi dzanja langa nloti nkulephera kuwombola?

Kodi kapena ndilibe mphamvu zopulumutsira?

Nditangodzudzula chabe, nyanja yaikulu itha kuuma,

ndipo mitsinje itha kusanduka chipululu.

Chifukwa chosoŵa madzi

nsomba zam'menemo nkuyamba kununkha,

ndiponso kufa ndi ludzu.

3Nditha kuphimba thambo ndi mdima,

ndi kulisandutsa ngati likulira maliro.”

Kumvera kwa mtumiki wa Chauta

4Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena,

kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka.

M'maŵa mulimonse amandidzutsa,

amathwetsa makutu anga kuti ndimve,

monga amachitira amene akuphunzira.

5Ambuye Chauta anditsekula makutu,

ndipo sindidaŵanyoze kapena kuŵapandukira.

6 Mt. 26.67; Mk. 14.65 Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya,

ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu.

Sindidaŵabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu.

7Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako,

chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza.

Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala.

Ndikudziŵa kuti sadzandichititsa manyazi.

8 Aro. 8.33, 34 Wondikhalira kumbuyo ali pafupi,

ndaninso angandiimbe mlandu?

Tipitire limodzi ku bwalo lamilandu.

Wofuna kutsutsana nane ndani?

Nabwere pafupi.

9Ambuye Chauta ndi amene amandithandiza,

ndani anganene kuti ndine wopalamula?

Ndithu, onse ondizenga mlandu adzatheratu.

Kutha kwake ngati chovala chodyewa ndi njenjete.

10Ndani mwa inu amaopa Chauta,

ndi kumvera mau a mtumiki wake?

Aliyense woyenda mu mdima, wopanda chomuunikira,

akhulupirire dzina la Chauta,

ndipo adalire Mulungu wake.

11Nonsenu amene mumasonkha moto

ndi kuyatsa zikuni kuti muwononge anzanu,

loŵani inuyo m'moto wanu womwewo,

yendani pakati pa zikuni zimene mudayatsazo.

Mudzakhala m'mazunzo,

ndipo ndi Ineyo Chauta amene ndidzagwetsa mazunzowo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help