1Ngwodala aliyense woopa Chauta,
amene amayenda m'njira zake.
2Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito.
Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
3Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka,
m'kati mwa nyuma yako.
Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi,
kuzungulira tebulo lako.
4Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala
munthu woopa Chauta.
5Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse.
Uwone m'mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendere bwino
masiku onse a moyo wako.
6Ukhale ndi moyo wautali
kuti uwone zidzukulu zako.
Mtendere ukhale ndi Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.