1Inu Mulungu, pulumutseni ndi dzina lanu,
onetsani ndi mphamvu zanu kuti ndine wosalakwa.
2Inu Mulungu, imvani pemphero langa,
tcherani khutu kuti mumve mau a pakamwa panga.
3Anthu onyada andiwukira,
anthu ankhalwe amafunafuna moyo wanga,
iwo saganizako za Inu Mulungu.
4Komatu, Mulungu ndiye amandithandiza,
Ambuye ndiwo amachirikiza moyo wanga.
5Adzaŵabwezera adani anga zoipa.
Aonongeni, Inu Ambuye,
chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
6Ndidzapereka nsembe kwa Inu mwaufulu.
Ndidzatamanda dzina lanu, Inu Chauta,
popeza kuti ndinu abwino.
7Mwandipulumutsa m'mavuto anga onse,
ndakondwa poona adani anga atagonja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.