Ezek. 41 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Pambuyo pake munthu uja adapita nane m'chipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu, nayesa mphuthu zake. Muufupi mwake munali mamita atatu mbali iliyonse.

2Muufupi mwake mwa khomo munali mamita asanu. Zipupa zake zam'mbali zinali za mamita aŵiri ndi theka muufupi mwake mbali iliyonse. Adayesa kutalika kwake kwa chipindacho, kunali mamita makumi aŵiri, muufupi mwake mamita khumi.

3Kenaka adakaloŵa m'kati nakayesa mphuthu zapakhomo. Zinali za mita limodzi, ndipo khomolo linali la mamita atatu. Zipupa za m'mbali mwa khomolo zinali za mamita atatu ndi theka mbali iliyonse.

4Pambuyo pake adayesa chipinda chenichenicho napeza kuti m'litali mwake ndi muufupi mwake munali mamita khumi. Apo adandiwuza kuti, “Chimenechi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”

Zipinda zina

5Tsono munthu uja adayesa khoma la Nyumba ya Mulungu, linali la mamita atatu. Panali zipinda zina kuzungulira Nyumbayo, chilichonse muufupi mwake chinali cha mamita aŵiri.

6Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana, chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulunguyo panali zochirikiza zipindazo, kuti zisamatsamire pa chipupa cha Nyumba ya Mulungu.

7Zipinda zam'mbalizo zinkapita zikukulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda, potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika chapamwamba.

8Tsono ndidaona chiwundo chozungulira Nyumba ya Mulungu. Chidapanga maziko a zipindazo, ndipo chinali cha mamita atatu.

9Khoma la kunja kwa zipindazo linali la mamita aŵiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho

10ndi zipinda za Nyumba ya Mulunguyo panali bwalo la mamita khumi m'kupingasa kwake, kuzungulira Nyumba yonseyo.

11Zipinda zam'mbalizo zinali zotsekulira ku mbali za chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayang'ana kumpoto, china chinkayang'ana kumwera. Kukula kwa chiwundo chosamangapo kanthu kunali mamita aŵiri ndi theka kuzungulira ponseponse.

Nyumba yakuzambwe

12Chakuzambwe, kuyang'anana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu, kunali nyumba inanso ya mamita 35 muufupi mwake. Khoma lake linali la mamita aŵiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, m'litali mwake linali la mamita 45.

Miyeso ya Nyumba ya Mulungu

13Tsono munthu uja adayesa Nyumba ya Mulungu, m'litali mwake inali ya mamita makumi asanu. Bwalo la Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu.

14Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakuvuma kwa bwalolo muufupi mwake munali mamita makumi asanu.

15Kenaka adayesa kutalika kwa nyumba yoyang'anana ndi bwalolo chakuzambwe kwa Nyumba ya Mulungu, ndi njira zam'kati ku mbali iliyonse. Zonsezo zinali za mamita makumi asanu.

Chipinda cha m'thunthu mwa Nyumba ya Mulungu, chipinda cham'kati ndiponso khonde lam'kati loyang'ana kunja,

16mazenera ndi made ake, zonsezo zinali zochingidwa ndi matabwa. Pamwamba, kupenyana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu idaakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, ndipo mazenerawo anali okutidwa.

17Pamwamba pa khomo loloŵera ku chipinda cham'kati,

18adaazokotapo zithunzi za akerubi ndi za kanjedza. Kerubi mmodzi adaakhala pakati pa kanjedza muŵiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziŵiri:

19ina inali nkhope ya munthu, yoyang'ana kanjedza wa mbali imodzi, ina inali nkhope ya mkango yoyang'ana kanjedza wa mbali ina. Zidachingidwa choncho kuzungulira Nyumba yonse.

20Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa zitseko panali zithunzi zozokota za akerubi ndi za kanjedza.

21Mphuthu za chipinda cham'thunthu kutalika kwake mbali zonse kunali kolingana. Kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu chooneka ngati

22guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali wa mita limodzi ndi hafu, m'litali mwake munali mita limodzi, muufupi mwake munalinso mita limodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi makoma ake, zonse zinali zopanga ndi mtengo. Munthu uja adandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limene limakhala pamaso pa Chauta.”

23Chipinda cham'thunthu chija chinali ndi zitseko ziŵiri, malo oyera analinso ndi zitseko ziŵiri.

24Pa chitseko chilichonse panali zigawo ziŵiri zopatukana.

25Pazitsekopo adazokotapo zithunzi za akerubi ndi za kanjedza, monga pa makoma aja. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lam'kati.

26Pa mbali zonse za khonde lam'katilo panali mazenera, ndipo pa zipupa zake zonse adazokotapo zithunzi za kanjedza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help