Zek. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yerusalemu ndi mzinda wopembedzerako anthu onseMau olosa

1Mau a Chauta onena za Israele. Chauta ndiye adayala mlengalenga ndi kukhazikitsa dziko lapansi, ndiyenso amene adalenga mpweya wokhala mwa munthu. Iye akunena kuti,

2“Ndidzasandutsa Yerusalemu kuti akhale ngati chikho cha vinyo amene adzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomzungulira. Adani omwewo adzathira nkhondo dziko la Yuda ndiponso mzinda wa Yerusalemu.

3Tsiku limenelo Yerusalemu ndidzamsandutsa mwala wolemera kwambiri kwa mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kuunyamula, udzaŵapweteka koopsa. Mitundu yonse ya anthu a pansi pano idzasonkhana pamodzi kuti imuukire Yerusalemu.”

4Chauta akunena kuti, “Tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamchititsa mantha osokonezeka nawo, ndipo wokwerapo wake adzachita msala. Banja la Yuda ndidzaliyang'anira, koma akavalo a adani ao onse ndidzaŵachititsa khungu.

5Pamenepo atsogoleri a Yuda adzavomera kuti, ‘Indedi, anthu a ku Yerusalemu amapeza mphamvu mwa Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wao.’ ”

6Tsiku limenelo mafuko a ku Yuda ndidzaŵasandutsa ngati mbaula yotentha pakati pa nkhuni, ngati nsakali yoyaka pakati pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yoŵazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma anthu a ku Yerusalemu adzakhalabe mwamtendere mumzinda mwao.

7“Chauta adzayamba wapulumutsa mahema onse a ku Yuda, kuti ulemerero wonse wa banja la Davide ndi wa anthu a ku Yerusalemu usapambane ulemerero wa Yuda.

8Tsiku limenelo Chauta adzakhala ngati chishango chotchinjiriza anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti anthu ofooka kwambiri mwa iwo adzakhala amphamvu ngati mfumu Davide. Tsono banja la Davide lidzakhala lolamulira zonse ngati Mulungu, ngati mngelo wa Chauta woŵatsogolera.

9Tsiku limenelo ndidzaononga mitundu yonse ya anthu yofuna kuthira nkhondo Yerusalemu.

10 Yoh. 19.37; Chiv. 1.7 Mt. 24.20; Chiv. 1.7 “Tsono anthu a pa banja la Davide ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndidzaŵadzaza ndi mtima wachifundo ndi wakupemphera. Motero adzati atamuyang'ana amene adambaya, adzamlira kwabasi monga muja amamlirira mwana akakhala mmodzi yekha. Adzamliradi kwambiri monga muja amamlirira mwana wachisambamu.

11Tsiku limenelo kulira maliro ku Yerusalemu kudzakula monga m'mene kunaliri polira Hadadirimoni m'chigwa cha ku Megido.

12Dziko lidzalira, banja lililonse palokha. Banja la Davide lidzalira palokha, akazi akenso adzalira paokha. Banja la Natani lidzalira palokha, akazi akenso adzalira paokha.

13Banja la Levi lidzalira palokha, akazi akenso adzalira paokha. Banja la Simei lidzalira palokha, akazi akenso adzalira paokha.

14Mabanja onse otsala adzalira paokha, ndipo akazi aonso adzalira paokha.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help