1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, kodi ukufuna kudzaweruza Yerusalemu? Kudzaweruza mzinda wodzaza ndi anthu opha anzaoŵa? Tsono uudzudzule chifukwa cha machitidwe ake onse onyansa.
3Unene kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Wadziitanira tsoka iwe mzinda umene umakhetsa magazi a anthu ake ambiri. Ndiwe mzinda umene umadziipitsa ndi mafano amene udadzipangira!
4Wapalamula chifukwa cha kukhetsa magazi. Wadziipitsa chifukwa cha mafano amene udapanga. Motero wachepetsa masiku ako, ndipo zaka za moyo wako zatha. Nchifukwa chake ndalola kuti mitundu ya anthu ikunyoze, ndipo kuti maiko onse akuseke.
5Maiko apafupi ndi akutali omwe adzakunyodola, iwe wa mbiri yoipawe ndi wokonda zandeu.
6“Taona m'mene akuluakulu onse okhala mwa iwe amaphera anthu anzao, aliyense potsata mphamvu zake.
7Eks. 20.12; Deut. 5.16; Eks. 22.21, 22; Deut. 24.17 Anthu ako akhala akunyoza atate ao ndi amai ao. Akhala akuzunza alendo okhala nawe, akhalanso akusautsa ana amasiye ndi akazi amasiye.
8Lev. 19.30; 26.2 Wanyoza zinthu zanga zopatulika, ndipo waipitsa masiku anga a Sabata.
9Mwa iwe muli ena ochita ugogodi kuti aphe anzao. Mulinso ena odyera zansembe pa zitunda zachipembedzo. Muli anthu enanso ochita zonyansa.
10Lev. 18.7-20 Mwa iwe muli ena ogona ndi akazi a atate ao, ndi enanso ovutitsa akazi pa nthaŵi yao yosamba.
11Ena amachita chigololo ndi akazi a anzao, ena amachita zoipa ndi apongozi ao. Enanso amaipitsa alongo ao, ana a atate ao.
12Eks. 23.8; Deut. 16.19; Eks. 22.25; Lev. 25.36, 37; Deut. 23.19 Mwa iwe muli ena olandira ziphuphu kuti aphe anzao. Ena amalandira chiwongoladzanja ndi kupezapo phindu pa zimene amakongoza, ena amaopsa anzao kuti apeze phindu. Onsewo andiiŵala Ine. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
13“Nchifukwa chake Ine ndichita kuti m'manja bu nkudabwa kwambiri chifukwa cha phindu lako lopeza monyenga, ndiponso chifukwa cha kuphana kumene kumachitika m'kati mwa malinga ako.
14Kodi mtima wako udzakhala wolimbabe ndiponso manja ako adzakhalabe amphamvu, ndikadzatsiriza kukulanga? Ine Chauta ndatero, ndipo ndidzazichitadi.
15Ndidzabalalitsa anthu ako pakati pa mitundu ina ya anthu ndi kuŵamwazira ku maiko akutali. Ndimo m'mene ndidzakuchotsere kuipa kwako.
16Ndidzakunyozetsa pamaso pa mitundu ya anthuyo. Motero udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Ng'anjo ya Mulungu yoyeretsera17Tsono Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
18“Iwe mwana wa munthu, Aisraele onse asanduka achabechabe m'maso mwanga. Akulingana ndi mkuŵa, chitini, chitsulo ndi mtovu, zimene zatsala m'ng'anjo atayeretsa siliva.
19Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Popeza kuti nonsenu mwasanduka ngati zotsala zachabe, ndidzakusonkhanitsani ku Yerusalemu.
20Monga muja anthu amasonkhanitsira siliva, mkuŵa, chitsulo, mtovu ndiponso chitini m'ng'anjo, nasonkheza moto kuti uzisungunule, ndimo m'menenso Ine ndidzakusonkhanitsireni ndili wokwiya ndi waukali. Ndidzakuikani m'kati mwa mzinda ndipo ndidzakusungunulirani m'menemo ngati m'ng'anjo.
21Ndidzakusonkhanitsani mumzindamo ndi kukoleza moto wa mkwiyo wanga, mpaka mutasungunuka.
22Mudzasungunukadi monga momwe siliva amasungunukira m'ng'anjo. Motero mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndakukwiyirani.”
Machimo a atsogoleri a ku Israele23Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,
24“Iwe mwana wa munthu, uza Yerusalemu kuti iye uja ndi dziko losayeretsedwa, ndiponso losavumbidwa ndi mvula chifukwa cha mkwiyo wanga.
25Atsogoleri ake ali ngati mikango yobangula pogwira nyama. Apha anthu, alanda chuma ndi zinthu za mtengo wapatali. Akazi ambiri aŵasandutsa amasiye mumzindamu.
26Lev. 10.10 Ansembe ake omwe aphwanya malamulo anga, ndipo aipitsa zinthu zanga zopatulika. Sasiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba. Sadaphunzitse anthu kusiyana kwake pakati pa zoyenera pa chipembedzo ndi zosayenera. Sasamala masiku anga a Sabata, motero anthu sandilemekeza.
27Atsogoleri ake ali ngati mimbulu yokadzula nyama. Amakhetsa magazi ndi kuwononga moyo wa anthu, kuti apate phindu loipa.
28Ndipo aneneri ake abisa zimenezi monga muja amachitira anthu popaka njereza, amaziphimba ndi zimene amaona m'maloto ao abodza ndi m'maula ao onama. Amati, ‘Ambuye Chauta akunena zakutizakuti,’ pamene Ine Chauta sindidalankhule konse.
29Anthu am'dzikomo amasautsa anzao ndiponso amaba. Amazunza osoŵa ndi osauka. Amavutitsa alendo posaŵachitira zinthu mwachilungamo.
30Ndidafunafuna munthu pakati pao woti amange linga, woti pamaso panga aime pamene padagumuka, kuti ateteze dziko ndi kundipepesa kuti ndisaliwononge. Koma munthu woteroyo sindidampeze.
31Nchifukwa chake ndidaŵakwiyira kwambiri. Ndidzaŵaononga kotheratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Motero ndidzaŵalanga monga kuŵayenera.” Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.