1 Yer. 1.5 Mverani inu anthu a ku maiko
a m'mphepete mwa nyanja,
tcherani khutu, inu anthu akutali.
Chauta adandiitana ndisanabadwe,
adanditchula dzina ndidakali m'mimba mwa amai anga.
2 Ahe. 4.12; Chiv. 1.16 Adasandutsa pakamwa panga
kuti pakhale ngati lupanga lakuthwa.
Adanditchinjiriza ndi dzanja lake.
Adandisula ngati muvi wakuthwa, nandibisa m'phodo mwake.
3Adandiwuza kuti,
“Iwe Israele ndiwe mtumiki wanga.
Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
4Koma ndidati, “Ndagwira ntchito yopanda phindu.
Ndangoononga mphamvu zanga pachabe.”
Komabe zondiyenerera zili m'manja mwa Chauta,
mphotho yanga ili m'manja mwa Mulungu wanga.
5Chauta ndi amene adandiwumba
m'mimba mwa amai anga kuti ndikhale mtumiki wake,
kuti ndibweze fuko la Yakobe kwa Iye,
ndipo kuti ndisonkhanitse Aisraele pafupi ndi Iye.
Choncho ndimalemekezeka m'maso mwa Chauta,
ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
6 Yes. 42.6; Lk. 2.32; Ntc. 26.23; Ntc. 13.47 Chautayo akunena kuti,
“Nchinthu chochepa kwambiri kuti ukhale mtumiki wanga,
kuti udzutse mafuko a Yakobe
ndi kuŵabweza kwao Aisraele amene adapulumuka.
Ndidzakusandutsa kuŵala kounikira mitundu ina ya anthu,
kuti chipulumutso changa chikafike
mpaka ku mathero a dziko lapansi.”
7Chauta, Mpulumutsi ndi Woyera uja wa Israele,
akulankhula ndi wonyozedwa kwambiri uja,
wodedwa ndi mitundu ina ya anthu,
kapolo wa mafumu ankhanza.
Akunena kuti,
“Mafumu adzaimirira mwaulemu poona iwe,
akalonga nawonso adzadziponya pansi chafufumimba.
Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Chauta,
amene ali wokhulupirika, Woyera uja wa Israele,
amene adakusankhula.”
Akonzanso Yerusalemu8 2Ako. 6.2 Chauta akunena kuti,
“Nthaŵi imene ndidakukomera mtima, ndidakuyankha,
ndipo tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza.
Ndidakusunga ndipo ndidakusandutsa
kuti ukhale chipangano kwa anthu,
kuti ndilibwezere dziko mwakale
ndi kuligaŵagaŵa dziko loonongekali.
9Ndidzauza am'ndende kuti atuluke,
ndi amene ali mu mdima kuti aonekere poyera.
Adzapeza chakudya m'mphepete mwa njira,
adzapeza busa pa magomo.
10 Chiv. 7.16, 17 Sadzamva njala kapena ludzu.
Mphepo yotentha kapena dzuŵa sizidzaŵapsereza,
chifukwa amene amaŵachitira chifundo
adzaŵatsogolera ndi kuŵaperekeza ku akasupe a madzi.
11Mapiri anga onse ndidzaŵasandutsa njira yoyendamo,
ndipo miseu yanga yaikulu ndidzaikonza.
12Onani, anthu anga adzachokera kutali,
ena kumpoto, ena kuzambwe,
enanso adzachokera ku Asuwani kumwera.”
13Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga!
Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi!
Yambani nyimbo, inu mapiri!
Chauta watonthoza mtima anthu ake,
ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.
14Koma anthu a ku Ziyoni adati,
“Chauta watisiya ife,
Ambuye atiiŵala.”
15Apo Chauta adafunsa kuti,
“Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere,
osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe?
Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake,
Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
16Iwe Yerusalemu, ndidadinda
chithunzi chako pa zikhatho zanga,
zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
17Amisiri odzakumanganso akubwera mofulumira,
ndipo okupasula ndi okuwononga akuchokapo.
18Uyang'ane pozungulira,
uwone zimene zikuchitika.
Anthu ako onse akusonkhana,
akubwera kwa iwe.
Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo,
anthu ako adzakhala chinthu chokukongoletsa.
Udzaŵaonetsera monga amachitira mkwati wamkazi.
19Ndithudi, iwe amene wasanduka bwinja,
amene udaasiyidwa ndi kusakazika,
tsopano udzaŵachepera anthu odzakhala mwa iwe.
Ndipo amene adakuwononga aja
adzaŵapirikitsira kutali ndi iwe.
20Ana ako obadwa pa nthaŵi yako yachisoni
adzakuneneranso m'khutu mwako kuti,
‘Dziko likutichepera,
utikulitsire malo oti tizikhalapo.’
21Tsono iwe udzadzifunsa kuti,
‘Kodi ndani adandiberekera ana aŵa?
Ana anga onse adamwalira
ndipo sindidanthenso kukhala ndi ana ena.
Ndidaali ku ukapolo, ndidaaiŵalika.
Nanga ndani adaŵalera ana ameneŵa?
Ndidaatsala ndekha.
Nanga ana ameneŵa adachokera kuti?’ ”
22 Bar. 5.6 Ambuye Chauta akunena kuti,
“Ndidzakodola anthu a mitundu ina.
Ndidzaŵakwezera mbendera kuti adzabwere.
Tsono adzabwera nawo ana ako aamuna
ataŵatengera m'manja,
ndiponso ana ako aakazi,
ataŵasenzera pa mapewa.
23Mafumu adzakhala ngati atate okulerani,
akazi a mafumuwo adzakhala ngati amai okuyamwitsani.
Adzagwetsa nkhope zao pansi ndi kukuŵeramirani.
Adzaseteka fumbi la m'mapazi mwanu modzichepetsa.
Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta,
ndipo amene amakhulupirira Ine sadzachita manyazi.”
24Kodi mungathe kuŵalanda ankhondo zofunkha zao?
Kodi mungathe kuŵapulumutsa akaidi kwa mfumu yankhalwe?
25Chauta akuyankha kuti,
“Ndithudi, ankhondo adzaŵalanda akaidi ao,
ndipo mfumu yankhalwe adzailanda zofunkha zake.
Ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu,
ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
26Ndidzaumiriza okuzunzani kuti
adzadye mnofu wao womwe.
Ndipo adzaledzera nawo magazi ao omwe,
monga momwe adakachitira ndi vinyo watsopano.
Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta,
Mpulumutsi wanu, ndine Momboli wanu,
Wamphamvu uja wa Yakobe.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.